13/04/2026
```NDI APRIL 13 2026, KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KU MASANA, KWA TSIKU LA LERO MONDAY/LOLEMBA, TATIYENI TIWONE;```
👇🏻👇🏻
*NTHENDA YA MAUKA/MASUNGU NDI ZIZINDIKIRO ZAKE;*
Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685
✍🏻 Mauka omwe amadziwikaso kuti candidiasis (Masungu), Ndi nthenda ya yeast (yisiti) omwe amayamba makamaka m’chiwalo cha mkazi (vaginal) koma nthawi Zina matendawa amagwilaso anthu amuna. Matendawa amachitika pamene fungus wotchedwa Candida akuchulukira chulukira m,thupimo;
↪️ Nthawi zambiri Candida amakhala m’thupi mopanda vuto koma pomwe, akachuluka amayambitsa matenda monga mauka.
⏩ Si nthenda yopatsilana pogonana monga momwe timadziwila nthenda zinazi ngati chindoko, chinzonono, chikhuthula ndi nthenda zina ayi komabe mkazi akakhala nawo matendawa ndi zotheka kupatsila mamuna ndi kukhala nawoso mauka (wina mtima wake waphwa apapa mmmm😳😳
⏩ Musadzakhumudwe kwambili pomwe ma Dr apeza vutoli kawili kawili amakuwuzani Inu Abambo kapena Inu Amayi kuti Dosage imeneyi anzanuwo achikondi anuwo nawo akabweleso kuti nawo azalandile yawo treatment, Ndipo zimenezi sizimakhala zowopswa komaso zachilendo ndipo ambili mwakumana nazo zotelezi ndikusiya chikayiko m,mutu mwanu chokhudza anzanu abanja, Tikuti ayi ndithu mauka nawo Ali ndi kuthekela kokubayini Jenta nonse kuti muchile; 😱😱
*KODI MAUKA AMAYAMBA MOTANI;*
Poyambilila Tatiyeni tidziwe kuti Kundata kumakhala ma bacteria abwino bwino achilengedwe Omwe amateteza ndata kuti izikhala ndi thanzi labwino, Ma bacteria abwinowa amapha ndi kuteteza ma bacteria oyipa omwe angalowele Pazifukwa zosiyana siyana, ndikuwonetsetsa kuti Ndata ndi yotetezeka, yosamalika bwino;
↪️ Koma ngati tikudwala matenda osiyana siyana m,thupimu timamwa mankhwala ngati ma-antibiotic kwa nthawi yayitali ndi enaso, Mankhwala amenewa (amapha mabakiteriya abwino aja ku (abuja) Kundata zomwe zimasiya ndata kukhala yopanda Chitetezo zomwe zimayika ndata pa chiwopswezo kwa adani Omwe angalowe ku ndata ndi Kuyambitsa mauka;
2. *KUTSUKA KUNDATA NDI ZINTHU ZOSAYENELA;*
Kwa nthawi yaitali ndakhala ndikuphunzitsa kuti, Kundata kunapangidwa kuti kuzizitsuka ndi kudziteteza kokha mwa chilengedwe, Azimayi ambili samanvetsa nkhani imeneyi choncho amayesela kutsuka ndi soap wamitundu yosiyana siyana komaso mankhwala osiyana-siyana kaamba ka zifukwaso zosiyana siyana kwa iwowo, choncho kutsukila mankhwala kapena soap zimawononga ndi Kupha ma bacteria achilengedwe zomwe zimasiya pa chiwopswezo Cha matenda amauka mosavuta;
3. *DIABETES (KUCHULUKA KWA SHUGA M,THUPI;*
Kukhala ndi shuga wochuluka m’thupi (diabetes) kumayambitsaso vuto la mauka makamaka Kwa Amayi
4. *KUCHULUKA KWA KUSOWA UKHONDO;*
Sambani m,manja moyenela ndi soap pomwe mukugwila ku ndata kwanu, Nthawi yowopswa pankhani yoteteza ndata ku mawuka ndi ija nthawi yopanga zogonana, Amuna ambili kunja kuno amakonda zogwilana maliseche pomwe akuyamba zogonana, Mudziwonetsetsa kuti mwasamba m,manja moyenela ndi soap pomwe mukufuna zogwilana izi popewa kulowetsa Kundata tizilombo toyipa;
- Kuvala zovala zosachapa moyenela maka maka zovala za mkati ma pantie ndi ma bumshot azimayi ziliso ndi chiwopswezo chobweletsa matendawa ku ndata yanu;
4. *ZOKOMETSELA KU NDATA;*
