Chilani Herbal Clinic Plus

Chilani Herbal Clinic Plus CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS

```TATIYENI TIWONEKO MATENDA A;```👇🏻👇🏻*URINARY TRACT INFECTION (UTI)*_Matenda a mu m,nchinjila Cha mikodzo;_Dr Phiri *CH...
15/02/2026

```TATIYENI TIWONEKO MATENDA A;```
👇🏻👇🏻

*URINARY TRACT INFECTION (UTI)*
_Matenda a mu m,nchinjila Cha mikodzo;_

Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685

✍🏻 *Matenda a Urinary Tract Infection (UTI) ndi matenda Omwe amayambitsidwa ndi kachilombo (bacteria) otchedwa (Escherichia Coli) mwachidule amangoti (E. Coli); Awa ndi ma Bacteria omwe amagwira njira yonse ya mikodzo, kuyambira urethra, bladder, ureters, mpaka ma kidney, Ndipo amagwila aliyense Abambo, Amayi komaso achichepere.*

*"Well"* Ndisanayambe kutambasula nkhani yokhudza *"UTI"* *Tandilolani kuti ndifotokozele pang'ono kuti tikamati (UT), Urinary tract ndi chiyani? Choyambilira mu nkhani ino tiphunzilapo ndi kudziwa za Urinary tract, Komaso tiphunzila zokhudza Infection matenda Omwe amakhudza (Urinary tract) UT; zomwe ndi urethra, bladder, ureters, mpaka ma kidney.*

*URINARY TRACT NDI CHIYANI?*
⏩ Urinary tract ndi njira zomwe zimapanga mikodzo kuyambila m,ma Kidney, Komaso njila zomwe zikuyenda mikodzo kupita ku chikhodzodzo, Izi zikuphatikizaso chikhodzodzo chimene *( bladder )* komaso njila yomwe imatulutsa mikodzoyo *( urethra )*

⏩ UTI imayamba pamene bacteria uyu odziwika kuti *(E. Coli)* walowa mu urethra ndikukwera kulowa mu bladder mpaka kukafika ku ma kidney ndikuwononga njilazi kupanga mabala Omwe amapangitsa kunva ululu komaso Kusokoneza system yonse yokhudza kayendedwe ka mikodzo;

*ZIZINDIKIRO*
⏩ *Zizindikiro za UTI*
Munthu okhala ndi UTI angakhale; ndi zizindikilo Monga izi:
1. Kunva Kupweteka ululu pokodza;
2. Kumava kufuna kukodza pafupipafupi koma mkodzo umatuluka pang’ono;
3. Mkodzo wokhala ndi fungo loipa;
4. Mkodzo okhala ndi mtundu wachikasu kwambiri,
5. Mukamamaliza kukodza mikodzo yanu imaphatikizana ndi magazi
6. Kupweteka m'mimba pansi pa nchombo kapena kumbuyo (chiwuno)
7. Kutentha thupi (fever) makamaka ngati yafika ku ma Kidney;
8. Mkodzo okhala ndi chifunga mukamakodzamo,
9. Kupweteka, kuwotcha kuwaulo, Malo ozingulila maliseche;
10. Nseru, kufuna kunsava vutoli likakula kwambili;

*KODI KACHILOMBO KA (Escherichia coli) Kamapezeka bwanji mu thupi la munthu ndi kuyambitsa matenda a Urinary tract infection?*

⏩ Ma bacteria awa omwe nthawi zina amakhala mwachibadwa m’matumbo amayambitsa matendawa ngati kachilomboka kafika kumalo osayenera, Nthawi Zinaso izi zimachitika ngati asintha nthundu ndikukhala owopswa,

Nthawi Zinaso E. Coli amapezeka mthupi mwa munthu ngati munthuyo akukonda kudya zinthu zosasamalidwa bwino Monga;

1. Kudya kapena kumwa zinthu zosasamalidwa moyenela,
2. Madzi osasamalidwa;
3. Chakudya chosaphikidwa bwino ngati (nyama, mazira, mkaka wosaphikidwa moyenela)
4. Masamba kapena zipatso zosatsukidwa moyenela;
5. Kusasamba m,manja kapena Kusamba m,manja mosasamala Panthawi yomwe tikufuna kudya chakudya Cha m,tundu uliwonse;

⏩ Ngati munthu wabwela kuchokela kuchimbudzi ndikuyamba kugwila, kuphika zakudya asanasambe moyenela;

E. coli amakhalaso m’chimbudzi ndipo ngati munthu sasamala akhoza kutenga kachilomboka kumeneko ndi kudzagwila zakudya kapena kugwila Malo osayenela zomwe zingafalitse kachilomboka kulowa mu urethra (njira yotulukila mkodzo)
izi zimachitika kwambiri maka maka kwa akazi chifukwa urethra yawo ili pafupi kwambili;

⏩ Ngati amaliza ku toilet ndiye akudzisamala (kuchokera kumbuyo kupita kutsogolo) kungafalitseso kachilomboka

↪️ Kugonana kumbuyo kenako ndikulowa koyenela, Ma bacteria amasamutsidwa kuchokera ku a**s kupita ku urinary tract kapena m’mimba

↪️ Zipatala kapena zida zosayeretsedwa bwino monga, Catheter ya mkodzo
Zida zachipatala zosayeretsedwa bwino iziso nazo zingakwelezele kutenga kachilombo koyambitsa matendawa.

*KODI UTI NDI YOWOPSWA MOTANI?*
↪️ UTI ndi yowopswa ngati sinazindikilidwe mwansanga Ndipo thandizo silinapezeke mofulumila;

1. Imayambitsa matenda ovuta okhudza ma kidney;
2. Imachepetsa chilakolako chogonana kwa Amayi kapena Abambo
3. Umakhala pa ululu wa m,Nanu,
4. Imawononga system yopanga umuna kwa Abambo
5. Umuna nthawi yogonana umatuluka ochepa pena osatuluka kumene;

⏩ Ngati tikunva ndikuwona zina mwa zizindikilo zomwe tafotokoza mu lesson ino, chonde tisaphweketse koma kuthamangila kuchipatala kapena bwelani kuno ku *CHILANI HERBAL CLINIC PLUS;* Kuti mudzapeze Machilitso anthendayi ndi Kuthana ndi zizindikilo zonse zobwela chifukwa cha matendawa;

