
28/04/2025
*"EDEMA" kutupa, kudzadza madzi m'thupi*
Uku ndi kutupa kwa thupi koyambitsidwa chifukwa cha kuchuluka Kwa madzi m'thupi. Chiwalo chimodzi or thupi lonse limatha kutupa.
*Choyambitsa*
Izi zimayamba pamene misempha yaphulika ndipo ikutaya madzi kumalowa mu ziwalo zina zamuthupi ndipo pamene madziwo adzadza malowo amatupa. Izi zimagwira mtima, mapapu, ubongo, misempha ndipo zizindikiro zimasiyana molingana ndi mbali yomwe yagwidwayo.
*Zonsezi zimayambitsidwa ndi izi;👇🏽👇🏽*
1. Kuyima malo amodzi nthawi yaitali
2. kumwa mankhwala othana ndi BP komanso ululu nthawi yaitali
3. Kudya mchere ochuluka
4. kusowa kwa maprotein mmagazi
5. Nthenda ya mapapu, impsyo komanso chiwindi
6. Kukhala oyembekezera
7. Zotengera kobadwira
8. Diabetes/Sugar
9. Mavuto a mtima
10. Mavuto akapumidwe
11. Kufa kwa ziwalo
*Zizindikiro*
1. Kutupa kwa mapazi, mimba, miyendo
2. Kuthabwanyika kwamalo omwe atupa mpaka kulowa mkati osabwelelapo
3. Kukanika kuyenda bwinobwino
4. Kukanika kupuma
5. Kupweteka pa mtima
6. Kutopa
7. Kutsokomola magazi
8. kusaona bwinobwino
9. Tulo
10. Kuphwanya kwa mutu, khosi,
11. Nseru, kusanza
12. Kusokonekera kwa kakodzedwe
*Kuchiza kwake*
Kuthetsa vutoli kumayamba ndi kuthana ndi chomwe chikuyambitsa bvutolo kwenikweni.
1. Kumwa mankhwala ochotsa mchere komanso madzi muthupi
2. Osaima or kukhala malo amodzi nthawi yaitali
3. Kuchepetsa mchere muchakudya
4. Kukhala pa oxygen
5. Mankhwala ochepetsa kuthamanga kwa magazi
6. Operation yochotsa madziwo.