Ukaipa dziwa nyimbo

Ukaipa dziwa nyimbo Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Ukaipa dziwa nyimbo, Blantyre.

30/07/2021

```CHIKONDI CHIRIBE MASO
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Part 20
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Short Stories by "Aubrey That'sDhe Boss"
Story from the book of
"Amuna Amuna Anga"
๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ
๐Ÿ‘€
Kupitiriza mu 18 ๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡
Mu usiku umeneo Mkazi wabwana anapita kuntchito kwake pamene abwana anatengana ndi a Minister komanso Richmond ulendo waku special room kokapanga trace anyamata (James ndi Aubrey) ...
Mkazi wabwana atafika ku ntchito kwao kuja, anafikira kukumana ndi Hildah...
Hildah osanama adali munthu omangika kwambiri ndi wamantha, paja adamupatsa nthawi kuti akuyenera kumufufudza Cathy ndipo tsiku lisathe asanampeze.
Hildah analibe chochita chirichonse ndipo amachita kusowa poyambira pake kuti awuyang'ana kuyambira pati mzukwao mpaka tsiku lonse linadutsa kufikira usiku wake pamene a Bwana ake Janet amatulukira...

Janet: evening Hildah?

Hildah: evening boss!

Janet: I hope Cathy uja wapezeka???

Hildah; mmmm not really, madam...

Janet: (mokalipa๐Ÿ˜ ) Chifukwa chani??? Eeee?? Kodi sinakuwuze kuti masana onsewu umuyang'ane??? ๐Ÿ˜ฆ๐Ÿ˜ฆ Unangokhala kodi???? Hildah!? Ndiuze chulungamo,,,, Cathy alikuti?

Hildah: madam, ineo kutereko ndinamuyang'anatu masana onsewu koma zooopsa ndithu zomwe ndakumana nazo....

Janet: ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ Hildah???? Am i looking joking๐Ÿ˜ฆ๐Ÿ˜ฆ? Iwe Cathy ndati alikuti? Ukufuna undiuze kuti watulukamo muno? Eeeeeee? Ukufuna undiiyike m'mavuto iwe eti?

Hildah: ๐Ÿ˜ช๐Ÿ˜ช๐Ÿ˜ชsorry madam, Cathy sanatuluke... Nditapita kuchipinda komwe amagonako ndinamuona, ndipo anasanduka mzukwa moti mpaka ndinakomoka.... Izizi ndayamba kuziona dzulo mene anangosowa moti ulendo oyambaso ndinakomoka pamene ndinakumana nao mzukwa umeneu, ๐Ÿ˜ˆ๐Ÿ˜ˆ๐Ÿ˜ˆmpaka azironda kundikhuphiza kuyambira 6 o'clock m'mawa ndipo ndinkazizimuka chama 4 o'clock masana. azilonda ndi mboni anga madam....
Ineo nthawi yonseyi sindimakuwuzani zankhani yi kamba koti umboni weniweni ndimausowa komanso sindimazinvetsetsa zinthu zakezo. Koma lero ndanvetsetsano pamene ndinali kuchipinda kwake, anazabwera pa kona ngati apo akuchita kuopsa ๐Ÿ‘น๐Ÿ‘น๐Ÿ‘นndipo anandiuza kuti wadzukaso kwakufa ndipo athana ndi aliyense amene ali kuno. mzukwao unatsikimiza kuti uyambirira kupha inuo ndineo....

Eeeeeeee apa Janet osanama anachita mantha ndipo mavuvu amapanga aja anatheratu pompo anayamba kunjenjemera ngati wazizidwa... ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ
Pofuna kutsikimizadi ngati zomwe amakamba Hildah yo zinali zooonadi, anaitanitsa azilonda atatu panja nawafunsira mnyumba.

"kuti ndizoonadi Hildah anakomoka? "

Azilonda aja anavomereza za nkhani-yo
kuti ๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡
"mnyumba muno muli chinthu chinachake choopsa ngakhale kuti sitikuchidziwa madam."
Mukulakhula mwazilondawo anafotokozaso kuti ndizoonadi Hildah anakomoka pamene anaona zoopsazo zomwe sanathe kutifotokozera azilondaife kuti chinali chani chomwe anaonacho maningana ndi situation yomwe anali."

Atafotokoza izi azilondao, ndipamene ananyamuka kubwerera panja kuntchito yao.

Hildah: mwanva??? Madam ineo sindingapange chinthu osakudziwitsani, ...

Mkazi wabwana anagwidwa ndi mantha akuulu, anazingwa nasowa mtengo ogwira...

Janet; shaaaaaa!๐Ÿ™†๐Ÿ™†๐Ÿ™† Koma ndiye zativutatu apa, ndiye wati uyambirira kupha ifeo???

Hildah: eya madam unandifotokozera choncho ndithu, moti apopo umafuna uyambire ineo kundipha ndipo m'malo mwake unandisiya nkundiuza kuti wandisiya ndicholinga choti ndikudziwitseni kaye tonsefe tikhale tikudziwa tisanafe....

Eeeeee eeeeee๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€ chongotero Janet anauma pakamwatu ndipo amachita kusowa cholakhula uku akupuma mwa mantha..

M'mene amakambira izi, nkuti Memory akunva zonse, chipinda chomwe amakambirana izizi chinayandikana ndiku khitchini komwe amaphikirako zakudya Memory yo, ataona nkumanowo ndipamene anasiya zophikaphika zakezo ndikumakanvetsera pafupi..
Atanva izi Memory anachita kuluphalupha akunva kukoma kuti game apapa yiyenda bwino ndipo akhulupiriradi zoti Cathy panopa ndi mzukwa.
Anathamanga kuchipinda kwake, natsegula m'mwamba mwa sealing muja kumuwuza Cathy za situation m'mene iliri.
Apa anakambirana zokupsa anthu awiriwo naitana nzao m'modzi mwachinsinsi dzina lake Catalina.

Funso nkumati, Kodi ndichani zakupsa zomwe anakambirana mu utatu wawou, Cathy, Memory ndi Catalina???

Kupitiriza mu part 19,
๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡
Bwana: well done, I block-keni pompano....

Pompodi computer ina block, mpaka laptop ๐Ÿ’ป la Tinashe inazimira pompo kamodzindikamodzi kuti Thiii!!!

Zatheka bwana ndipo isiya kugwira ntchito kwa 24 hours.... Anatero yemwe anali katswiri wazama computer.

Bwana: ooooh anyamata anga, good work ndisaname...

Minister: apapa ndigwiritsa ntchito number yangayi kuyambira pano mpaka mbavazi zitagwidwa...

A Minister pompo anapereka order ku Military force kuti asirikali 50 apite ku cape town ndipo 30 apite ku Lodge yomwe kuli JAME akawagwire...

Apa Jame ndi Mkazi wake, asakufziwa kathu ndi Aubrey yemwe ndimkazi wake Tinashe.

Tinashe ataona kuti Laptop ๐Ÿ’ป lazima, anadziwa ndipo anapanga sense kuti laptop ๐Ÿ’ป singazime choncho pamene ili normal...

Tinashe; hunnie?

Aubrey; yes baby ndikufuna ndizigonatu koma,,,

Tinashe: china chake sichiribwino, laptop ๐Ÿ’ป yanga yazima ndipo sinazimepo ili mwa normal ngati m'mene zakhaliramu lero...

Aubrey: (modabwa๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€) Eeeeeee??? Yazima??

Tinashe: eya ndipo zikuonetsa kuti tapangidwa huck and block.... Kamba koti pa laptop ๐Ÿ’ป yanga yi chirichonse chinali bwino ndipo palibe chomwe chimavuta, and apapa ka bulb ๐Ÿ’ก ka red-ka๐Ÿ”ด kakuyakaso bwinobwino kusonyeza kuti iku charge. Koma yangozima yokha basi ngati kuti sikulandira moto...
Ndikukhulupirira kuti atipanga Trace ๐Ÿ—บ ๐Ÿ—บ apapa tisamale babie....

Aubrey: ooooh my God, zikhoza kukhaladi zooona izizi. Kamba koti ndim'mene tawaphera asirikali ao aja sangangotisiyasiya chonchi....

Tinashe: apapa ndiye kuti Jame ndi Mkazi wakeso akhoza kukhala pa mpeni kamba koti adziwa kuti Jame akulumikizana ndifeo more over ndi ๐Ÿ’ฃ bomba lomwe laphulika lija kunyumba kwake kuja ndikupha asirikali onseyaja obviously iyeyonso akuyenera kumupanga Trace kamba koti sangamusiyesiye and akudziwa kuti akamupeza iyeuja ifeso atipeza mosavuta....

Aubrey: eeeee ndipo apopo nsaname Tinashe. Umaganiza heavy.... And ndikukhulupirira zomwe ukukambazi .
Shaaaaa, ndiye titanino apapa?

Tinashe: titenge phone yakoyo pompanopompano ndipo umutumizire Jame messege kapena kungomuimbira kumuwuza kuti athawe pompano akatelo achotsemo Simcard yo, Simcard yo asaitaye,