⏩ Pewani zonse zomwe takambilana zomwe tafotokoza kuti ndizo njila zomwe zimafalitsa matendawa poti kupewa kumaposa kuchiza;

Dinani Facebook link yomwe ili pansiyi ngati mukusangalala ndi zomwe Timaphunzitsa muno mu *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* Mukatelo dinaniso pomwe palembedwa kuti (follow) mukatero Dziwani kuti chilichonse chomwe taponya chidzakupezani ku FB yanu;
👇🏻👇🏻

https://www.facebook.com/share/1HnZ4jjAiS/

Kapenatu Dinani Whatsapp link yomwe ikupezeka pansiyi, mukadina, Dinaniso ndi kupanga join request kuti mukhale member wathu ku Whatsapp, Kumeneko Timaphunzitsa komaso kupeleka ma remedies Omwe amakuthandizani kupeza Machilitso Inu mulikunyumba;
👇🏻👇🏻

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

⏩ Kuchokela kwa Ine Wanu wanu *Dr Phiri;* kuno ku *CHILANI HERBAL CLINIC PLUS;* Nyumba ya Machilitso, Kuphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa komaso kupeleka Machilitso Pogwilitsa ntchito zinthu za *CHILENGEDWE*

*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* _100% NATURAL HERBAL_
*We Treat & Care*
*+265888890685*
*+265999890685*
*+265990453883*
*+265997463434*
*Doctor Phiri*

*KODI TIMADZIWA KUTI MADZI AMASAMBA APAPAYA MDIWOFUNIKA PA THANZI? MADZI A MASAMBA A PAPPAYA (Pawpaw Leaf)*Dr Phiri *CHI...
15/02/2026

*KODI TIMADZIWA KUTI MADZI AMASAMBA APAPAYA MDIWOFUNIKA PA THANZI? MADZI A MASAMBA A PAPPAYA (Pawpaw Leaf)*

Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685

Masamba apapaya amathandiza kuchiza matenda Monga awa;
👇🏻👇🏻

1. Chinzonono (gonorrhea) chikhuthula,

2. Chindoko (syphilis)

3. Urinary track infection (UTI) Matenda a munjila ya mkodzo,

Nthawi zambiri masamba a papaya amakandulidwa kapena kuphikidwa kenako kumwa madzi ake obiliwila a green

Matenda opatsirana pogonana Omwe amayambitsidwa ndi mabakiteriya

Mabakiteriyawa omwe amachiritsidwa ndi maantibayotiki a kuchipatala komanso madzi amasamba apapaya nawo angachilitse matendawa;

Koma ngati mukaona kuti zikulimbikila patatha 7 Days pitani kuchipatala akawone bwinobwino vuto lanu

Papaya ndi mankhwala Omwe Amachiza matenda osiyana-siyana Monga;
1. Kusabereka (infertility);
2. Kupweteka kosatha m’chiuno;
3. Kuwonongeka kwa ziwalo zam’kati;
4. Matenda kufalikira m’thupi lonse;
Tingagwilitse ntchito masamba apapaya popanga Machilitso a matendawa;

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

Lowani Whatsapp group yathu kapena dinani link yomwe ikupezeka pansiyi ndikudinaso mawu olembedwa kuti (follow) kuti nkhani zathu zidzikupezani mosavuta;

https://www.facebook.com/share/1AX9ah7DpQ/

Call Or Whatsapp
+265888890685
+265999890685

```NDI FEBRUARY 15 2026, KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KU MASANA KWA LERO SUNDA...
15/02/2026

```NDI FEBRUARY 15 2026, KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KU MASANA KWA LERO SUNDAY TATIYENI TIWONEKO ZA CHIWALO CHOFUNIKA KWAMBILI ICHI;```
👇🏻👇🏻

*CHIWINDI (LIVER) NDI CHIYANI? NANGA CHIMAGWILA NTCHITO YOFUNIKA BWANJI MTHUPI LATHU?*

Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685

✍🏻 Liver *(chiwindi);* ndi chiwalo chachikulu kwambili chomwe chili m’thupi la munthu, Chiwalochi chimapezeka kumanja kwa m'mimba (upper right abdomen), pansi pa mapapo.

*NTCHITO ZA LIVER;* *(Chiwindi);*
- Ndi Kuyeretsa kutsuka magazi,
- Chimachotsa poizoni (toxins) ndi zoipa zonse zonyansa zinyalala m'magazi.
- Kupanga bile Omwe ndi madzi othandiza kugaya mafuta.

*KUSUNGA MPHANVU ZA M,THUPI;*
1. Chimasunga shuga (glucose) ngati glycogen kuti thupi ligwiritse ntchito mtsogolo pakafunika kutero .

2. Kupanga mapuloteni ofunika monga albumin ndi zinthu zothandiza kuumitsa magazi (clotting factors).
3. Kuthandiza kusintha mankhwala chimathandiza kusintha ndi kuchotsa mankhwala m’thupi.

*TIYENI TIWONE MATENDA OMWE AMAGWILA (LIVER) CHIWINDI;*

*1. HEPATITIS A,B,C,D,E,* Awa ndi matenda mitundu 5 isanu yomwe Imayambitsa kutupa kwa chiwindi ndipo amayambika chifukwa Cha ma virus omwe amalowa ndikukhazikika mu mchiwindi;

*2. CIRRHOSIS*
Uku ndi kuwonongeka kwa chiwindi kwa nthawi yayitali.

*3. LIVER CANVER*
khansa ya chiwindi.

