Machiritso Natural Remedies

Machiritso Natural Remedies MACHIRITSO NATURAL REMEDIES! Please be advised that, Whatever we share here should not/Should never replace what the hospitals/Doctors tell you.

Mukadwala kapena Mukamva mthupi Thamangilani ku Chipatala!.

🇲🇼YOUR HEALTH IS OUR PRIORITY🇲🇼.

21/05/2026

Ma ubwino a Mdulidwe

21/05/2026

🛑ULCERS/ ZINA MWA ZILONDA ZA MMIMBA🛑

Dziwani kuti Izi ndi zina mwa zilonda za mmimba ndipo masiku ano ndi zilonda izi kapena kuti vuto ili ndi vuto lomwe lafala kwambiri pakati pathu. Mmimba mumatha kukhala ndi zilonda zosiyanasiyana komano izizi za ma ulcers ndi za special chifukwa sizimatha kuchila mwazokha popanda mankhwala kapena zokudya zochiza.

ZINA MWA Zizindikiro zoti muli ndi Vutoli:

🩸-Kumva Ululu kapena kuotcha m'mimba:
Kuwawa uku kumatha kuchitika makamaka mmusi mwa mabele kumapita chakumchomboku penanso mpaka chamu nthitimu. Ndipo munthu umatha kumva kuwawa kwambiri maka nthawi yomwe uli ndi njala ndipo ukangodwa kenakake kabwino mmimba mumasiya.

🩸-Kungodya pang'ono, Kudzikuza kapena kukhuta:
Izi zimatha kuchitika penanso angakhale uli ndi njala koma mimba ili full chidzadzile.

🩸Kusagaya bwino chakudya m'Mimba:
Momwe wakhalira chakudya osagaika, no toilet, penanso kumanva kuotcha mkati mwa mimbamu.

🩸Nseru ndi kusanza (Nausea and vomiting).

🩸Kutentha kapena kuotcha kwa mtima (Heartburn/ acid reflux).

🩸Kuchepa kwa thupi popanda chifukwa komanso kusowa chilakolako chachokudya.

🚨MA WARNINGS:
Ma Ulcers amatha kufika poipisitsa ndipo amapha. Kotero zinthu zili mmusizi zikangokuchitikirani chonde thamangirani ku Chipatala:
📍Kusanza magazi kapena kusanza zinthu zooneka ngatip khofi (Vomiting blood or vomit that looks like coffee grounds).

📍Chimbudzi chakuda, chomata ngati phula (Stools that are black, sticky).
📍Chizungulire ndi kufooka kwambiri (Sudden dizziness, feeling faint).

📍Ululu waukulu wa m'mimba wosapiririka (Sudden, sharp, or severe stomach pain that does not go away).
Zimenezi ndiye zina mwa zinthu zofunika kuzidziwa ku nkhani ya ma Ulcers.

🍀Ma Remedies ake:
Ngati muli ndi vutoli gwiritsani ntchito njira izi ndipo mudzathana ndi vutoli ndipo Zotsatirazi ndizo njira zina zomwe mungagwiritse ntchito:

🍀-Madzi a Kabichi/Cabbage water/juice:
Kabichi ali ndi mavitamini ambiri monga Vitamin C, amene amathandiza polimbana ndi kachilombo ka H. pylori komanso kuchiritsa zilonda. Kumwa madzi a kabichi wa fresh tsiku lililonse kumathandiza kapena kuti kumachiritsa zilonda za mmimbazi mwachangu kwambiri.

🍀-Uchi /Honey:
Uchi uli ndi mphamvu yopha tizilombo (antibacterial) ndipo ungathandize kuchepetsa kukula kwa mabakiteriya omwe amayambitsa zilonda zam'mimba. Kotero idyani uchiwo komanso mudzithira mu tea ndi zakudya zanu zofuna sugar.

🍀-Nthochi /Bananas:
Nthochi zimathandiza kuteteza m'mimba kupanga nembanemba zomwe zimateteza ku asidi wamphamvu kapena kuthetsa acid kumene.

🍀-Adyo kapena kuti Garlic:
Adyo amathandiza kupha tizilombo tomwe timayambitsa zilonda ndipo akhoza kuthandiza kuti zilonda zisafalikire.

