07/07/2025
Apolisi ku Mwanza ati akusunga mwana yemwe dzina lake ndi Letisha Kampeni amene akuganiziridwa kuti watayidwa ndi mayi ake.
Malinga ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Mwanza, a Hope Kasakula, mwanayu akungokwanitsa kufotokoza kuti amachokera m'mudzi mwa Mkando m'boma la Mulanje ndipo ali standard 4 ngakhale akulephela kunena komwe mayi ake apita.
A Kasakula apempha akubanja la mwanayu kuti akamutenge ndipo agwiritse ntchito nambala izi polumikizana ndi apolisi: 0999343828 kapena 0884112145
Wolemba: Catherine Alumando, Mwanza.