*4. FATTY LIVER DISEASE;* mafuta ochuluka mu liver (chiwindi). mafuta akachuluka mu mchiwindi zimayambitsa matenda okhudza chiwindi;

⏩ Ngati chiwindi chawonongeka kwambiri, munthu angakhale ndi zizindikiro monga:
1. Munthu angamalephele kuwona mokwanila (Khungu)
2. Maso kukhala achikasu (jaundice)
3. Kutopa kwambiri;
4. Kupweteka m’mimba mbali ya kumanja;
5. Kusowa chilakolako choti adye kapena kusanva njala;

Choncho apa tawona kuchuluka kwa matenda Omwe amakhudza chiwalo Chofunika kwambilichi, Ndipo kuphunzila zambili zokhudza chiwindi kungakhale kuthandiza ifeyo poti kupewa kumaposa kuchiza;

Pachifukwa ichi tikhala tikubweletsa vuto lililonse palokha lomwe tafotokoza ngati matenda Omwe amakhudza chiwindi mu masiku otsatilawa, Tikhalaso tikufotokoza zizindikiro za matendawa komaso zomwe tingachite kuti tithandizike ndi matenda Omwe angagwile chiwindi chathu;

⏩ Kuchokela kwa Ine *Dr Phiri;* Kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS Lilongwe;* Kwa lero tiyeni tilekeze pamenepa;

⏩ Ndipo ngati mukufuna kuphunzila zambili bwelani kwa Whatsapp group, Kumeneko mungatipeze potsatila link yomwe tayika m,munsiyi, Dinani ndikupanga join request kenako dikilani kuti muvomelezedwe;

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

*Call Or Whatsapp*
+265888890685
+265999890685

*KODI CHIWINDI (LIVER) NDI CHIYANI? CHIMAGWILA NTCHITO YANJI MTHUPI MWATHU, NANGA NDI MATENDA ANJI OMWE AMAGWILA CHIWALO...
15/02/2026

*KODI CHIWINDI (LIVER) NDI CHIYANI? CHIMAGWILA NTCHITO YANJI MTHUPI MWATHU, NANGA NDI MATENDA ANJI OMWE AMAGWILA CHIWALO CHOFUNIKA KWAMBILICHI?*

✍🏻 Iyi ndi lesson yomwe tikhale tikuphunzila kuyambila lero Sunday February 15 2026, Kufotokoza nkhani zonse zokhudza chiwindi *(Liver)* kuli ndi nkhani zambili chifukwa chiwindi chimagwila ntchito zambili komaso chimagwidwa ndi matenda ochuluka, Choncho lesson yathu yokhudza chiwindi tikhala tikuyibwelesa m,magawo magawo kufikila pomwe timalizile, Ndipo lesson yotsegulila group yathu Kwa tsiku lililonse kuyambila lero sunday tikhala tikubwelesa nkhani yokhudza chiwindiyi *(liver)*,

Tsano kuti ma lesson athu onse okhudza chiwindi asakuphonyeni pitani ndikudina link yathu ya Facebook ndikudina pomwe palembedwa kuti (follow), mukatelo ndiye kuti zonse zikupezani mu phone yanu;
👇🏻👇🏻

https://www.facebook.com/share/1P6bL7zEnq/

⏩ Inu Omwe muli pa group yathu ya Whatsapp khalani tcheru tsiku lililonse Chigawo Cha ku m,mawa, Nkhani yokhudza chiwindi chomwe ndi chiwalo chofunika kwambili ikhala ngati chitseko chomwe tizitsegulila group yathu Kwa tsiku lilonse mpaka pomwe timalizile kufotokoza zokhudza chiwindi (liver);

Bwelani ku Whatsapp group ngati mukufuna kupezeka ku group yathu, Kumeneko timaphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa komaso kugawa ma remedies Omwe amathandiza kudzipezela Machilitso kuchokela mu zinthu zachilengedwe, Dinani Link imeneyi pansipa ndikupanga Join request ndikudikila Adimin kuti akulowetseni;
👇🏻👇🏻

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS* Kuphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa, komaso kupeleka Machilitso Pogwilitsa ntchito zinthu za *CHILENGEDWE*

*Call Or Whatsapp*
+265888890685
+265999890685

*NGATI MUNAWUZIDWA NDI CHIPATALA KUTI MULI NDI MA FIBROIDS/ZOTUPA ZA MCHIBELEKERO KOMA MUKUNYALANYAZA SIMUKUTHANA NAZO;*...
13/02/2026

*NGATI MUNAWUZIDWA NDI CHIPATALA KUTI MULI NDI MA FIBROIDS/ZOTUPA ZA MCHIBELEKERO KOMA MUKUNYALANYAZA SIMUKUTHANA NAZO;*

✍ Ma Fibroids, omwe amadziwikanso kuti uterine fibroids, ndi zotupa za mchibelekero zomwe simakhala Cancer ayi.

⏩ Zotupazi zimayamba ndi ma sayizi ang'ono kwambili kenoko ndikumakula Ndipo ngati mwazilekelera zimakula pang'ono-pang'ono ndikumafika 5 to 7, 10 penaso 14 Centmetres zimafika, Ndipo chingakhale chimodzi ziwili or zoposa pamenepo;

⏩ Zotupazi zikayambika zimatha kuyambitsa zizindikiro zosiyanasiyana malinga ndi kukula kwake, chiwerengero chawo, ndi malo omwe zamalewo mkati mwachibelekero ngakhaleso kunja kwake Kwa chibelekerocho

*Zizindikiro za fibroids zingaphatikizepo:*

1. Period, Kutuluka magazi kwambiri kuposa momwe zimayenela kukhalila;
2. Period, Msambo umatha kupitiliza masiku 7;
3. Kumva kukhuta kapena kupanikizika m'dera la chiuno Chonse kuzungulila;
4. Kukodza pafupi-pafupi;
5. Kuvutika nthawi yokodza kapena kukodza pafupi-pafupi;
6. Kudzimbidwa;
7. Kupweteka kwa msana kapena miyendo;

8, Kutulutsa magazi ngati mukupanga period nthawi yogonana koma isali period;

9, Kunva kuwawa Kwa chiwuno ndi msana mukamagonana;

10. Kunva kuwawa, Ululu mukamagonana;
11. Chizungulile (chizumbazumba);
12. Mseru kufuna kunsaza

⏩ Zikamakula kwambili mimba Imatha kumakula mosiyana ndi momwe inalili kumbuyo;

13. Nsana kuwawa ngati mwaimilira Kwa nthawi yaitali;

14. Kukanika kutenga mimba ngati pakufunika kutelo

⏩ Kafuku-fuku amati chomwe chimayambitsa ma fibroids/Zotupazi sichimadziwika bwino bwino ayi

↪️ *koma pali zinthu zingapo zomwe zimakwelezela kwambili kuyambika Kwa zotupazi:*

↪️ Zomwe Kusiyana kwa ma Hormonal: Estrogen ndi progesterone, mahomoni opangidwa ndi o***y, amathandizira kukula kwa fibroids.