Ngakhale kuti akhoza kutipanga trace kugwiritsa ntchito Simcard yo, akangoitaya zitivuta kuti tizalumikizane naowonso kamba koti ifeso kuno tikhala tikusithaso Simcard ndi phone yonwe.
I think ๐Ÿค” ma messege anthuso aziwawona tikamalumikizana ngatidi ati huck kunyumba ko,
Ndiyeno plan yomwe tipange apapa ndiyakuti, tikaika Simcard mu phone ndikulumikizana ndi Jame, tidziiichotsamo ndipo pompo tizisitha malo.
Pambuyo pa izi, tikuyeneraso kulumikizana naye Jame muchiyakhulo chovutirako kupatulula chichewa, English ndichi zulu kuti asamatitorere mphweka.
Ndichiyakhulo chanji chomwe ukuona kuti tikhoza kumanvana naye Jame?

Aubrey: eeeee apo ndiye ndizoonadi, chisena ndichomwe Jame amanvaso.

Tinashe: okay, tisachedwe mtumizireko messege kapena olo ungomuimbira pompano athaweko maningana ndi nthawi.

Aubrey anatenga phone ija ndikumuimbira Jame apa nkuti chirichonse chomwe amakambira Aubrey ndi Jame pa phone akuzinva pama computer ao A Minister, ndi Abwana ndi ena onse ku room yao. Asirikali nao atatsala ndi 3 minutes yokha kuti afike ku lodge kuja.

Aubrey: hello Shamwali, chonde ne usalonge pilongero pinango tayi, koma chinalongenechi basiyene, thangoyache taphwata napyachitefe pire...

Meaning yake: hello aise, chonde usalakhule chirakhulo chirichonse, koma chomwe ndikulakhulachi basi kamba koti tagwidwa ndizomwe tapanga zija....

JAME: waaaa, taphatwa tani potho shamwali?
Meaning: iiiiiii, tagwidwaso bwanji aise?

AUBREY; waaa usapidwalire tayu kuti ninalimbana naifewa ngakugoswa.. Nakupanga npholemphole pyepyo ola pano tiribe tayu bukako kweko nankazakoyeneo mwachinchino pano anaphatwako..

Meaning yake: aaaa, usaiwalire kuti amene tikulimbana nawowa ndiopsa.. Ndikuwuza bwinobwino zazimenezo nthawi pano tiribe chokako kumeneko ndimkazi wakoyo pompano ugwidwako.

JAME: kamala m'muji ndiye ndumo mwamala gaka na moto, ndiye penu tinayenda kupi kamala?

Meaning: ndiye kunyumba ndiko kwatha kuyaka ndi moto ndiye tipita kuti kaya?

Aubrey; baaaaa, ndokoni olo patchanga pena, munaphatwaaa baa, muibulusemo khadi yanu chinalongeranaifechi wapinva penu? K**ala pepobi, ijaikhemo pangamala ma ola ashanu nawiri mangwana kunja kungaecha..

Meaning: aise, pitani olo patchire, mugwidwakotu aise, muichotsemo Simcard yanu mu phone mo wandinva kaya? Ukatha udzaikemoso after 7 hours kunja kukacha..

JAME: nachita tepo baa... Mwachinchino pano
Meaning: ndipanga choncho aise... Pompano.

Eeeeee koma olo ineso mwandipinda palibe ndichimodzi chomwe ndanvapo babie ๐Ÿ˜๐Ÿ˜โ˜บ. Well ndiyeno apapa chotsa sim card yo mu phone ndipo usatengeso zovala zako, tenga zofunikira zokhazo tizithawako kuno. "Anatero Tinashe' atamaliza Jame kulakhulana ndi Aubrey.
A Minister; aaaaa???
(Molusa muja๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ) akuti chani apaa??

Bwana: talakhulani akuti chani kodi anthuwa?

Richmond: anthuwa ndiafiti ndithu ndikhulupirireni.

Atafunsidwa ma exparts aja, m'modzi mwaiowo anayakha,
"Mmmm bwana, ndisaname chirakhulo ichi sindinachinvepo olo kuchionako olo,,,

Minister: tafufudzani pompano....!

Bwana: mmmmm a Minister? Chirakhulo ichichi nchakumalawi Ndipo chikuyenera kukhala chisena koma vuto sindimachinvaso ndichovuta kwambiri cha mtundu wa anthu ovuta maganizo kwambiri...

Richmond: eya,,, ndanenatu kuti anthuwa ndi afiti.. Chirakhulo chanji chimenechi olo m'machinva m'mene chimanvera muja???

Anangonena kuti ndichisena, anayamba kufufudza pa computer yaoyo on Google translate Language...
Ndipo akanvera voice ija anapanga record yo, abwana amalakhula wa computer ndikumapanga type...
Ndipo zinawatengera mpaka 10 minutes yokha nadziwa chomwe amakambiranazo pambuyo poti anafufudza on Google translate.
Apa nkuti nawo asirikali aja anali atafika kale ku lodge ija Ndipo ena analowa mkati mwa Lodge yo pamene ena anazungulira panja pake ponse uku mifuti yao ilim'manja.
AINUAKE a lodge ndi antchito ena onse kunali maso okha mwaaa kuyang'ana, ndipo ataona kuti inali Military Force yopsa ija itachita kukungana ndi akasinja ao panja ponse sanafunseso olo pang'ono chomwe amafuna asirikali wo ndipo m'malo mwake kunali kungoyang'anira basi kuti apange zomwe akufunazo basi.
Atatsala pang'ono kufika ku room lomwe anabuka Jame ndi mkazi wake, asirikali kunali kuchenjezana kuti akhala osamala pamene akutsegula chitsekocho kamba koti munthu yo anali oopsa kumbali yama bomba ๐Ÿ’ฃ pambuyo poti waphaso asirikali 10 usiku wake omweo ndinkhani yama bomb ๐Ÿ’ฃ ๐Ÿ’ฃ yomweo.
Asirikali kunalidi ntcherutu pamene Wankulu wao anayamba kuwerenga.
A Minister, a bwana komanso Richmond ndiama computer onsewaja akuonerera pa computer yao.
M'mene amapangira asirikali wo.
Atangoyamba kuwerenga kuti 5....
Eeee, A Minister anachita kuyang'ana kumbali uku atagwira kumutu kuti anve zokuthaitha
Maningana ndim'meneso zichitikira ndi asirikali oyamba aja....

5...........
4......
3...
2..
1.
Atangoti, 0.........
Anatsegula chitseko chija ndikulowa kuchipinda kuja, ndipo anaimba phone nsirikali yo kuti Jame uja wamupeza...
Mama ma!!! Koma kunali kunyadira Abwana, Richmond, a Minister ndiama computer aja kuti chigawenga chija achipeza....

A Minister: hahaha! ๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚ Ndimadabwatu kuti mbalame ngati imeneyi ingativute ifeo????

Richmond: hahaha huuu kumeneko ndiye kubwera.

Koma anakadziwa, sibwezi atayambiratu kusangalala, Wankulu wa asirikali o atakafundukura pa bed po anapeza kuti zinali zovala anazikulunga pogonapo zomwe atazifunda zimaoneka ngati anthu. ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ 
NOOOOOOOOOOOO! NOOOOOOOO!!!!!!!!!!
NOOOOO!
Apa abwanao, Richmond, ama computer wo komanso abwana akuzionera okha malodzao..
Mpaka a Minister ataona zimenezozo myendo inachita kuziziritatu mpaka kugwa pansi
๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚ malodza awa palibe amene anawakhulupirira kuti Jame ndi otani..
Asirikali atayatsa ๐Ÿ’ก bulb lakuchipindako anaona chingwe china chitatulukira pa window mpaka pansi NDIPO anadziwa kuti Jame anabanduka...

Richmond: ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜  Hayii,,, ndinanenatu!!!! Anthuwa ndi afiti.......

Next..........
๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚
๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚
๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚
Eeeeee apa ndakomoka ndithu......
Kodi kuthawa kwake kwakanthawi kokhaka anathawa bwanji? zinatheka bwanji zimenezi, nanga ngati anabisala momo anabisala malo otani???
Kodi a Jame ndi Aubrey kupanga Tinashe paiwo okha anakakwanitsa????
Aubrey ndi Tinashe ziwathera bwanji ku cape town ko pamene asirikali okwana 50 awalondola kale konko?
Mkazi wabwana naye wazizira nkhongono ndi mzukwa umeneu ๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚, kodi apanga zotani????
Next is part 21....

Whatsapp number for group
(+265994917253)
Pa WhatsApp tinamaliza ndipo tinayambaso nkhani ina.

Written by Aubrey That'sDhe Boss ```

27/07/2021