🍀-Aloe Vera:
Madzi a aloe vera amadziwika ndi mphamvu yake yoziziritsa komanso kuchiritsa zilonda zam'kati mwa thupi ndi zammimba, Muviikeni mudzimwa madzi akewo.

🍀-Turmeric:
Turmeric ali ndi chinthu chotchedwa curcumin chomwe chimachepetsa kutupa (inflammation) m'mimba ndikuthandiza kuteteza chikopa cha m'mimba.

💫Zakudya za ma Probiotics:
Zakudya monga yogati (yogurt) zili ndi mabakiteriya abwino omwe amathandiza kubwezeretsa dongosolo labwino la m'mimba ndikulimbana ndi tizilombo toyambitsa matenda.

💫Zinthu zoti mupewe:
Kuti zilonda zipole msanga, m'pofunika kupewa kusuta fodya, kumwa mowa, kudya zakudya zokometsera ndi ma spice kwambiri (spicy foods), komanso kumwa mankhwala opha ululu monga aspirin kapena ibuprofen mopanda dongosolo bwinobwino. Ngati momwe ndanenera muja, Ngati mukumva kupweteka kwambiri kapena mukusananza magazi, pitani ku chipatala mwachangu kuti mukalandire thandizo kuchokera kwa akatswiri odzitsata izi.

💥Kwa amzathu omwe mumawadziwa ma remedies ena a Ma Ulcers tigaileni mu Comment section mo tiphunzire nawo...zikomo.

Osaiwalakupanga LIKE...SHARE...FOLLOW.
________________________________________

Mtengo uwu ulipo kwanuko...Mtengobwa ma Lemons kapena nanunso mmadana ndi zabwino🥲🍀
20/05/2026

Mtengo uwu ulipo kwanuko...

Mtengobwa ma Lemons kapena nanunso mmadana ndi zabwino🥲🍀

20/05/2026

Nyengo zanu zidzasintha 💫

20/05/2026

🛑TIKAMBE ZA IMPSO🛑

Chiwalo chilichonse chamthupi komanso pa thupi pathu ndichofunikira kwambiri. Ndipo Kidney kapena kuti impso ndi chiwalo chimodzi mwa dziwalo zofunikira kwambiri mthupi la munthu. Aka ndi ka chiwalo komwe kali mkati mwathupi osati kunja. Angakhale zili chonchi impso imakumana ndi mavuto ambiri kumali ya matenda osiyanasiyana.

Kotero mu ndime iyi tikambeko zina mwa zizindikiro zomwe mukazinva kapena kudziona mufunikira kuthamangira ku chipatala kuti mukadziwe momwe ka chiwaloka komanso thupi lanu lilili. Chifukwa zizindikirozi zimatsonyeza kuti impso yanu ili ndi matenda kapena ili pa chiopsezo choti itha kusiya kugwira ntchito kapena kugwidwa matenda.

Apa tili ndi zina mwa zizindikiro zakuti kidney yanu ili ndi matenda. Zindikiraninso kuti zina mwa izi zimatha kukhalanso zizindikiro za matenda ena omwe inu muli nawo. Ndi chifukwa chake timakakamiza kuti mukayezetse ku chipatala kuti tidziwe vuto lanu.

ZIZINDIKIRO ZINA NDIIZI:

🍁Kupweteka kwa msana malo amodzimodzi kapena nthiti.
🍁-
🍁-Kusowa chilakolako cha chokudya.
🍁-Kupweteka kwa nthiti komanso malo olumikizana.
🍁-Kufooka kwathupi kosatha komanso kupweteka kwa mascles a mziwalo zosiyanasiyana.
🍁-Kukhala ndi mavuto ena okhudza maso.

🍁-Kukhala otopa nthawi zonse ndi opanda mphanvu

🍁-Kuyabwa kwa pathupi kapena khungu komanso kuuma kwa khungu.

🍁-Kuvutika kugona tulo osabwela.
🍁-Kutupa kwa mapazi, miyendo komanso zi sukusuku ena amati kasukusuku/ ankles.
🍁-Kukodza mkodzo wa thovu, kukodza mowirikiza komanso kukodza zophatikizana ndi magazi.

Zizindikiro zina zikuluzikulu zimatha kubwela tsopano pomwe ma Kidneys asiilatu kugwira ntchito kapena akapanikizika ndi matenda.