*Genetics:* Pakhoza kukhala ma genetic component, monga momwe ma fibroids amayendera m'mabanja

⏩ Zotupazi zimakula, Zinthu zomwe zimathandiza kuti thupi likhalebe ndi minofu, monga insulin-like growth factor (IGF), zingakhudze kukula kwa ma fibroid/zotupazi.

*ZODZIWIKA NDI ZAKUTI*
👇🏻👇🏻

Zotupazi zimachulukila kwambili pomwe azimayi afika kuyambila dzaka 20 zakubadwa kupita mtsogolo;

⭕ Zakuntundu, Mbiri ya banja lanu ngati kuli anthu omwe anadwala ndi ma fibroids kwanuko;

*⭕Kunenepa kwambiri*
*⭕Kuchepa kwa Vitamini*
*⭕Kumwa mowa mwauchidakwa.*

⭕ *Kulera wachizungu yemwe wachitika Kwa nthawi yaitali mthupimo*

⏩ Ngati mukukayikira kuti muli ndi ma fibroids kapena mukuwona zizindikiro, m'pofunika kukaonana ndi dokotala kuti akudziweni bwino komanso ndondomeko ya chithandizo chomwe muyenela kulandila Pothana ndi kuchiza zotupazi.

⏩ *Ndipo dziwani kuti anzathu achipatala Cha Mankhwala achizungu akazindikila Kuti muli ndi Zotupa za m,mimba/Fibroids amakupatsani Mankhwala ma Tablets olelera aja Kuti aphwetse ndi kuchiza zotupazi pokhapokha ngati apeza Kuti zotupazi zikanali zazing'ono, koma akapeza Kuti ndi zazikulu njila yomwe amatsata ndikupanga Operation Kuchotsa zotupazi*

*⏩ Kuwopswa Kwa njila ya operation yomwe anzathuwa amatsata ndi kwakuti;*
1. Samathana ndi vuto lomwe likuyambitsa zotupazi motelo kupita Kwa nthawi zimatha kuyambilaso

2. Ngati mulibe magazi okwanila nthawi ya operation zimatha kuyambitsa mavuto ena

3. Pazifukwa Zina munthu opangidwa operation yo amatha kuluza moyo

*Kumbukirani kuti, ngati mukukumana ndi zizindikiro zatsopano, zowopswa, kapena zosalekeza, m'pofunika kuti mupite kuchipatala mwamsanga akakupimeni.*

*KUWOPSWA KWA ZOTUPA ZA M,MIMBA/FIBROIDS NGATI SIZIKUCHIZIKA*
👇🏻👇🏻

⏩ Ngati ma fibroids mwawalekelera osachitapo kanthu Kuti muchile ku matendawa; mumatha kukumana ndi Mavuto osiyana-siyana, ngakhaleso zotsatira zake zimatha kusiyana-siyana malinga ndi momwe munthu alili.

*Zina mwa zizindikilo za ma fibroids osachiritsidwa ndi izi:*
👇🏻👇🏻

⏩ Kupweteka kwambiri kapena kutaya magazi kwambiri komwe kungafunike opaleshoni ya mwadzidzidzi.

↪️ Kuchepa kwa magazi m'thupi chifukwa chotaya magazi kwambiri, zomwe zimabweretsa kutopa, kutupa komanso kufooka ndi chizungulile.

↪️ Kudwala matenda a chikhodzodzo/Bladder chifukwa cha kukanikizika kwa chikhodzodzo.

↪️ Kudzimbidwa ndi mavuto ena a m'matumbo chifukwa cha kukanikizika kwa matumbo.

↪️ Kusabereka kapena zovuta zokhudza mimba/pakati, Monga kubereka mwana asanakwanile miyezi yake kapena kubala mwana okufa

↪️ Myoma kupindika, komwe kungayambitse kutsekeka kwa mitsempha yomwe ikupereka chotupacho ndikupangitsa kupweteka kwambiri

↪️ *Kugwilitsa ntchito njila za chilengedwe pochiza kuthana ndi matendawa ndi kodalilika kwambili chifukwa Mankhwala achilengedwe amakabwezeletsa chilengedwe chanu ndikuchotsa zoyambitsa zonse kusiyana ndi njila ya operation chifukwa operation amangochotsa zotupazo koma vuto loyambitsa samathana nalo zomwe zimadzamelaso kutsogolo*

⏩ *Zoyenela kudziwa ndi zakuti ngati mukukumana ndi zizindikilo zomwe tafotokoza mu nkhani yathu ino mukuyenela kuthamangila Chipatala mwansanga akawunike chifukwa Kuthana ndi zotupazi ndi ma Herbal ndi kophweka kwambili panthawi yomwe zotupazi zikanali zazing'ono kusiyana ndikudzafuna Chithandizo zotupazi zitadutsa pa mulingo wa 7.5 up to 10 Centmetres* Chifukwa ma sayizi awa amakutengelani nthawi komaso ndalama zambili Kuti m***ane muchile kuzotupazi mwinaso osachila kumene mpaka kupita ku operation zikukanika kuchizika ku mankhwala azachilengedwe;

⏩ Ife a *CHILANI HERBAL CLINIC PLUS* tili ndi Mankhwala opangidwa kuchokela Ku zitsamba omwe amachiza Kuthana ndi zotupazi mwa ukadaulo mpaka inuyo mudzasimba lokoma.

⏩ *Bwelani Kuno Inu Nonse omwe mukukumana ndi mavutowa Kuti mudzalandile Machilitso Anu, Timapezeka ku Lilongwe mu Crystal Lodge Building Room Number 16B, Ngati muli Kutali, Tangoimbani 🤳 kapena Lembani Whatsapp ku ma number omwe tayika pansiwa Ndipo mudzathandizidwa*

Dinani link yathu iyi pansipa ndikudina pomwe palembedwa kuti (follow) kuti nkhani zathu zonse zisamakuphonyeni;
👇🏻👇🏻

https://www.facebook.com/100085653754521/posts/860667660131685/?app=fbl

Komaso Dinani link yathu iyi pansipa ngati mukufuna kuti nkhani zathu zizikufikani ku Whatsapp group yathu, Dinani ndi kupanga request to join Ndipo mudzakhala mukuphunzila zambiri kudzela ku Whatsapp;
👇🏻👇🏻

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

*CHILANI HERBAL CLINIC PLUS* _100% NATURAL HERBAL_
*We Treat & Care*
*+265888890685*
*+265999890685*
*+265997463434*
*+265990453883*
*Doctor Phiri*

