08/06/2024
WA MAU A MULUNGU PA MOYO WATHU πβοΈ
:23-24 ππΉβοΈ
π£οΈNdipo tsopano, cotsani milungu yacilendo iri pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli. Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ace.
πΉβοΈ Okondedwa azanga apaulendo mau awa akulankhura ndi Mulungu kudzera mwa Yoswa kulankhura ndi ana a lsrayeri zokhudza kuchotsa milungu yachilendo pakati pao, mau awa tikuwapeza pamene Yoswa akubweleza kucita pangano pakati anthu ndi Mulungu, ndipo tikumva ana a lsrayeri akulonjeza kusatumikira milungu ina koma Yehova yekha, ndipo Yoswa akuwacenjezaso kuti ngati mwabvomekeza kutero chotsani milungu yonse pakati panu ndi kusankha Yehova Mulungu yekha, tikuyenera kuchotsa tchimo pakati pathu π.
πΉβοΈ Okondedwa azanga apaulendo, Mulungu akulankhura ndi moyo wathu lero zakuchotsa milungu yachilendo pakati pathu, ngati tabvomera kuntumikira lye yekha tichotse tchimo pa moyo wathu ndikuika mtima wathu pa lye yekha, Mulungu atalankhura kudzera mwa Yoswa ana a lsrayeri anamvomera kuchotsa tchimo pakati pao, m'bale or m'longo mau awa lero ndi athu Mulungu akulankhura ndi moyo wathu, Yoswa akulankhura ndi moyo wathu zakuchotsa milungu yachilendo (tchimo ) pakati pathu tiyeni tibvomere monga lsrayeri pakulapa tchimo lathu lero, tiyeni tifewetse khosi mtima wathu pamene talankhulidwa talalikidwa taphuzitsidwa ndi kulapa tchimo lathu, tiyeni tikonze moyo wathu lero pakulapa tchimo, tiyeni tichotse milungu yachilendo pakati pathu kuti Mulungu atsekure njira zathu ndi kuika chipambano pa moyo wathu. Ambuye Akudalitseni ndi kulenga chatsopano mwa inu. β