```CHIKONDI CHIRIBE MASO
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Part 19
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Short Stories by "Aubrey That'sDhe Boss"
Story from the book of
"Amuna Amuna Anga"
๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ
๐Ÿ‘€

Tinasiyira apa๐Ÿ‘‡ mu part 18.

M'mene nthawi imati 10 o'clock asirikali aja anali akutulukira ku nyumba kwa Jame kuja, apa Richmond, Abwana komanso a Minister akungowonerera video m'mene asirikaliwo amapitira, Aubrey ndi Tinashe nawo ali pa laptop ๐Ÿ’ป yao kuonerera chomwe chichitike chimodzimodziso uku Jame akusakidwao ndi Mkazi wake ali maso pa phone kufuna kuona chomwe chikufuna kuchitikacho.
Jame, Mkazi wake, Aubrey ndi Tinashe, onsewa samawawona asirikaliwo kamba koti camera yao imajambula pabalaza pokha nyumba ya Jame, koma Richmond, Bambo ake ndi Abwana ndiomwe amaona chirichonse ngakhale panja pomwe asirikaliwo anafikirapo kamba koti ama user setilite yomwe imaona pafupifupi pena paliponse.
Asirikali analipo okwana khumi (10) ndipo asanalowe mnyumba muja kunali kupatsana ma sign ndi manja m'mene muwaziwira asirikali ankhondo momwe apangira muja.
Mchoncho asirikali onse 10 kunali kuzungulira nyumba ija, ena pafupi ndichipinda cha Jame.
Atanvetsera nkati muja amanva kulira kwa wailesi ndithu....
Mtsweeeeeeeeeeeeeeee!
Apa kunali kugwedezera mutu kuti mbava ija yapezeka.....
Asirikali 5 anaima pa window onse mwantcheru kupangira kuti pamene asirikali ena 5 akhale akulowa nyumbamo Jame asatheso kupeza mpata othawa...
Asirikali 5 ena anatsegula chitseko chapa khomo polowera mnyumbamo nalowa koma onse akuchita kuyenda ngati mphaka olo ka mdidi..
Atangolowa, Jame ndi Mkazi wake no anayamba kuonano ๐Ÿ“ท video ija pamene asirikali amalowa mnyumbamo,

Mkazi wa Jame:(modabwa) ooooh, Mulungu wanga! Asirikali wa?????

JAME: eya, wazionatu? Sumachita makani wati tisalire???

Mkazi wa Jame: koma, babe, asirikali ake amenewa unakalimba? Taona zimphona zake iwe...

JAME: uziti tinakalimba????

Kukambadi chulungamo, asirikali ake sanali macheza, zinali zimphona zamphavu zao zija, zazitali ndizochita kuopsa komwe olo ngakhale ndi maonekedwe ao....

Apa naye Aubrey ndi Tinashe anali ndithu akuonerera masewerowo...

Aubrey: oooh akufuna apange chani?

Tinashe: dikira uone, asayerekeze kutsegula chitsekocho, akangotero onsewo alim'madzi!!!

Aubrey: ooooh kaya tione kuti zitha bwanji...

Apa nkuti nawo a Richmond alimaso pa Computer kuti mbava yothawitsa Mkazi wake Tinashe igwidwe basi...

Richmond: oooh apapa ndiye ameneyi olo patavuta maka mwamtundu wanji, mbava imeneyi singathawe...

Abwana; ofcoz kamba koti olo m'mene aizunguliramu nyumbao kuthawa kungavutedi...

A Minister: well, awawa ndima exparts ndithu olo ngakhale chiyambireni ntchito yao, palibe ndi munthu m'modzi yemwe anawakanika kumugwira.

Bwana: ndikhoza kugwirizana nanu kamba koti akuchita kuonetsa m'mene akupangira...

Mwa asirikali anayi (4) anatseka chitseko cholowera mnyumba ndikuima pafupi ndichitseko chakuchipinda chomwe nsirikali wina anagwira chotsegulira chitsekocho kuti azitsegula..
Koma anakadziwa sanakapanga...
AUBREY ndi Tinashe kunalitu kuonetsetsa kuti chichitike ndichani?
Naye Jame ndi Mkazi wake mitima inali m'mwamba uku ikugunda kuti Diii! Dii! Dii! Kufuna kuona chomwe chichitikecho.

Apa mtsirikali yemwe anagwira chitsekocho, anayamba kuwerenga kuti akangofika ka 0, akakha chitsekocho ndipo asirikali enao adzangofikira kulowa. Ndipo aliyense anali ntcheru kuti alowe ndipo akamugwire Jame komanso asirikali enaso 5 onse anali panja panyumbao pa window lachipinda chomwe amagona Jame ndi Mkazi wake anali aliso mcheru.
Apa anayamba kuwerenga ndi zala kuti,
5,.................
4............
3......
2...
1..
0
Atangokakha chitseko, akuti azilowa kuchipindako, panachitika spaki yoopsa Yamoto๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ wamagetsi ndipo Battery ija inaphulika ndikuyaka ngati ๐Ÿ’ฃ ๐Ÿ’ฃ ๐Ÿ’ฃ Bomba kuti PHUUUUU!!! ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ chimoto chazaoneni chija Mpaka mnyumba yonse ndipo asirikali onse anachita kunyenyeka ngati pepala la kope mene imasandukira phulusa ikamapsa ndi moto...
Pompo ma camera omwe amaonerera video Tinashe, Aubrey, Jame ndi Mkazi wake, anasiya kuonetsa atangowona komanso kunva kuphulika kwa bombalo...
Hey! Heeeey! Heeey! Zooosatheka! Ndikuti ndiooooooooooooosatheka!!!! Haay! Ama Camera inu chikuchitika apachi ndichani????? Aaaa?..
Eeee a Minister anachita kukula mutu akuti ndizosatheka zomwe amazionazo ndipo apa anachita kugwiridwa ndi abwana...
Apa naye Richmond kukamwa kuli yaaasa uku manja atagwira kunkhongo kusowa cholakhula...