*SEPTILIN**K40,000* Only Per Bottle;Awa ndi mankhwala Omwe anapangidwa mwa ukadaulo kwambili chifukwa mankhwalawa amagwi...
12/02/2026

*SEPTILIN*

*K40,000* Only Per Bottle;
Awa ndi mankhwala Omwe anapangidwa mwa ukadaulo kwambili chifukwa mankhwalawa amagwila ntchito zambili akalowa mthupi mwa munthu Ndipo zomwe amachita mankhwalawa ndi zodabwitsa pozindikila kuti kugula mankhwala awa munthu umachilitsidwa ku matenda ambili osiyana siyana,

- Mankhwalawa amathandiza kwambili kukweza chitetezo cha m,thupi polimbana ndi matenda omwe amabwera kamba kakutsika kwa chitetezo Cha munthu monga:

1. Zotupa ( sinusitis)

2. Zilonda za Mphuno

3. Kutuluka Madzi mkhutu ( otorrhea)

4. Mathonsozi ( tonsillitis)

5. Mabala a mthupi ( furunculosis)

6. Fever/ thyphod

⏩ Omwe muli ndi zotupa zosadziwika bwino ndi zotuluka tuluka pa khungu panu ma allergy gulani mankhwala ake amenewa kuti m***ane nazo zimenezo;

7. Syphilis;
Mankhwalawa amachizaso matenda opatsilana pogonana Monga Chindoko;

STIs
Matenda ambili Omwe munthu amatenga ndikuvutika nawo akagonana mosadziteteza ndi munthu wina;

⏩ Ndipo ngati mthupi mwanu muli kachilombo kaja ka HIV ndiyeno mukungokhalila Kudwala mwayesetsa njila zambili koma cholowane cholowane wa matenda sakutha Kwa Inu, Basitu gulani mankhwala ake amenewa mudzachila ku matenda ambiliwo;

Omwe muli ndi HIV/ AIDS gulani kuti ikuchireni ubwino koma osati mugule ndi cholinga chochiza ai.

⏩ Septilin ndi herb yabwino kwambiri aliyense atha kumwa pofuna kukweza chitetezo Cha mthupi osati Odwala okha ai.

Omwe mukufuna product iyi bwerani ku inbox price ndi *K40,000*

Eni ake a Himalaya amafotokoza kuti full dosage ya mankhwala awa munthu ayenela kumwa kuyambila 10 up to 12 weeks zomwe zikusonyeza kuti munthu akuyenela kumwa mabotolo awili kapena atatu kuti apange full treatment

*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* Call Or Whatsapp
+265888890685
+265999890685

```NDI FEBRUARY 12 2026, KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KUMASANA KWA TSIKU LA LE...
12/02/2026

```NDI FEBRUARY 12 2026, KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KUMASANA KWA TSIKU LA LERO LACHINAYI, TATIYENI TIKAMBILANE AMAYI ZOKHUDZA;```
👇🏻👇🏻

*FUNGO LACHILENDO KUMALISECHE,*

_KODI MUNAYAMBA MWAZIFUSAPO KUTI KODI FUNGOLI LIMATANTHAUZA CHIYANI?_

Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685

✍🏻 Amayi ambiri amachita manyazi kufunsa zokhudza fungo lomwe likunveka kumaliseche kwawo, pomwe Amayi ena ambili amaganizikira kuti malowo ndi afungo ndi kale zomwe zili kuganiza mwa umbuli makamaka Kwa Omwe ma infections akumaliseche sawachoka, Komano kudziwa zenizeni zokhudza fungo la ku Maliseche kungakhale kuthandiza Kuthana ndi vutoli,

Ndata inalengedwa mochititsa chidwi imatulutsa madzi payokha Omwe amatsuka ndata Ndipo Ili ndi ma bacteria achilengedwe Omwe amathandiza kulimbana ndi ma bacteria owononga Omwe amawononga ndikubweletsa fungo loyipa, choncho chifukwa Cha kuchuluka kwa ma bacteria oyipawa amagonjetsa ndikufowoketsa ma bacteria achilengedwewa zomwe zimabweletsa mavuto afungo ku ndata amawoletsa ndata ndi kumatulutsa fungo loyipa

↪️ Choncho kudziwa mtundu wa fungo lomwe likutuluka ku ndata kungakuthandizeni kuzindikira vuto ndi mtundu wa infection yomwe yalowa m'thupi mwanu, choncho tiyeni Tiwone Zina mwa izi;

*1. BACTERIAL VAGINOSIS BV)*
Ili ndi Vuto lomwe limachitika kawilikawili, Ndipo zizindikiro za vutoli ndi fungo ngati Nsomba zowola;
Ndipo fungoli limakula kwambiri mukangomaliza kugonana kapena kapena mukamagonana;

*2. TRICHOMONIASIS*
Awa ndi Matenda opatsirana pogonana) matenda omwe amayambitsidwa ndi tizilombo tating'ono (parasites). Ndipo fungo lake limakhala fungo loyipa kwambiri komanso lamphamvu Ndipo zizindikiro za matendawa ndi!
1. Kutuluka chikazi chobiriwira green,
2. Chikasu yellow kapena mix green and yellow; komanso kuyabwa kapena kuwawa mukamakodza.

3. *YEAST INFECTION* (Candida)
Ngakhale yeast infection nthawi zambiri simanunkha kwambiri, ikakula imatha kukhala ndi fungo;

Fungo lake: Limatha kununkha ngati thobwa lowola Ndipo Zina mwa zizindikilo ndi Monga;
1. Chikazi chokhuthula ngati chambiko kapena ngati (nkaka *(curdled milk)*
2. Kuyabwa kwambiri kundata;

*4. KUYIWALA TAMPOON KAPENA COTTON*
Nthawi zina fungo loyipa kwambiri komanso lowola limatha kubwera chifukwa cha chinthu chomwe chinayiwalika m'kati (monga thonje kapena tampoon). Izi ndizowopswa chifukwa zimabweretsa tizilombo toyambitsa matenda msanga.

