27/04/2025
UTHENGA WOCHOKERA KU STAY ALIVE INITIATIVE
Tikhala tikudziwitsani kuti abambo okwana 125 adzipha kuyambira January mpaka March chaka chino. Chiwerengerochi ndichokwera poyerekeza ndi abambo 109 omwe adzipha pa nthawi yomweyi chaka chatha.
Malinga ndi zomwe wachiwiri kwa M'neneri wa Apolisi, a Harry Namwaza, adafotokozera, zinthu monga ngongole, mavuto a mโbanja komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo ndi zomwe zikuchititsa anthu ambiri kudzipha.
Pakadali pano, anthu onse omwe adzipha chaka chino ndi 153 โ abambo 125 ndi amayi 28.
Tikupempha abambo onse komanso aliyense amene akukumana ndi mavuto kuti asamadziphimbe ndi nkhawa. Funsani thandizo! Limbikitsani kutuluka poyankhula ndi anzanu kapena kupita kwa maofesi a Apolisi omwe ali pafupi nanu kuti mupeze chithandizo choyenera.
Moyo ndi wofunika โ tiyeni tikhale ndi moyo!
Stay Alive Initiative โ Kukuthandizani Kukhalabe ndi Moyo.