Bwana: zosatheka! Ndikuti zitheka bwanji izizi???

M'modzi mwama exparts wama computer anayakha... ๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡
Aaaaah, Bwana?.... Anthuwa ndiopsa makamaka Munthu akusakidwao mukuti Jame yo...

Bwana; ndikuti chachitika ndichani iweee????

Apopo ndima.. Ndi.... Ndi. Ndimafuna ndiziti Jame simunthu wamba bwana, kamba koti system yathu itapanga search za bomba ๐Ÿ’ฃ sirinaonetse kuti kumaloko kuli ๐Ÿ’ฃ bomba.. Koma system yomwe anagwiritsa ntchito ndiyakuti, anatchera moto wamagetsi popangitsa spark ngati njira yachilokolo ndipo chifukwa cha spark yake ndiyoti inali yoopsa nchifukwa chake nyumbao inayaka motero ngat bomba ๐Ÿ’ฃ...

Minister: oooh, oooh, aha... Munthu yi ndiye kuti akutiwerenga.... Kamba koti matchera achitika apowo zachita kuonetseratu kuti amadziwa kuti akhala pa mpeni ndiyeo pakuthawa kwa nzakeo ndi Mwana wanu Tinashe.

Richmond; NDIMUPHA!!!! Ndimanja anga ameneyi.... Oooooh taonani? ๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Kupha asirikali onse 10 pakamodzi ngati nkhuku chonchi????? ๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Jame??? Jame??? Jame wandifikapo....

Bwana; ndipo mwazi wa anthu amenewa Jame uubweza mu 24 hours kuchokera pano and komwe uliko, yamba kuchotsera nthawi...
Ticwo tock tick tock tick tock

Minister; ndipo munthu ameneyi afe ngati mwana...

Pamene Nyumbao inayaka, panatuluka phokoso lalikulu lomwe linadabwitsa anthu oyandikana ndi mnyumbao kuti chachitika ndichani???
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Usiku omweo anthu kunali kuthamangira kunyumbao uku ena akuimbira a fire ๐Ÿš’ ๐Ÿš’ ๐Ÿš’ kuti akazimitse moto wo.
Alandilord kunali kuthamanga loliwiro ladoka lija kufuna kuona chomwe chinachitika pa nyumba paowo...

Alandilord:(manja alikumutu) ๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€ Hey!!! Hey!! Oooooh nyumba yanga!!!! ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ....
Nyumba yanga ine...!!!!

Anthu kunali kugwira kumutu kuti Jame ndi Mkazi wake onse afera momu,
Alinkati modandaula muja, galimoto la fire ๐Ÿš’ linafika ndikuyamba kuzimitsa moto uja apa zinthu zitaonongeka kale...
M'mene moto unachepako mphavu ndipamene mafupa a Sirikali ena amaoneka komatu mbali ina itachita kunyenyerekatu kaya ngati chani!!! Ndipo anthu ena atapeza mafupawo kunali kulira ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ ndikutsikimizadi kuti Jame ndi Mkazi wake wafera pangozio..
Zinali zonvetsa chisoni ndithu kwamaneba ndi alandilord pazakufa kwa Jame ndi Mkazi wake maningana ndim'mene amaoneramo.
๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ...

JAME: maaaa! Mamaine!!! Koma zooopsa aise....

Mkazi wa Jame; eeeeee koma iwe? Mkazi wa Aubrey ndioopsa iwe wanva? Mmmmm ndipo apa mkwiyo wa anthu awa ukhala ukukulirabe pa iweo mwamuna wanga kamba koti adziona ngati ndiweo unapanga chipongwecho kupha mpaka asirikali ons.

JAME; ndipo babie, ndikuyenera kusamala kamba koti apapadi mkwio wao ndiye wachita kukwereratu ndipo ngati BP yao inali pa 10% ndikukhulupirira kuti pano ili pa 99.8%....
AUBREY: apapa nzosachitaso kufunsa, asirikali onse pano ndikukhulupirira kuti ndimitembo basi komwe aliko...

Tinashe: zooonadi babie ndipo musakaikeso m'mene zatero awowo kwao kwathera pompo basi..

AUBREY: aaaa komano iweo ndiwe ooopsa kwambiri... Mmmmm wandidabwitsa...

Apa setilite ikuwinakabe ndipo ataona pa screen paja, expart wina anati๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡

A Minister? Musadandaule kwambiri ndipo apapa tapeza plan yompezera munthu ameneyi..
Mutume munthu m'modzi pompano kumalo komwe kwaphulika bombalo ndipo apite ngati ofufudza ndipo akaonetsetse kuti mwamaneba omwe ali pangozio kuonerera akamupatse number ya Munthu yo (Jame) apo ayi ya Mkazi wake.
Akatero atitumizira number yo ndipomwe timupangire trace pa phone yakeo musiku omweouno ndipo timpeza basi.

Minister: mzeru imeneo.....

Ndipo a Minister pompopompo anatuma munthu kupita kumaloko ngati ofufudza,
munthu ofufudzao anafikakodi kumaloko maningana ndi nthawi ndipo atafusafusa za number phone yamunthu yemwe wafao (JAME), anapatsidwa ndiyamkazi wake yomwe.
Pompopompo naye anaitumiza kwama exparts aja.
Atafika ma number phone aja kunalitu likiliki ndizam'mangum'mangu ku search ma number aja,
Ata search ๐Ÿ”Ž number ya Jame sinapezetse location iliyonse kamba koti Simcard yake inapsera limodzi ndi phone yomwe imajambula ija.
Ataika number ya Mkazi wake ndiyomwe inaonetsano za location yomwe ali Jame, kumbukirani kuti Jame panthawiyi amagwiritsa ntchito number phone yamkazi wake.
Number yo inaonetsa malo omwe anali Jame yo ndi Mkazi wake ndipo anachita kudziwa ndi Lodge yomwe amagonao..
Atapitirizabe ku search ๐Ÿ”Ž, mpaka anapezamoso number ina yomwe anagwiritsa ntchito kulumikizana ndi munthu wina, ataona conversation yama messenge yo anali odabwa nazo kwambiri ndizomwe amachezazo.
Atapanga search ๐Ÿ”Ž bwinobwino za number yachirendo yomwe imaonetsa mu phone ya Jame yo anadziwa kuti anali Tinashe ndi Aubrey..
Pompo atapangaso search ๐Ÿ”Ž, inaotsetsa location yomwe inali Tinashe ndi Jame komwe uko ku Cape town...

Minister: hahahahhaha

Bwana: wapezaka wapezekaaaaaa!!!!

Richmond: aha! Zikuonetsa kuti ndawina chigao tsopanooo........ Uchi wanga wapezeka Huuuuuu!!!

Eeee apa kunali kusangalala ndipo Pantchito yoopsa yomwe anaipanga ma exparts wo mpaka kuwapeza anthu onse ndimalo omwe ali tsopano.

M'modzi mwama exparts analakhulaso.
A bwana, phone yanuo musaigwiritsetso ntchito mutuma order yowafufudza anthuwa I think ๐Ÿค” ma plan anthuwa anadziwika kamba K**a messege omwe mumatumizirana ndi asirikaliwo, ndipo number yachirendo yomwe tafufudzai ndiyomwe ima hucker ma messege anuo.
Apapa ndikufuna ndii block computer yomwe akugwiritsa ntchitoyo ndiye ndikudikira chirolezo chanu bwana...

