12/09/2024
Machinjiri - KABAZA
*Safety Awareness Campaign*
Ndife okhuzidwa ndi chiwelengero chochuluka cha ngozi zapa mseu, makamaka kwa amzathu anjinga zamoto omwe amaziziwika kuti a KABAZA kuno ku Machinjiri.
Kuno kwathu ku Machinjiri, Ngozi za njinga zamoto zachuluka kwambiri chifukwa;
1. Amayenda mosasamala pa mseu, monga kuthamanga kwambiri pa mseu
2. Kusowa upangiri wakayendedwe kapamseu ndi kuphwanya malamuro
3. Kuyenda pa mseu atamwa mowa
_Kungotchula zochepa chabe.
Bungwe lokhuzidwa la
*Active Youth Association*
Takonza Misonkhano yokacheza ndi Anyamata ndi azibambo omwe ameyendetsa njinga zamoto kapena kuti a KABAZA.
Cholinga Cha misonkhano yi ndi
*🦺Kukagawana nawo mauthenga osiyanasiyana okhuza kayendedwe kapamseu, mmene angazitetezere komanso kuteteza moyo wa anthu ena kudera lino ndikuchepetseratu ngozi zapa msewu kuno ku Machinjiri.*
Tizapelekanso uthenga wa zaumoyo, Ma Ufulu ndi udindo woteteza ana
komanso kuipa kogwilitsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo.
*Malo amene tiwafikire a KABAZA wa ndi awa:*
✓Luwanda
✓Nthawira
✓Area 5
✓Lizeyo-Area 12
*Masiku amisonkhano Yi ndi awa:*
9 October 2024
10 October 2024
11 October 2024
12 October 2024
Misonkhano yonseyi izizayamba
8:00 mmamawa
Ife abungwe la
*Active Youth Association*
Timakhulupilira kuti
💪mu umodzi muli mphamvu !
Tonse pamodzi TINGATHE !
Pogwilirana manja ndikuchepetseratu ngozi za pa msewu kudera lino ndikupanga Machinjiri wathu kukhala wokongola, wotetezeka ndi wa mtendere.
Tikukuitanani nonse anthu akufuna kwa bwino, inu amabungwe, azamolonda, ogwira ntchito za boma, achinyamata kuti tizakhale limodzi tsiku li
Ngati mukufuna kuziwa zambiri, mukufuna mupeleke chinthandizo pa msonkhano wu
*Tiyimbireni pa*
0 997 286 698
Muyankhurana ndi
*Michael Mataka*
Mneneli wa bungwe la
*Active Youth Association*
Komanso m***a kubwera ku Office yathu pa
*South Lunzu Health Centre*
⚠️TIYENI TONSE TIGWIRANE MANJA POCHEPETSA NGOZI ZA PAMSEU🦺