Pali chizolowezi choika zokometsela kundata ati mamuna anzinva kukoma nthawi yogonana, Mukuyenela kukumana ndi Doctor odziwa bwino za izi chifukwa kupanda kutero mudzadzika pachiwopswezo Cha mauka osatha;
5. *KUTSIKA KWA CHITETEZO M,THUPI*
Ngati Chitetezo chatsika m,thupi zimabweletsaso chiwopswezo chodwala mauka osatha chifukwa tizilombo tachilengedwe ta m,thupi tosunga thanzi la ndata nato timafaso chifukwa Cha Kutsika kwa Chitetezo ku;
6. *KUVALA ZOVALA ZOTHINA KWAMBILI*
Mukamavala zovala zothina mumasiya ndata yopanikizika zomwe zimayika pa chiwopswezo chopha tizilombo tachilengedwe toteza ndata yanu, Choncho ndata yanu imakhala yopanda Chitetezo ku tizilombo towononga tomwe tingalowe ku ndata yanu ndi Kuyambitsa mauka;
*ZIZINDIKIRO ZOTI MULI NDI MAUKA M,THUPI MWANU;*
1. Kuyabwa kowopwsa ku ndata yanu, (Abuja)
2. Kunva kukoma mukamakanda poyambilila mukamaliza kukanda kunva kuwawa (ululu);
3. Kutentha kapena kupweteka ku ndata
- Ululuwu umakulila makamaka mukamakodza kapena nthawi yugona
4. Kutuluka zinthu zoyera ngati mkaka wosakanizika
5. Fungo ngati nsomba zowola kapena khoswe okufa
6. Kutupa kapena kufiira ku ndata;
7. Kupweteka kapena kusapeza bwino m’munsi mwa m'mimba
8. Kunva kukoma kophatikiza ndi ululu mukamagonana zomwe nthawi yoyambilila pogonana mumanva ululu;
*KUPEWA MAUKA NDI KUTHANA NAWO;*
Ukhondo Omwe mungamachite pa thupi lanu ndiyo njila yoyambilila yothananilana ndi mauka;
1. Sambani m,manja ndi soap pafupi-pafupi nthawi zonse
2. Tsukani ndata yanu ndi madzi ozizila nthawi zonse
3. Onetsetsani kuti pomwe mukupanga zodyanadyanazi ndi achikondi Anu nonse mwatsuka m,manja mwanu moyenela ndi soap
4. Osatsuka ndi soap ndata yanu
5. Osanamizidwa ndi anzanu pothila zinthu kumalokooo
6. Sinthani zovala zamkati tsiku lililonse Pomwe mwangomaliza kusamba osabweleza zovala makamaka zamkati
7. Kumagona osavala kuti ndata izipitidwa mphepo
8. Ngati muli nthawi yaitali kuchipinda imeneyi si nthawi yovala pantie ayi
9. Chepetsani zakudya zokhala ndi shuga wambiri ngati muli ndi vuto la shuga kapena pezani njila yodzichilitsila ku matenda a shuga
10. Amayi onetsetsani kuti pomwe mwamaliza kuzithandiza ku toilet pukutani zoipazo kuchokela kutsogolo kupita kumbuyo powopela kulowetsa tizilombo Kundata yanu,
11. Pali Abambo ambili Omwe Ali ndi chizolowezi cholowetsa gadafi kumbuyo kwa Amayi
Sindikufuna kulowelela nkhaniyi zimenezo ndi chisankho chanu, Koma pomwe mwasankha KUCHITA zimenezo mudziwonetsetsa kuti kwinako kumaso (ku ndata) musaloweso ngati mwasankha kumbuyo kuwopela kulowetsa tizilombo mpaka mutatsuka gadafiyo ndi soap;
⏩ Pogwilitsila ntchito mankhwala opangidwa kuchokela ku zinthu zachilengedwe limodziso ndi uphungu oyenela, Mungathe kuchilitsidwa ku matenda a mauka (Masungu);
⏩ Bwelani kwa ife kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS Lilongwe;* Kuno mudzakumana ndi *Dr Phiri;* Amene adzakuthandizani kuti muthane ndikupewa matenda amauka munjila yomwe Inu simukuyembekezela;
⏩ Bwanji tilekeze pamenepa nkhaniyi, Kuchokela kwa Ine Wanu wanu *Dr Phiri;* Kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS Lilongwe;* Nyumba ya Machilitso; Kuphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa komaso kupeleka Machilitso Pogwilitsa ntchito zinthu za *CHILENGEDWE;*
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* _100% NATURAL HERBAL_
*We Treat & Care*
+265888890685
+265999890685
+265990453883
+265997463434
*Doctor Phiri*