Bwana: well done, I block pompano....

Pompodi computer ina block kedwa, mpaka laptop ๐Ÿ’ป la Tinashe inazimira pompo kamodzindikamodzi kuti Thiii!!!

Zatheka bwana ndipo isiya kugwira ntchito kwa 24 hours....

Bwana: ooooh anyamata anga, good work ndisaname...

Minister: apapa ndigwiritsa ntchito number yangayi kuyambira pano mpaka mbavazi zitagwidwa...

A Minister pompo anapereka order ku Military force kuti asirikali 50 apite ku cape town ndipo 30 apite ku Lodge yomwe kuli JAME akawagwire...

Apa Jame ndi Mkazi wake, asakufziwa kathu ndi Aubrey yemwe ndimkazi wake Tinashe.

Next......
Nkhani-yi ndiye yafikapo ndithu, Jame sakudziwa kathu kuti kwatumidwa asirikali okwana 30 kuti amugwire, kodi olo Jame yo, apapa angalimbe???
Nanga asirikali 50 amene akupita ku cape town wo, zikathako bwanji poti Tinashe ndi Aubrey sakudziwapo kathu kenakalikonse Laptop ๐Ÿ’ป amadalilao nayo ndiyo yapsao.
Next is part 20..
Kodi zitha bwanji?? ๐Ÿค”๐Ÿค”๐Ÿค”๐Ÿค” nawo a Richmond zikuonetsaso kuti zao ziripabwino ๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚

Whatsapp number for group
(+265994917253)

