12/09/2022
KOMA PALIBE CHIDZATILEKANITSA😭
M'Mudzi winawake munali kukhala anthu ambiri, koma unali mudzi wa malamulo, ndipo anthu onse anali ogwirizana.
Ndiye amfumu a mmudzimo anali atalamula k*ti: "Sitifuna kumva ndi kuona k*ti wina wa mmudzi muno ndi mkristu, ndipo akadzayerekeza munthu wina k*tsatira chikristu adzalira kwambiri".
Ndipo iyi inali lamulo lamphamvu ndiponso loopsa, ndipo anthu onse amayenera kuitsatira lamuloli, ndipo tsiku lina munthu wina anapezedwa akupemphera mnyumba mwake, koma anthu ena anamnenera kwa olamulira ndipo anamugwira ndi kumupha, izi zinapereka mantha kwa anthu ena amene anali akristu.
Ndiye mkati mwa mudzi muja munali munthu wina amene ankalalikira Uthenga, ndipo analalikira Uthenga kwa anthu osiyanasiyana.
Ndipo banja linalake linatembenuka mtima, ndipo onse anali kumasonkhana kunyumba inayake Koma zinali zopatsa mantha kwambiri, chifukwa mfumu inali itakwiya kwambiri, ndipo tsiku lina anagwidwa mmodzi wa mgulu lija la akristu, ndipo anamumenya ndi kumupachika, ndipo anapachikanso chikwangwani cholembedwa k*ti: "Winanso Ayerekeze kupanga zosakhala bwino apachikidwenso".
Izi zinapereka chiopsezo kwa okhulupirira ena, ndipo ambiri anayamba k*taya mtima, ndipo ankadzifunsa k*ti: "Kodi ndi liti tidzapeze mtendere ife"?😭😭
Okhulupirira anadandaula kwambiri, Koma Mlaliki uja anawauza k*ti: "Mukudziwa, moyo wachikristu nd moyo wowawitsa kwambiri, koma tiyeni tiiwale zakumbuyo, koma tiganize zak*tsogolo, tiyeni tipirire koma tikhale chifupi ndi chiyembekezo chathu mwa Kristu Yesu, pak*ti ngati ine ndi inu Yesu adatikonda ndipo anatifera natitenga, Palibe angatichotse mmanja mwake, palibe amene angatisiyanitse ndi chikondi chake, Koma tilimbe pak*ti ngakhale masautso tikudutsawa sangatisiyanitse ndi chikondi cha Yesu Kristu"🙏.
Anthu aja atamva mauwa analimbika mtima kupirira mmayesero onse, ndipo anali okonzeka k*tonzedwa chifukwa Cha Yesu Kristu, Ndipo patsogolo pake anthu aja anadzionetsera poyera, ndipo anayamba kumabvomereza poyer