03/09/2018
KAPOLO WACHIYEMBEKEZO SEASON ONE
EPISODE 01.
Misonzi yachimwemwe, misonzi ya kukhaula,
ufulu wamu mtima kapena mtendere wamumtima
ndi zinthu zomwe mwamuna kapena mkadzi wina
aliyense amazikonzekera mwa iye yekha
pakusankha kwake. Kusankha pochita zinthu
kumabweletsa chisangalaro kapena ukapolo
wamuntima kutengera ndi momwe mwini munthu
wapangira chiganizo chako. Kupelewera
pamaganizidwe kapena kupanga chiganizo
ndikomwe kudaika anthu ena mmabvuto azaoneni
osakanikilana ndi chisangalaro chamagazi.
Kuphana, kupusisana mchikondi komanso pa
ndalama. Kugwilisidwa ntchito pankhani
yazandale komanso chinyengo cha ulamuliro.
Ukapolo mchikondi, ukapolo mu ulamuliro,
ukapolo wamumtima omwe udamumatilira
mnyamata wina chifukwa cha chikondi komanso
kupelewera mphabvu pama phunziro ake. Ukapolo
okhala ndi chiyembekedzo.
Kufunafuna wachikondi ndiko kumakhala chiyambi
cha kuvutika mmaganizidwe ngati ukuzitengelera.
Zimapindulitsa ku mapeto ngakhale zimakhala
zopanda chiyembekedzo kuti zikathera kuti?.
Chifukwa anthu ochuluka amapanga maubale
anseri posaganizira kuti mawa lingathe
kubalanji....
"Linda kodi umangoti undiyankha
mawa,undiyankha mawa uzandiuza liti
makamaka?. Chonde abale kumakhalako ndi
mtima wachikondi"
"Iii iwe Sanny ndikuti mawa. Uzandikiletso
ndikamachoka kumjigo nthawi ngati zomwe zino"
"Aaa koma ine ndatopa ndisaname, mwezi
panopa ukutha ukungondiuza kuti mawa
tikakumana tsiku lirilonse, bwanji
osangondimasula?"
"Mmm Sanny tionana mawa"..
Linda anachoka pomwe tinaima paja kundisiya
ndekha ndekha ndukukira ndi mtima. Chinari
chitsimo chake ndikakumana naye kumufunsa za
nkhani yanga yomwe ndidamusimbira kuti
ndidagwa naye mchikondi. Chibadwireni changa
sindinapangepo chibwenzi. Mkadzi aliyense amene
ndinkafunsila ankandikana. Bvuto sindimaliziwa
koma ndikangoti nthawi izakwana pozilimbitsa
mtima ndi umphawi wachikondi omwe ndidali
nawo mumtima. Ndinafunitsisa kwambiri Linda
atakhala wachikondi wanga koma samandiuza
amangoti mmawa.
Ndinapita kunyumba ndili ndi nkhawa chifukwa
tsiku limeneri ndimaona ngati andiyankha koma
ndinachoka opanda chimwemwe mumtima.
Ndimakhala ndi makolo anga ndipo
amkandikonda kwambiri.
Mmawa kutacha ndinatenga zobvala zanga
mkuchapa bwino lomwe. Chachiwiri chomwe
ndidachita patsikuli ndikupita kubafa kukasamba.
Ndinazipopera perefyumu kuti mwina Linda
akandioneko kusintha. Ndidabvala bwino zedi
moti ndimachita kuziona ndekhanso kuti
ndikamuimisa mutu Linda patsikuli poti anyamata
amaganizo opusa ochuluka amakhulupilira kuti
kubvala bwino ndikomwe kumakopa atsikana
mtima kuiwala kuti kubvala bwino ndikusamala
kwa thupi lako basi osati kukopa pankhani
yachikondi..
"Eee-ee Sanny lero ndiye wauphatu ulusi"..
