26/04/2026
NKHANI ILI MOTERE:
•Pa 13 April 2026, bungwe la Football Association of Malawi linatulutsa ndandanda wa mabwalo 14 omwe anavomerezedwa kuchititsa masewero a ligi yaikulu.
Iwo anafotokozanso kuti mabwalo a Kamuzu, Nankhaka ndi Mzuzu sanafikire mulingo woyenerera ndipo akuyenera kukonzedwa. Izi ndi malingana ndi mphamvu zomwe FAM inapatsidwa ndi FIFA poyendera mabwalowa.
•Pa 21 April 2026, Super League of Malawi inatulutsa ndandanda wa masewero amu sabata yoyamba kuti Mighty Wanderers ndi Karonga United adzakumana pa Kamuzu Stadium pomwepo angakhale inatsekedwa.
•Pa 22 April 2026, Atolankhani omwe atayankhulana ndi akuluakulu a FAM ananenabe kuti bwaloli silili loyenera kuchititsa masewerowa ndipo SULOM ikuyenera ipeze bwalo lina.
•Pa 22 April pomwepa, Praise Mike Majawa wa MBC adalemba nkhani yomwe inafotokoza kuti mlembi wamkulu wa SULOM, A Williams Banda, anena kuti masewero otsegulira ligi achitikabe pa bwalo la Kamuzu.
A Banda anati akonza zomwe zimasowekera pa bwaloli komanso kuti ndi wokonzeka kulandira chilango chilichonse chomwe FAM ipereke. (https://www.facebook.com/100081330802581/posts/1023968973657453/?app=fbl)
•Pa 23 April, SULOM inapempha FAM kukayendera bwalo la Kamuzu koma FAM inati pa malamulo a FIFA, siwololedwa kukayendera bwalo kutatsala maola 48 kuti masewero achitike ndipo SULOM ipezebe bwalo lina. Koma SULOM inati masewero titchayabe pomwepo. (https://www.facebook.com/reel/3670049153134919/?app=fbl)
•Pa 24 April 2026, kunabwera lipoti yakuti SULOM ndi FAM amvana. Ankati a Brigadier Gilbert Mittawa analankhulana ndi a Fleetwood Haiya kuti masewerowa aseweredwa pa bwalo la Kamuzu. Anthu adakondwa kwambiri. Ukutu kudali ku mmawa. (https://www.facebook.com/100063943606691/posts/1460346822773424/?app=fbl)
•Madzulo apa 24 April 2026, FAM inatulutsa kalata kufotokoza kuti bwalo la Kamuzu likadali lotseka ndipo masewero akachitikapo chilango chiyenda. Kalatayi angakhale a Haiya adaikanso ku tsamba lawo. (https://www.facebook.com/10009531563484