Written by Aubrey That'sDhe Boss ```

25/07/2021

```CHIKONDI CHIRIBE MASO
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Part 18
๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€
Short Stories by "Aubrey That'sDhe Boss"
Story from the book of
"Amuna Amuna Anga"
๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ
๐Ÿ‘€

Tinasiyira apa๐Ÿ‘‡ mu part 17.

Aubrey: apapa basi sister wangao sindirimbana nae komwe aliko kaya alimoyo kaya wafa koma mzimu wake ukhale wamtendere, apo ayi ause mumtendere......
Ndikusasamala kwangwa komwe mkwampangitsa mlongo wanga kukasowa ndipo uwuwu unali udindo wanga womutetezera and sindikudziwa kuti ndikapita kunyumba Amayi ndidzikawauza chani ine??? ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ

Tinashe: babie musalire chonde inu...... I know how pain your feeling ๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข

Aubrey: ๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข, babie, apapa m'mawa basi chama 3 o'clock m'banda kucha ndikupita ku airport ๐Ÿ›ฌ ndikadulitse matikiti anthu basi tizipita...

Tinashe: ๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ข๐Ÿ˜ขokay amuna anga mulimonsemo ndipanga basi.

Naye Jame mutu unali utamukuliratu ndinkhani imeneyi kuti olo mkazi wake amuyambira pati kumuwuza zazimenezi.

Mkazi wa Jame: koma Babie, chachitika ndichani??? Mmmm inetu ndi mkazi wako and sunayenere kundibisira chirichonse kaya, ndiuze..

JAME: oooohk, ndinkhani yaitali komano ndingofotokoza mwachidule...
Paja Aubrey amagwira ntchito yokamusiya mwana wabwana ku school, ndiye kunabwera mtsikana wina timamuti Tinashe mwana wabwanao from America ๐Ÿ‡ป๐Ÿ‡ฎ kokapanga maphunziro ake. Tinashe ndizoti primary yake anaphunzirira ku Malawi ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ komwe anapalanako ubwezi ndi Aubrey, kuchokera pompo anasiyana pamene Tinashe makolo ake anamuitana kuno South Africa ๐Ÿ‡ฟ๐Ÿ‡ฆ kuzapitiriza maphunziro. Ndiye ataonana ndipomwe Tinashe anamukumbukira Aubrey ndikupalanaso ubwezi, bambo a Tinashe atadziwa kuti Aubrey wantchito wao apalana chibwezi ndi mwana wao, zinawaipira kwambiri pambuyo poti mwamuna wamwana wawoyo anali atampeza kale, Richmond dzina lake mwana wa a Minister....
Ndiye ataona kuti mwana waoyo wamukondetsetsa kwambiri wantchitoyo anagwirizana ndi a Minister wo kuti amuphe Aubrey yo!

Mkazi wa Jame: chaaani????? Mmmmmm mpaka pamenepa zooona?

JAME: eeeeeee moti apapa Aubrey amuthawitsa mwana wa abwanakeo moti ulendowu ndimakamusiya kutali ku Cape Town.

Mkazi wa Jame; mmm ndinamuona tsiku lina katsikanako ndiye kakongolerenji mayi, ndi Aubrey yo zosakhalana zija and ndizoonadi kuti CHIKONDI CHIRIBE MASO..... Komano abwanao samusiyasiya Aubrey amafufudza basi mwanjira iliyonse....

JAME: for sure moti Abwana wo ayamba kale Kupha anthu omwe akukhudzidwa ndinkhani yi pazakusowa kwa mwana wao, moti ๐Ÿ‘ฎ officer waphedwa kale komanso gateman wakunyumba kwao ndiamene timawaona pa ๐Ÿ“บ TV pankhani zamadzulozi.

Mkazi wa Jame: ooooh God for bit... Ndiye Aubrey yo bwanji akuleka kungothawira ku Malawi ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ! Komanso ifeo izizi zikhoza kutivutirako mesa akudziwa kuti Aubrey yo amakhala kuno ndiweo?..

JAME: eya akudziwa zimenezo ndithu, moti apapa ati akufuna abwere kunoko azathane nane kamba koti adziwa kuti ineso ndiamene ndamuthandizira Aubrey kuti amusowetse mwana wabwanayo.
Ndiye apapa chonde mkazi wanga undinve sindikufuna m'mawa ndidzakhale mtembo ine pano pamaso pako tisanadyerere chikondi chathuchi. Pa chifukwa ichichi tiye tingosowa madzulo pompano tione kolowera.....

Mkazi wa Jame: chani? Babie ulibwinobwino koma iweo? Usiku ngati uno tizilowera kutiko nanga?

JAME: usadandaule mkazi wanga, ndikudziwa kuti nzovutadi kuti undinvetse komano undinvetsa pamawa zikazachitika, zakatunduso aliyense tiye timusiye mom'muno ife tizithawa.....

Mkazi wa Jame: babe sizoona izizi koma... Mmmm? Ineso nsaname sindingakwanitse..

JAME; (mokupsa mtima๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ) iwe!!!! Ukufuna ndife???? Eeeeee?? Ine ndimwamuna wako ukuyenera kundinvera kaya, tikutayatu nthawa apapa ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ !!! Sukuona? Okay fyn ineo ndikukanyamura chikwama changa chakumbuyo ndiziona kolowera iweo zitsala ndapita....

Mkazi wa Jame: babie,,,, taimani kaye! Inuo zinthuzi mwazirakwinitsa nokha pondizizimutsa ngati chonchi, koma bola munakandiziwitsako masiku am'buyomu bwezi pano tikudziwa zochita kaya....

JAME: (molusa ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜ ) iwe, ndakuwuza kale! Kuti ngati usakufuna tsalaa....

Mkazi wa Jame: amuna anga musandipsere mtima vuto sineo kaya......

JAME: (mwamwano) Mervis??? Ineo ukufuna undiuze ndimazidziwa izizi kuti zingafike apapa? ๐Ÿ˜ ๐Ÿ˜  sungaone wekha pafika zinthuzi mpaka officer ๐Ÿ‘ฎ wa police kuphedwa ndiye ine ndindani? Ineo sindimakonzekera kaya, and ndichifukwa chake ndamuthawitsira Aubrey kutali kuti mwina mwake tithe kukhala pa mtendere ngati mwakale...

Pompo mkazi wa Jame sanayakheso kena kalikonse anangoweramitsa mutu pansi kuti atani, Jame atakolowa kuchipinda kukapakira tizovala zake, naye mkazi wake anamulondola kuchipindako nkumakapakiraso nae zovala zake mu laptop bag.

M'mene nthawi imati 9 o'clock ya usiku, mkazi wabwana ananyamuka ulendo wakuntchito kwake..
Atafika analowa ndikukafikira kukumana ndi Hildah...
Hildah atawaona abwana ake atulukira, kunali kuwathamangiratu mwa nsangalala aja anvekere
"Oooooh Mulungu alolaso kuti tikumane". Koma mukupezako bwanji madam?

Janet: pang'onopang'ono basi nzoti ndachita kuthawakotu ku chipatala...

Hildah; mmmm oooooh?

Janet: eya, koma business yayendako bwanji m'buyo mwangamu?

Hildah: chirichonse chinali bwino madam koma we had one problem yomwe inachitika kunoko.

Janet: mmmm? Vuto lanji makamaka?

Hildah: a gate man analowa nyumba muno eti kumazamugwiririra Cathy uja mpaka Cathy anayamba kukuwa ndikuthawa. Nditakalowa ku room komwe kunali Cathy kuja nsinampeza cathy yo atathawako ndipo nditamufunsa gateman uja kuti wapita kuti Tsikana umamugwiririra yo, anayamba kuyakha mwano ndipo ndinamuombera ndi mfuti pompo ndikufa....

Janet: ooooh komano iyeyo anaganiza bwanji mpaka akalowe muno ndikumazagwiririra munthu odwala ngati ameneuja?

Hildah; ineso kudabwatu kuti mpaka level imeneyi?? Moti nsaname anandipsetsa mtima ndikumuombera...

Janet: ofcoz kuti unatero komano unakawasiya ndikuzandifotokozera ndekha ndikabwera zinakatichitira ubwino...

Hildah: ndizoonadi madam moti ineso ndinatha kuona kuti ndalakwitsa Koma zinali zitachitika kale ndiye nanga ndinakatani, komanso sinanga sindimayembekezeraso kuti mufika lero. Pepani madam ndinalakwitsadi.

Janet: ooohk its okay osadandaula ndakunva zimachitika, ndiye nkhaniyi waidziwa ndindani kunoko?

Hildah: mmmm Sindikukhulupirira kuti alipo amene anaonerera izizi zikuchitika...

Janet: ooooh well ngati palibe yemwe akudziwa its okay palibe kathu...

Ndipo Umu ndim'mene Hildah anawabwatikira nalo bodza abwana ake Janet mpaka anakhulupiriradi chirichonse maningana ndim'mene amafotokozera Hildah..
Memory aliku room kwake anangodabwa Cathy watulukira kuchipinda kwake mwabefu, atamufunsa nkuti nchifukwa chani akuoneka wamantha komanso anathawiranji komwe analiko...
Cathy anafotokoza chirichonse m'mene zinakhalira ndipo atafotoka Memory kunali kuseka mwankhaza muja atanva zoti mpaka Hildah anakomoka ndi plan yomwe anaseweredwa ndi Cathy yo, mukucheza kwao kunapitirira motere.