"Oooh Ife ndichoncho alongo".. Ndidamuyankha
ndili ndi chimwemwe zedi. Uyu anali mlongo
wanga Susan amene adalu wankulu kwa ineyo
poti m'banja mwathu tidalimo awiri basi. Adali
okongola ndithu.
"Eee lero ndiye kuti Linda akandiuza ndithu ngati
mlongo wanga wandichemelera, lero mbambadi
ndibwera ndi nkhokwe yachimwemwe komwe
ndikupitaku". Ndidazilankhulira mumtima.
Ndinauyamba ulendo wopita kukagada Linda.
Ndinafika pamtengo pomwe ndimakonda kuima
ndipo ndinasamira mtengo ndikutulusa Blackberry
wanga wa China uja amakhala ndi tochi uja.
Ndinangokhala mphindi zochepa kenako
ndinamuona Linda akubwera atanyamula
zotungira madzi limodzi ndi mayi ake."Eee apa
ndiye yalakwa bwanji. Aaa komabe sindilora
ndimulankhula" Sizomwe ndimkayembekezera ayi
komabe ndidazilimbitsa mwachinyengo.Akudutsa
pomwe ndinaima paja ndinalephera mkupeleka ndi
moni omwe mpaka anadutsa .
"Shaaa ndimulankhulitsa akamabwera sindilora
ayi lero andiuza yankho amene uja".
Patangodutsa mphindu zochepa Mwamwayi
ndinamuona wanyamula chidebe amayi ake
kuwasiya pa mjigo pompaja akutungura zina.
"Ooh Mulungu wayankha ndithu.. Mhu mhu,
Linda! Linda! Linda! Kodi sukundinva?"
Sinandikhuza zedi poti kulankhula kwanga kudali
kungozitaitsa nthawi poti ngakhale kucheuka
mkomwe sadacheuke. Ndinaona kuti kungoima
sizithandiza kanthu koma kumsatira.."Kodi
mwayamba mwano aLinda?" Ndidamfunsa
nfikuyenda mbali yakumanja kwake ndikuzifira
ndekha momwe ndidabvalira.
"Iwe Sanny, ukuona kuti ndalemeredwa ine ndiye
umafuna ndiyime pamene paja ndizitani?,
Komanso ukuona kuti ndili ndi amayi anga moti
ulibe mantha?"
"Mmm pepa Linda, undikhululukire"
"Kodi ukufuna chani?"
Adafunsa mosonyeza kuti sadali okondwa nane
zomwe zimkandichosa chilimbikiso.
"Ndikufuna undiyankhe kaya"."Ndikuyankhe
chani?"
"Linda sukuziwa nkhani yomwe ndinakuuza?"
"Eya sindikuiziwa tanena".
Munthu ndinamuuza kuti ndikunfuna chibwenzi eti
kumandiuza kuti ndilankhulenso kawiri.
Zidandukhuza koma simdafowoke.
"Linda tsiku lomwe ndinakuona ku Sukulu kuja
ndinagwa nawe mchikondi"
"Sanny, kodi mutu wakowo umaganiza? Padutsa
matsiku angati chindiuzileni zopusa zimenezo?"
"Ambiri Linda, mwinanso mwezi ukutha"."Ndiye
sungazipatse yankho wekha kuti sindikufuna?"
Ndinakhumudwa kwambiri chifukwa uyu anali
mtsikana wa nambala 22 kundikana.
Ngakhale adandiswera mtima wanga kwa nthawi
imeneyi Sindinabwelere kuopa kuonetsa kufooka.
Ndinapitiliza kuonjezera mfundo zanga. 'Linda
ndine chitseko chopanda feremu, pokufusira iwe
ndinadziwa kuti ndiwe feremu lamoyo wanga"..
"Sanny! Chonde"
Adalankhula mwaukali koma ine sizinandipase
jenkha nfipo ndidavomera." Ineyo Linda!,
Ndilankhule"
"Bwelera pompano sinfikufuna kukuonanso"."Ndiyankhe koma chonde ndagwira mwendo
wako".
"Ndikuti ubwelere".