*ZOYENERA KUCHITA*
- Pewani "Douching": Musatsuke ndata yanu Pogwilitsa ntchito soap wantundu uliwonse;
- Tsukani ndi madzi aukhongo koma ozizila osati a mu fridge ayi koma ongotunga;
- Valani zovala za Cotton: Izi zimathandiza kuti mpweya uziyenda bwino.
- muzipewa kugwila ndata yanu ndi manja kapena zala musanasambe
- Pewani kugwilidwa ku maliseche ndi zala zosasamba;
- Pewani kupukuta ndata yanu ndi zinthu zosasamalidwa bwino;

↪️ Pitani ku Chipatala ngati mwaona fungo lachilendo kuti akawunike bwinobwino ndi kupeza vuto, musamagula mankhwala panokha othetsela fungoli pitani Kaye ku chipatala kuti akakuyeseni (test) kuti mudziwe mtundu wa infection yomwe muli nayo.

Dziwani kuti *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* Ndi Chipatala chomwe chingathane ndi fungo la ku Maliseche kwa masiku osapitilila 7 ngati vutoli lakhudza ma infection Omwe tafotokoza mu nkhani yathu ino;

↪️ Tiyeni tikumbukile *CHILANI HERBAL CLINIC PLUS;* Ngati Tili ndi vuto lililonse lokhudza ndata, Bwelani kuti muchilitsidwe;

⏩ Tiyeni tiwagayile azimayi anzathu uthengawu popanga Share ku anzathu Omwe tikuwadziwa kuti nawonso aphunzile zokhudza fungo la ku Maliseche;

⏩ Ndipo ngati mungakonde kuti Muziphunzila nkhani zathu kuchokela ku page, Dinani link yomwe tayika pansipa ndi kupitiliza kudina Malo Omwe alembedwa kuti follow, Mukatelo ndiye kuti nkhani zonse zomwe tikuphunzitsa kuno ku Facebook sizikudutsani;

https://www.facebook.com/share/1R85hBVLY6/

⏩ Ndipo ngati muli kale kuno ku Facebook ndiyeno mukufuna kuti nkhani zathu muziziphunzila kuchokela ku group la Whatsapp, Bwelani podina link yomwe ili pansiyi ndi kudina Join request mukatero dikilani Adimin kuti akupangeni proof, zikatheka ndiye kuti Muziphunzila nkhanizi kuchokela ku group la Whatsapp;
👇🏻👇🏻

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

Ine Wanu wanu *Dr Phiri* Kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* Nyumba ya a Machilitso, Kuphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa komaso kupeleka Machilitso Pogwilitsa ntchito zinthu za *CHILENGEDWE*

*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS;* _100% NATURAL HERBAL_
*We Treat & Care*
+265888890685
+265999890685
+265990453883
+265997463434
*Doctor Phiri*

```NDI FEBRUARY 11 2026 KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KUMASANA  NDABWELASO NDI ...
11/02/2026

```NDI FEBRUARY 11 2026 KUCHOKELA KUNO KU CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS, CHINO CHIGAWO CHA KUMASANA NDABWELASO NDI NKHANI YOFUNIKA KWAMBILI IYI YOFOTOKOZA ZA;```
👇🏻👇🏻

*HUMAN IMMUNAL VIRUS*
*(TIZUKUTE ZA HIV)*

Dr Phiri
*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS*
_CHIPATALA CHANU_
+265888890685
+265999890685

✍🏽 Kodi tonse muno tikudziwa kuti HIV yo payekha amayimila chiyani? Amayimira Human Immunodeficiency Virus, Pamene AIDS ndi acquired immune deficiency syndrome so mukhoza kuwona kuti gwero la lesson yi kwambiri igwera pa immunity;

⏩ Well, virus ameneyi ndiwowophya kwambiri Ndipo wasokoneza mitundu ya anthu ambili padzikoli chifukwa choti amafara nsanga malinga ndi njira yake yofalirayo komanso amakalimbana ndi chitetezo cha nthupi mapeto ake akachigonjetsa mpamene munthu amadwara chimpwirikiti cha matenda called AIDS kafukufuku amawonetsa kuti virus ameneyi adachokera ku chimpanzee late 1800s then nkulowa mwa alenje osaka nyama.

⏩ Zitatero anthu anayamba kupatsirana koma munthu oyamba kupezeka ndi virus yi adali homos*xual wachi French in Palis France mu 1983 ndipo chifukwa cha umphawi wa kuno ku Africa nthendayi inatitsalira mungoona chiwerengerochi muzotsatilazi Monga; Botswana — 19.9%
South Africa — 19.1%
Zimbabwe — 11.9%
Namibia — 11.6%
Mozambique — 11.5%
Zambia — 11.1%
Malawi — 8.1% and from 1990- 2020 about 13,000 people have died HIV and AIDS only in Malawi according to UNAIDS.

*ZOKOLEZERA ZAKE*

⏩ Ndisanafike pofotozela zomwe zimakolezera nthendayi ndimafuna ndingosiyanitsapo pakati pa HIV and AIDS although mmwambamo ndafotokoza komabe need to add some more clarification.

↪️ Well, HIV ndinanena kare kuti ndi ka chilombo komwe kamalimbana ndi asilikali a nthupi zikatero akawagonjetsa mpamene muthu amayamba kudwara matenda ambiri omwe timangoti AIDS.

↪️ Zimene zikutanthauza kuti utha kukhara ndi kachilomboka koma osadwara chimpwirikiti cha matenda ngati immune system yako ili ndi mphanvu zokwanira zomapanga control tizilombo toyambitsa AIDS tija.

↪️ So pali ma factors ambiri omwe amapanga contribute kuti munthu akhare bwenzi la mphasa Kwa munthu amene amatenga kale HIV monga kupitiliza kugonana mosadziteteza ndi munthu emwe mmagazi ake muli kachilombo kamene kamayambitsa AIDS ka.

↪️ Mchitidwe wa uhule kaya kukhara ndi abwenzi ogonana nawo ambiri zimakolezeranso kuti munthu utenge HIV yo chifukwa sudziwa kuti abwenzi wo kumbari akugonananso ndi ndani ndipo nthupi mwawo ndi motani.

↪️ Kubwerekana zipangizo zokuthwa kwambiri monga ma lezala, mipeni ndi zina zoterozo koma kwambiri ndi kubwerekana ma jakeseni kwa anthu omwe amagwiritsa ntchito ma drugs monga ma nyaope aja zomwe kwathu kuno ku malawi siza common.

↪️ Kugawana magazi (blood transfusion) mosatsata ndondomeko zoyenera zimathandizanso kuti kachilombo ka HIV ka kakhare kakufalabe pakati pa anthu chifukwa ikoko kamakhara mmagazi a munthu.