Memory; (๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚) aaaaaa Koma Amayi, amayiiinee hahaha ndafwa basi... Eeee komano iweo unaganiza bwanji mpaka pamenepa...
Ndiye wadziwa ku room kwanga kuno sealing inaboka pakakona apo ndipo chotsekera ukuchiona apocho ndimachita kutsekerapo.. Bwanj kwapanopa uzigona momo ndipo uzikhala kaye momo usakuoneka... Chakudya zakomera kuti ndimaphika ndine ndiye ndizikubweretsera mam'mawa, masana ndimadzulo za toilet osadandaula tipezaso njira chapompano.

Cathy: oooohk ok, poti palibeso malo ena omwe ndikhoza kumakabisala its okay nditero mpaka tione pomwe pafike zinthuzi.....

Memory: apapa zinthu ziribwino atetha mutu amenewa amayenda mbali lero ayenda pakati ndithu....

Umu ndim'mene Cathy ndi Memory anagwirizana zoti azichita ndipo anamulowetsa mu sealing mpaka anampasa zofunda ndizoyala zake namutsekera konko...

Janet: ndiye Cathy panopa alikutiko?

Hildah: mmmm alinkati mom'muno Koma sindikudziwa kuti exctaly pati pati...

Janet: m'mawa lonse lisadutse asanapezeke...

Hildah; ok bwana zanveka.......

Apa Hildah anayambano kulingalira kuti Cathy zuthekaso bwanji kuti amupeze ndipo mutu unayamba kumutetha kuti nanga m'mawalo sapezeka, abwana akeo amupanga zotani?
Hildah anayamba kulingalira mpaka motere ๐Ÿ‘‡
"Shaaa Koma ineo ndipange bwanji, cathy nduyo wasanduka mzukwao, Koma izi zindithera bwanji? "
Koma a Hildah ngati safotokoza bwinobwino kwa abwana ake zokhuza Cathy yo kodi abwanao achirandira motani komanso apanga zotani???

M'mene nthawi imati chama 11, Abwana ake Aubrey aja anawaimbira akazi ao (Janet) kuti apite kunyumba, kunyumbako kunali abwana, Richmond komanso ndi a Minister ndi ma exparts aja odziwa ma computer anali atawaitana....
Mkazi wabwana amafunikira kuti afotokoze zakomwe Aubrey amakhala...
Atafika akazi abwana aja ndikufunsidwa anaperekadi direction yakomwe Aubrey amakhalako.
Apa Bwanao kunali kutumiza information yokhudza Aubrey, maonekedwe ake, location yake ndi zambiri kwama Expart wo odziwa ma computer komanso anatumiziraso asirikali ena ofufudza mwachinsi aja, kukakhala m'ma border ndiye nkhope yakeo ndi ya Tinashe zinali zitafika kale...
Apa nthawi iyi inali yausiku ndithu pomwe amakambirana izi, program inali yoti Aubrey asakidwe kaye mwachinsinsi ndi asilikali achinsinsio muusiku wa m'mawa, ndipo Odziwa ma computer wo anapatsidwa nthawi yakum'mawa kuti ayambe kumufufudza Aubrey yo pogwiritsa ntchito setilite.
Nthawi ikuti chama 12 o'clock pakati pa usiku, Aubrey anali atagona Koma Tinashe naye anali pa Laptop ๐Ÿ’ป yake, alinkati mopanga zomwe amapangazo anamuzutsa Aubrey mwaphuma muja...

Tinashe: Hey,,,, Aub??? Aub......!!! Aub???

Aubrey: (mitopatopa) mmmm.... !!

Tinashe: tadzuka uzaone izi!!!!

Aubrey: chani....??

Tinashe: zomwe apanga bambo anga...

Aubrey; (mozizimuka) Eeeee๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€๐Ÿ‘€?!!! Apanga chani???

Tinashe: tafikatu babie uzaone...

Aubrey anadzuka mwamphavu muja ulendo okaona...

Tinashe; awa ukuona apawa ndima messege omwe amatumiza bambo anga pa whatsapp...
Amatumiza zinthuzi zathu....

Aubrey: Eeeeeee?????????????????

Tinashe: eya, and apapa zimapita kwa asirikali apa border komanso m'ma airport ๐Ÿ›ฌ osiyanasiyana muno mu South ๐Ÿ‡ฆ Africa kuphatikiza secrets army forces..

Aubrey : ooh oh, oh... O... Ooooh hwwuuuuuu!! Mulungu wanga ma doko onse apa oti tinakatha kutulukira ndiye atsekedwa..

Tinashe: sizokhazo babie, map ๐Ÿ—บ akunyumba komwe umakhala ndi Jame kuja apezekaso pa list yama messege yao.... Zomwe zikusonyeza kuti Jame ndi Banja lake liri m'madzi...
Apapa babie titani?

Osanama Aubrey anagwira kumutu podziwa kuti game apapa ndiye yalakwa and ku airport ๐Ÿ›ฌ kuja nako kwamwa madzi, akaona m'ma border namo ndumo munaikidwa mingazo..

Aubrey: okay babie... Apapa, pakufunika mzeru zakuya koopsa kamba koti pafika zinthuzi ineo ndikuyenera kuvomereza basi ndipo ngati ndikufa, ineo ndifera konkuno basi.
KOMA NGATI NDICHONCHO AAAPA SINDILOLA KUTI NDIFE NGATI MWANA, NDIFA NANE NDITAZUNZA.

Tinashe: babie inu musamakhale chonchi... Zokufazo ineo sindikugwirizana nazo....

Aubrey: sinanga ukudziwa kale kuti iweo mwanjira iliyonse sungafe Koma ineo...

Phwaaaaโœ‹! Amayo!!!
Ichi chinali Chimbama chomwe Tinashe anamuomba nacho Aubrey atalakhula mbwerera...

Tinashe: iwe wandikwana wanva!!! Ungamanene zimenezi zoona? Kodi ineo ndirikuno chifukwa chani? Eeeee? Makolo anga ndichifukwa chani ndinawathawira nyumba mwao nkumadzakhala ndiweo kuno???? Eeeee?

Aubrey: its okay am ๐Ÿ’” sorry... Kungoti m'mutumu mukuyenda zinthu zambiri....

Tinashe: usamang.........

Akuti Tinashe azimalizitsa kulakhula phone ya Aubrey inkaitana....

Aubrey: Hello...?

Hello man ndineo Jame, ndimati ndalama ija mutumiza nthawi yanji coz ineo am ready apapa..

Aubrey: ooohk man sorry naiwala man more over apapa m'mutumu zinthu sizikulongosokabe man.
Si uli pa mukuru paja?

Jame: eya man... Number yake utumizire yomweyi ndiya mkazi wanga....

Aubrey: ok man wait for few minutes.....

Patangodutsa ma minutes ochepa Aubrey anatumiza ndalama ija...

JAME: babie... Musadere nkhawa plz plz, amati chiyambi cha mtendere ndi mavuto... Ndipo pakutha kwa izizi tidzakhala osangalala kwambiri as a family....

mkazi waJame: (mosisitika) mmm ok.....

JAME: babe,,,,, mukulakhula mosisitika chifukwa chani? Mmmm?
Apapa tiye tinyamuke tikakwera Tax tizipita ku Lodge.....

Mkazi wa Jame; ok amuna anga ndikunvani... Ndikusisitika kumene kamba koti izizi nsaname sizikundisangalatsa olo pang'ono.

JAME: oooh chabwino ndakunvani...

Jame akufuna azinyamuka anamuimbira phone Aubrey....

Phone: Ring....! Ring.....! Ring......!

Jame: hello....!

Aubrey: yes man, yafika?

Jame; eya apapa ndikunyamukatu man....

Aubrey: taima kae usadule phone akuti Tinashe akulakhule...

Tinashe anamulanda phone Aubrey.

Tinashe: hello???

Jame; yes Tinashe...

Tinashe: ulinyumba?

Jame; ayi apapa ndiripanja ndikufuna ndinyamuke ndizipita apapa...

Tinashe; ooohk, ubwerere mnyumbamo pompano upite pomwe pali switch yamagetsi yanyumba yanuo...

Jame: ohk ndikulowa...

Tinashe: umpatse torch mkazi wakoyo azikuwunikira ukafika pa switch yamagetsio.

Jame: ooohk ndafikapo.....

Tinashe: tagwetsa mita yo...

JAME; OK.....
Yah ndagwetsa.....

Tinashe: ndinaonamo nyumba mwakomo Battery ๐Ÿ”‹ la Galimoto m'mene ndinafika muja, sindikudziwa ngati ilipo...

JAME: ilipo....
Ifike????

Tinashe : eya....

JAME: ok...
Yah aibweretsa yafika....

Tinashe: uimange ndi nthambo ziwiri kuma terminal akeo koma uisephanitse, positive uike ku negative ndipo negative uike ku positive..
Battery yo uike pafupi ndikuchitseko chakuchipinda kwakoko. I think ๐Ÿค” switch ilipafupi ndikuchipinda kwanu?

JAME : eya anaika kuchipinda kwathu... Ndapangatu...

Tinashe: ok well, utenge nthambozo zomwe walumikiza ku battery yo ndipo ulumikize pa main switch yakoyo, utsegule chalatacho ndipo uonamo nthambo zambirimbiri ndiye paliso zina ziwiri zazikuluzikulu ya black ndi red..

JAME : yah ndaziona....

Tinashe: yah ndiye uzisupule, ukatero utenge nthambo ya red yaku battery yo ulumikize pa nthambo ya red so yaku switch yo negative so chimodzimodz...

JAME: ndisasephanitse????

Tinashe: eya tasephanitsa kale ku battery yo..

JAME : ooohk.....
Yah zatheka...

Tinashe: ok tenga, ulusi wa twin ngati ulipo....

JAME; mmmmm twin tiribe.....

Tinashe: ok wazovala ulipo???

JAME: eya koma wa black....

Tinashe: ok ziribe kathu,,, uyeze kuti ndima meter angati kuchoka pomwe pali switch yako ndikufika pachitsekopo...

JAME : ooohk
Ndayeza ndima meter 5...