Ndinamugwira Linda mkono kusonyeza kuti
ndinafunitsisa atakhala wachikondi wanga..
"Iwe choka! Usandigwire"
Chidebe chonse chamadzi chinathera mthupi
mwanga mpaka ndipo simdakhulupilirw kuti izi
zikuchitikadi poti adali atandinyowetsa ndi mtima
omwe udagwa naye mchikondi...
"Munthu osanva ngati iwe sindinamuone ine,
ngakhale nditasowa chochita ndikapanidwe ndi
nkhono ngati iwe? Kuyamba kusamba chifukwa
cha une mjumazinva kuti mwafikapo pogwa
mchikondi ndiineyo?. Wavalabe masaviko ndi
makakeya ako uko uli ukakumanandiine
undiimitse mutu"."Linda ndi chani?"
"Nanga mtchetche iyi eti ikundifuna chibwenzi"..
"Ndiye mpaka kumutayira madzi?" Awatu adali
mayi ake tsono kufika pamalowa ali ndi chidebe
pamutu."Amama tsiku ndi tsiku ndikamapita ku
mjigo amandivutisa. Kusukulu kumene
amandisowetsa mtendere".
Ankaoneka ngati onvetsetsa koma zidandikhuza
zedi mayiwo zomwe adalankhula komanso minwe
adaonekera panthawi yochepa atangonva zomwe
adalankhula mwana wawo. "Iwe nyamata
uyang'ane opanga nawo zakozo, kungonva kuti
madzi ozimisira moto sanyasa ndiye uli uzimisire
pa mwana waine?"
Nthawi yomweyo ndinaona mayi ake aLinda
akuponya madzi ena koma sindinalore kuti
athereso pathupi laine. Ndinagula mateyala
kuliyatsa liwiro.
"Ndikazangonvaso kuti ukulimbana ndi mwana wa
ine ndizakugwetsamo ine". Mawu amenewa
anandiopsa kwambiri ndipo ndinalumbira kuti
sindizanvutitsanso Linda.
Ndinafika kunyumba ndili madzi okhaokha.
"Sanny ndi chiyani?"
"Eee Susan panga zako"..
"Hehehe koma uona pole Iwe.. Muli ndi minyama
inu ndithu" Adalankhula akuseka mwachipongwe
zedi.
"Ukapitiliza zakozo ndikuthira makofi"
Nditangotero Susan sanalankhuleso kanthu.
Ndinalowa nyumba ndikusintha zobvala
ndikusekula wailesi ya panasoniki yanga
kumanvetsera. "Mukusowa mkadzi, mukuvutika
ndi matenda monga likango, tchilichili, fundu,
mwanaduwe komanso mankhwala amuitano
wamalonda, nkhope yamwayi oti ukangokodola
mtsikana kumangomwetulira?, apezeni Doctor
Faduweki ku Mozambique mu dera la Bvularo,
kapena imbani panambala izi; 0888...... .
Ndinatenga foni yanga ndikuyamba kulowetsa
nambala ija mofulumira. Sindinafune kuchedwa
koma kuyimba kuti mwina Doctor Faduweki
akandichotse minyama yanga..
"Halo!"
"Mwarandiridwa kuno kwa dokotara faduweki
ndikuthandizeni bwanji?"
Mawu okhao akuluakulu mantha anandigwira.
"Aaa ine ndimafuna mankhwala aakadzi bwana
wanga".
""Ooh sibvuto limenero, tsekani maso anuwo
pompano mupezeka muli kuno ndipo lero ndi tsiku
lomwe mupeze mayankho abvuto lanu". Adatero
mkuluyo kulankhula mosimikiza ndithu...
Zimatheka ndipo zikuchitika anthu mkuyamba
kuyendayenda, kuzibvuta ndi mtima kufunafuna
mankhwala pofuna kuthesa vuto lawo losowa
achikondi zomwe zili zosemphana pankhani ya
chikondi...
Tiyeni tione kuti zidatha bwanji mu episode
yachiwiri ndi mnyamata ameneyi...
Like & comment