↪️ Kodi mmadziwanso kuti aja a first aid aja amakharanso pachiwophwezo chotenga HIV pamene akum***andiza munthu emwe wachita ngozi? Yes, amene aja ngati sanavare zozitetezera pa ntchito yawo amathanso kutenga ka chilomboka.

⏩ Inde ukhoza kupulumuka pangozi za galimoto ndi ngozi Zina koma ngati pangozipo panali anthu Omwe Ali ndi HIV ndiyeno kunali kugundana gundana pomwe magazi Ali fwaa fwaa Uku mwachitika mabala Iliso likhoza kukhala gwero la kutenga kachilomboka;

↪️ Palinso ntchito zina zomwe zimapanga contribute kuti munthu utenge HIV monga ntchito zomwe umakhara close ndi anthu osiyanasiyana inuyo ndi mboni kuti pali guru lina la anthu ogwira ntchito omwe ambiri a iwo ali ndi HIV komabe uthanso ku suvival osatenga.

↪️ Pa moyo wa munthu pali stage ina yomwe umafika ukamakura (adolescent stage) ambiri pa stage imeneyi amakhara akutha nsinkhu chomcho amakhara ndi zilakolako zogonana za mphanvu kwambili Ndipo kupanda kusamalitsa umatenga HIV.

↪️ Kumwa mowa mwawuchidwa zimakolezera vutori pawiri choyamba ukaledzebwa umatha kupanga zinthu zosadziwika ngati kugonana ndi hule mosadziteteza komanso mbari ina njoti;

↪️ Ukamamwa mowirikiza komanso mopyora muyezo zimakasokoneza nthupi ntchito yolimbana ndi tizilombo ta HIV tija mapeto ake chitetezo chathu chimagonja nsanga munthu nkumayaba kudwara AIDS ngati;

↪️ Unali kare ndi HIV komanso ziziwike mu lesson ino kuti HIV and AIDS ndi nthenda imodzi yomwe ili m'guru la ma STIs komabe uthanso kuyitenga without having unprotected s*x with person who's positive monganso ichitira gonorrhea ndi azinzake.

↪️ Mu introduction mo mnanenamo kuti nthendayi inawatsalira kwambiri mayiko osawuka chifukwa kafukufuku amawonetsa kuti ma hule ambiri amayamba mchitidwewu chifukwa cha umphawi makamakanso kuma rural areas that mmatawuni.

↪️ So mukhozano kuwona how dangerous HIV is right? Sitichedwa kupatsirana chifukwa aliyense amafuna kugonana makamakanso plain kuti anve bwino ena kuti apeze ndalama nde mchifukwa ili nthenda yomwe ikupha anthu ambiri pa dzikoli.

*KUTHANA NAZO KWAKE*

⏩ Tisanatambasure za mmene tingathanirane ndi nthenda yowophyayi ndimafunanso kuti tiwunikirane mfundo zingapo zomwe zingatithandize kunvetsa bwino za ka chilombo kosawutsaka.

⏩ AIDS imayamba ndi virus chomcho kuwophya kwa virus yu nkoti saferapo mchifukwa matenda ambiri omwe amayamba ndi virus satherapo ndipo amakhara kwa nthawi yayitari akusawutsabe mtundu wa anthu.

↪️ Sungatenge HIV pokisana mwa normal koma ngati mukukisana mwa deep nde ukhare kuti umatulukanso chiseyeye(namtukunya) kapena uli ndi zilonda nkamwamo m***a kupasirana kachilomboka mosavuta koma mmalovu simukhara HIV, mu thukuta mulibe HIV choncho kungogundana thupi palibe chiwophyezo chilichonse.

Mu Sperms kapena chikazi Mulibeso HIV ndipokhapokha ngati Wina chiwalo chake chasupuka winaso chasupuka pamenepo ndithu amene analibeyo wayinyamula kwa mzakeyo, Ndiye chifukwa chake ife a zachipatala timalimbikitsa Kugwilana Kaye nthawi yogonana isanafike kupangila kuti aliyense anyowe kuti mwina mkudutsa motelera ndikutulukamo bwino bwino koma winayo alinako;

↪️ Chiwophyezo chotenga AIDS through an object ngati machine ometera ndi chochepa chifukwa magazi sachedwa kuwuma koma ngati magaziwo adakalipo iwenso nkuzichekera definitely wayinyamura unknowingly so be careful.

⏩ Asamakunamizeni wa blood group o nayenso amatenga HIV koma sali pa chiwophyezo ngati omwe ali ndi ma guru ena amagazi ndipo nthawi zina kumuyeza HIV imatha osamawoneka koma ali nayo chifukwa cha mphanvu ya mtundu wa magazi akewo.

↪️ Ena akhara akufunsa kuti kodi zimatenga nthawi yayitari bwanji kuti uyambe kudwara AIDS ine ndikuyankhani kuti zimangotengera mphanvu ya chitetezo chako cha nthupi koma kutengera average azibambo ndiwomwe amayamba kuwonetsa zizindikiro than azimayi.

↪️ Koma amene amatenga nsanga HIV ndi azimayi kusiyana ndi abambo malinga ndi chilengedwe cha maliseche athu koma omwe akufa kwambiri ndi azibambo kusiyana ndi azimayi ndipo omwe akuyitenga kwambiri ndi makamaka achinyamata ndi atsikana .

↪️ Pre-exposure prophylaxis known as (PrEP) ndi 99% antiviral drug yomwe amamwa anthu omwe amakhara pachiwophwezo chotenga HIV ndipo ngati atsatiradi ndondomeko zake satenga kachilomboka koma kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS* ndikuuzaninso zachilengedwe.

↪️ Mwamuna odulidwa (circumcised) amakhara a little bit safe kutenga HIV than osadulidwa ndi 50-60% ndipo ma ARV (antiretroviral) aja amathandizira kuti tizilombo ta HIV tisachulukane nthupi mapeto ake timangodekha.