Tinashe: yeza ulusi wakowo ma meter 6 ndipo ukhale ndima line 5 kuti usaduke, ukatero ukaumange pomwe pali kokhethemula ka switch ko koma molimba.... Ukatero pamwamba pa switch po ukhomepo ka nsomali ka 1 inc ndiye ulusio ukokere pomwe pali nsomalipo koma chonde pamene ukuwukokera m'mwamba ulusio switch isayake...

JAME: ok zikunveka ndipo zatheka...

Tinashe : ndiye ulusi wadutsa pa nsomalipo ukokere pafupi ndichitseko chakuchipindako, ukhomeso ka 1 inc kansomali pakakona pomwe payandikana ndichitseko chakuchipindako koma mukhale m'mwambabe ndichitseko. Ukatero uonetsetse kuti ulusiwo wakungika bwino.

JAME: zathekatu....

Tinashe: ndikukhulupirira kuti chitseko chinali chotseka m'mene mumakunga ulusio?

Jame: eya moti apapa olo kuti titsegule chitseko ndiye kuti ulusiu ukokeka ndipo switch ndikukhulupirira kuti ikhozaso kuyaka.

Tinashe: hahaha eya ndichoncho ndipo osayerekeza dala.. Mutulukire pa window...

Jame: hahaha eeee ndatha kuona apa kuti bombs ๐Ÿ’ฃ ndiye yatcheredwa..

Tinashe: yah ndipo musakaike....

Apa Jame anatsegula window ndikutuluka ndi mkazi wake, ndipo anachita kusiya ka wailesi kakulira chapansipansi kuti tsweeeeeee kuti anthu aziona ngati muli anthu.

Apa atatuluka anamuimbira phone Tinashe uja ndikumuwuza kuti watulukamo...

Tinashe: ohk komano phone yako imalimba moto ngati?

JAME: mmmmm 7 hours tu data akakhala on.
Koma ndirindi power ๐Ÿ”Œ bank...

Tinashe: okay ziribwino, yatsa wifi๐Ÿ“ถ wako ndipo upange connect ndi wifi ๐Ÿ“ถ yomwe alipafupi. ulowe pa Google ...

JAME: mmmm ๐Ÿ“ถ wifi wakuno ndiwa password.....

Tinashe: ooohk, gula bundle ya mwezi 5GB ndindalama yomwe tatumiza pa mukuru yo.
Koma uonetsetse kuti Simcard yomwe ukuikako mu phone isakhale yantchito kwambiri kamba koti suzaionaso!!

Jame: aaaaa easy ndakunva..

Tinashe: yah ulowe pa Google ndipo upange download application yotchedwa IMO.. Then umpange install..

Jame: oooh
Zatheka tu....

Tinashe: umulowe application yo ndipo upite kuma sitting akeo...

Jame: ndalowako....

Tinashe: upite pomwe palembedwa call and messages, ukatelo upange select pomwe palembedwa answer video calls automatically.
Ukatelo upite kuma settings a phone yakoyo ku Display ukapange select pa Display Light then upange always on...

Jame: zatheka....

Tinashe: okay data usiye on... Komanso uike pa power ๐Ÿ”Œ bank izikhala iku charge ukatelo phone yo ukaisiye pa sitting room pobisika poti munthu atakhala kuti walowa nyumbamo satha kuona koma camera ya phone ikhale angle yabwino yoti itha kumajambula zonse. Komanso ikhale ku silent... Chifukwa choti magetsi ndiozima uyatse Torch uike pa table kuti paziwala....

Jame; oooh chabwino ndakunvan...
I think ๐Ÿค” zatheka...

Pompo Tinashe anaimbira phone ija as video call ndipo phone ija inaziyakha yokha uku ikujambula...

Tinashe: yes pamenepo ziribwino utha kutulukano utatsekamo nyumbamo.

Apa amauyambano ulendo wokagona ku Lodge kuja ndipo za phone sanadauleso ka mobicel kaja ndikatundu yemwe anamusiya kunyumbako, awiriwa Jame ndi Mkazi wake anakwera Tax galimoto nakawasiya ku Lodge ko ndipo anakabuka room nakagona.
Komano Jame amakhala akulingalira zomwe amapanga kunyumbazo zomwe amamuwuza Tinashe ndipo Jame chonena analibe pazomwe amazipangazo.

AUBREY: mmmmm koma iweo Tinashe, wandiopsatu.... Mukatero mwatchera ๐Ÿ’ฃ bomba ๐Ÿ’ฃ???

Tinashe: exctaly babie.....

AUBREY: eeeeee koma iweo, khala ngati siwe mkazi???

Tinashe: mkazio ndiye amatani?

AUBREY: mmmm basi zatha....

Tinashe: mmm babie this is past 2 ndatopa tizigona...

AUBREY: mmmm babie,,, nanga ama computer aja sangatipeze?

Tinashe: akhoza kutipeza babie....

AUBREY: aaaa? Ndiye tikuyenera tipangepo kanthu kaya...

Tinashe: babie m'mawa ndatopa ine....

AUBREY: ok apapa ndakunvetsetsa... Tiye tikagoneni

Anthuwa anagona ndithu ndipo m'mene nthawi imati chama 7 o'clock ku m'mawa, kunja kunali kutacha kadzuwa Kali apo katatuluka....

Hildah, kunja kutamuchera anali ndi nkhawa koopsa pazomwe anamuwuza abwana ake kuti akamabwerera usikuo adzakhale atampeza Cathy amene amati wasowayo...
Hildah anali ndi mantha kuti mzukwao akauyambira pati kuwusaka...
Ndipo chochita chirichonse analibeso apapa...

A Minister komanso a Bwana ndi Richmond tsiku limeneli sanapiteso kuzintchito kwao koma kuma room omwe kumapangidwa control zama computer zokhazokha kuonerera ma exparts kuti apanga zotani zowayang'anira anthuwa...

Ma Expart wo atayatsa ma computer awowo ndikulumikizitsa ndi setilite anayambano kuona maiko osiyanasiyana kuphatikizapo dziko lao lomwe la South Africa ๐Ÿ‡ฟ๐Ÿ‡ฆ...
Anapanga select South Africa ๐Ÿ‡ฟ๐Ÿ‡ฆ, Durban.
Anayambano kuona aliyense mu mzinda wa Durban ndipo amakhala akuyang'ana Aubrey yo ndi Tinashe. Anayamba kuyang'ana kuyambira 7 o'clock yakum'mawa mpaka chama 6 o'clock usiku koma palibe amene anamuonapo pakati pa Aubrey ndi Tinashe, ndipo nthawi zina Jame amatha kumamuona koma chifukwa choti samamudziwa palibe chirichonse chomwe chinachitika..
Itafika 7 o'clock, ma exparts aja anawafotokozera abwana komanso a Minister kuti Aubrey ndi Tinashe sali mu Durban...
Ndipo anawauza mzeru yabwino kuti akuyenera kupita kunyumba komwe amakhalako kuti kufufudza kwina kukayambire kumeneko.

Minister: yah imeneo ndi mzeru yabwino... And munthu ameneo akuyenera kukamupana kuti aulule komwe wapita Aubrey ndi Tinashe.

Bwana: exctaly and akakana kuwulura akangomupha asafike kuno...

Pompo a Minister anatuma asirikali okwana 10 ofufudza mwachinsinsi aja kuti apite kunyumba kwa Jame yo chama 10 o'clock usiku. Awa anali asirikali ankhaza koopsa oti munthu akafuna kunchita mwano amatha kumamusenda khungu aliwamoyo. Asirikali wa kunali kuzikozekeretsa kuti lero akukapha munthu basi....
Pomwe abwana amatumiza messege kwa secrets army forces kuti ikamati 10 o'clock usiku akakhala atafika kunyumba ko.
Koma chosadziwa ndithu kuti panthawiyi Tinashe ndi Aubrey amakhala akuwaona ma messege wo, atanva zoti 10 o'clock asirikali okwana 10 akhala akufika kunyumba kwa Jame, anamuimbira phone Jame ndikumuwuza kuti ayatse phone yamkazi wakeo amulumikizitse ku video call ija yomwe anaika nyumba mwake muja aziona naye zomwe zikufuna kukachitika.
Apa nkuti Jame ali ndi mkazi wake ku Lodge kuja anabukako malo ogonera.
Atamuwuza zimenezo phone ija analumikizitsa ndithu ndipo chirichonse amatha kuona nyumba mwakemo ndi mkazi wake yemwe onse ali pa bed kupumula.
M'mene nthawi imati 10 o'clock asirikali aja anali akutulukira ku nyumba kwa Jame kuja, apa Richmond, Abwana komanso a Minister akungowonerera video m'mene asirikaliwo amapitira, Aubrey ndi Tinashe nawo ali pa laptop ๐Ÿ’ป yako kuonerera chomwe chichitike chimodzimodziso uku Jame akusakidwao ndi Mkazi wake ali maso pa phone kufuna kuona chomwe chikufuna kuchitikacho.
Next.......
๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚

Eeeee apapa game yafika posauzana ndithu...
Pama gulu atatuwa onsewa alindichidwi chofuna kuona chomwe chichitike.... Bola asapezeke wina okomokapo apa ๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚...
Nanga Hildah ndi plan yanji yomwe naye anapanga atalephera kumupeza Cathy????
Tiyeni tione mu part 19 mu kuti muli zotani!!!

Whatsapp number for group
(+265994917253)

Written by Aubrey That'sDhe Boss "```

Address

Blantyre

Telephone

0995079331

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ukaipa dziwa nyimbo posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Share on Facebook Share on Twitter Share on LinkedIn
Share on Pinterest Share on Reddit Share via Email
Share on WhatsApp Share on Instagram Share on Telegram