↪️ Kudekha kwa tizilombo ta HIV ko kumapangitsa kuti asilikari a nthupi azitolere mphanvu nde ukamapanga masewera olimbitsa thupi nkumadya zamaguru umawoneka wa thanzi oti aliyense sangakukayikire chifukwa chitetezo nthupi chili super ndipo;

↪️ Ma chances opatsira wina amakhara ochepa ngati mmene ndinafotokozera mu lesson ya Baby and HIV and AIDS kuti nzothekanso even or mmodzi wa inu ali ndi HIV m***a kugonana nkubara mwana koma osapatsirana even kwa mwanayo pali process yake go and read again lesson imeneyo ilipo pano pa group go and check pamwambapo ilipo.

↪️ Chizindikiro chachikuru cha nthendayi ndicho ka chifuwa kosanva mankhwara kwa mpaka 6 weeks kenako timatenda tina timazatsatira ngati sutsatira njira zoyenera mpameneno umayamba kudwara zambiri.

↪️ Nthawi zonse ndimanena kuti kupewa kumaposa kuchiza chomcho kuti titalikirane ndi nthendayi tiyeneyi tipewe makhalidwe omwe amakolezera nthendayi ndanena mmwambawo otherwise ngati inu simutenga ndekuti okondedwa wanu atenga ndikukupatsilani pomwe inu mukupewa, zofunika ndikumakambilana pa banja Lanu modekha zokhudza nthendayi.

↪️ Well, ndinati ndikuuzani ma antiviral a traditional so as of now m***a kumamwa cup imodzi ya madzi otentha mutayikamo 2teaspoon za cinnamon powder ndi 2teaspoon za uchi in every 2days pa week kuti akhare mtetezi wanu (antiviral).

↪️ Muyanike mu nthuzi masamba a moringa akawuma musinje ufa wakewo mudzika cup ya madzi otentha 2teaspoon nkumamwa mammawa before breakfast ngati antiviral wathu wachikuda komanso m***a kumamwa ginger tea or turmeric tea mwa chizolowezi.

↪️ Pali ma minerals ambiri omwe ali ndi ma antiviral monga Vitamin C and D, Zinc, Polyphenols, Potassium etc kuti mupeze zakudya zomwe muli ma minerals wa muwerenge lesson ya vitamins and minerals ndinasanjamo mwadongosolo ndipo ngati mu phone mwanumo mulibe lesson imeneyo osadandaula imeneyo idzakhala chitseko chotsekulila group ino tsiku Lina Ndipo muziyesetsa kuwona nkhani zonse za pa tsiku lililonse kuti muteteze thanzi lanu;

↪️ Ngati akupezani ndi HIV choyamba thokozani kuti anakupezani nayo ena amakhara kumamidzi oti alibenso access ya HIV test pamene ena ali nayo koma sakuyipeza akungodzifera ngati chigodora then tsatirani malangizo omwe mwapatsidwa kuphatikizapo;

↪️ Kukhara ndi okondedwa mmodzi ekha okhulupilika emwe m***a kumagonana naye otherwise kumangogonana mwachisawawa ndi ambiri umawonjezera tizilombo nthupi nde or udzimwa ma ARV sigwira so be careful.

↪️ Pali ma misconception ambiri okhudza ma herbs omwe amachizilatu HIV and AIDS ndipo ena amawononga ndalama zambiri kufuna kuti athandizike pa nthendayi chifukwa chokumana ndi anthu olakwika omwe amatsimikiza zoti iwowo ndi akadaulo pankhaniyi koma mapeto ake amakhumudwitsa;

↪️ Ndi zowona kuti pali mankhwara ochiziratu HIV and AIDS even kuchikuda koma ma report amawonetsa kuti nzaka zambuyomu mma 2000s AIDS idavuta kwambiri mmalawi mpaka nkuru wina adapanga mchape omwe anthu amapita kukamwa ndipo amakhara bwino so;

↪️ To be honest with you ineyo kufikila Pano ndapatsidwapo ma umboni ndi anthu ochuluka kuti Machilitso akutheka ndipo kuchila completely ku nthendayi zikutheka koma ngati simungafikile tsatirani ma antiviral ndakuuzaniwo komanso;

↪️ Paja pali lesson ya Immune system yomwe ndidafotokoza monveka bwino za mmene chitetezo cha nthupi chimafookera komanso mmene tingachikwezere kuti ngati tili ndi HIV tisafike podwara nayo AIDS so go and read again coz ma lesson wa amapatsirana kuwopa kutalikitsa, ngati lesson iyi mu phone mwanu mulibe ndikudzaponya imeneyi loweluka masiku awili akubwelawa kuti muthe kulumikiza bwino za nkhani yokhudza HIV and AIDS;

Ngati muli ndi chidwi chomaphunzila nkhani zathu zomwe timaponya ku Whatsapp group chonde dinani apa;
👇🏻👇🏻

https://chat.whatsapp.com/BxbKpaIx7to9lPTrIM7f7f

Ndikutsatila mawu olembedwa kuti request to join kuti mubwele ku group la Whatsapp;

Kapena dinani link ina yomwe ili m,munsiyi ndikudinaso mawu Omwe alembedwa kuti *(follow)* kuti nkhani zonse zomwe timaponya pa page yathu zisamakudutseni;
👇🏻👇🏻

https://www.facebook.com/share/16uDrcJNse/

⏩ Kwa lelo bwanji mundilole ndilekeze pano nkhaniyi, Ineyo Wanu wanu *Dr Phiri* kuno ku *CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS Lilongwe;* Nyumba ya Machilitso, Kuphunzitsa, Kulangiza, Kukumbutsa komaso Kupeleka Machilitso pogwilitsa ntchito zinthu za *CHILENGEDWE*

*CHILANI HERBAL ONLINE CLINIC PLUS* _100% NATURAL HERBAL_
*We Treat & Care*
*+265888890685*
*+265999890685*
*+265997463434*
*+265990453883*
*Doctor Phiri*

Address

P. O Box 20552 Kawale Lilongwe 2
Lilongwe

Opening Hours

Monday 08:30 - 20:00
Tuesday 08:30 - 20:00
Wednesday 08:30 - 17:00
Thursday 08:30 - 17:00
Friday 08:30 - 20:00
Saturday 08:30 - 20:00
Sunday 10:30 - 20:00

Telephone

+265999890685

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chilani Herbal Clinic Plus posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Practice

Send a message to Chilani Herbal Clinic Plus:

Share

Share on Facebook Share on Twitter Share on LinkedIn
Share on Pinterest Share on Reddit Share via Email
Share on WhatsApp Share on Instagram Share on Telegram