KAPEWEDWE KAKE:

💥-Mudzikonda kudya dzipatso zosiyanasiyana.
💥-Muchepetse kudya za sugar wambiri komanso mchere wambiri.
💥-Kumamwa madzi ambiri kuti mukhale hydrated komanso pangani masewero alionse olimbitsa thupi kuti magazi anu aziyenda bwino.
💥Pewani mowa komanso kusuta chifukwa zimapangitsa magazi osayenda bwino wa kumtima.
💥-Ngati mwadzidabwa chepetsani kudya ndiwo za nyama
💥-Mudzimwa madzi a mandimu amathandizanso.

REMEDY YAKE:
-Ma remedy awa amathandiza maka mavutowa akakhala sadakhazike komanso Kidney siidasiye kugwira ntchito.

🍀-Pezani Nyenje za chimanga ziwiritseni ndipo mudzimwa madzi ena a nyenje wo muthiremo ginger ndipo mudzithowa mmalo omwe mukunva kuwawa pa thupipo ndi madziwo.

🍀Njira ina, Funani nthangala za Maungu, dziyanikeni kenako dzipangeni ufa mudzithira mu phala kapena tea ndikumamwa.

🍀Njira ina, pezani nthangala za watermelon, dziyanikeni ndipo dzipangeni ufa. Mudzipanganso chimodzimodzi.

💥Inunso omwe mmadziwa za izi tiuzeni tiphunzire nawo the comment section is open.

_____________________________

Osaiwala kupanga SHARE, LIKE, FOLLOW kuti enanso athandizike.

Mwaikumbukira post ya dzulo yokhudza KHOLOWA...Awa ndi Ma Comments ena omwe mulinso ntchito zina za kholowa komanso ma u...
20/05/2026

Mwaikumbukira post ya dzulo yokhudza KHOLOWA...

Awa ndi Ma Comments ena omwe mulinso ntchito zina za kholowa komanso ma ubwino ake💥....Zikomo amene munalemba izi taphunzira nawo..ndakubisani maina ...kuopa zambiri

Aliponso akufuna kuonjezera😊

20/05/2026

Assalaam Alaikum💥
Good Morning lovely Family 💚
Mwadzuka bwanji lero

19/05/2026

🚨ZINA ZOKHUDZA KHOLOWA🚨

Inde tikukamba za masamba a mbatata yemwe timadya yemweyi...osati mbatatesi ayi. Ndipo kwathu kuno ndi dziko limodzi mwa maiko omwe amabvala komanso amakonda Mbatata imeneyi.
Ena mwa ma ubwino a Kholowa komanso zi ntchito zake:

🍀-Matenda:
Wiritsani masamba a kholowa ndipo mukatelo mudzimwa mmawa ndi masana cup imodzi ya madzi akewo. Izi zimathandiza kuchotsa zoipa mthupi monga ngati, chifuwa, chimfine ndi malungo ndi zina zambiri.

🍀-Chilonda:
Nyenyani masamba a kholowa ikani pa chilonda kapena pa bala or malo omwe mwabinya. Mukapaka phimbanipo muzipanga izi kawili pa tsiku Ndipo bala silichedwa kupola.

🍀-Thanzi La Mthupi:
Kugwilitsa ntchito kudya ngati masamba chabe zimathandiza nthazi la mimba, kuonjezera michere yofunikira mthupi ndi ma vitamins ndi thanzi lamagazinso kwa aliyense maka kwa mayi oyembekezera.

🍀-Kufewetsa Labour:
Kwa azimayi oyembekezera, Imwani madzi a masambawa mkapu yotentha pang'ono nthawi yomwe muli ku labour, koma mimba ngati sidan.khwime osamwa kwambiri koma mwachidule osamwa dikirani mukhale Sure kuti zili bhobho kaye ndipo mwatsala pang'ono kuchira

-Madzi a kholowa munthu wa mimba atha kumamwa koma zimathandiza koma mukamwa kwambiri zimathanso kupeleka vuto maka mimba ngati isanakule...Osamwa tsiku lililonse Ai mungayambe kuuma mimba.

📍Kwa amzathu omwe mumadziwa ntchito zina za kholowa komanso ma ubwino ake...Osamamana zomwe mudziwazo talembani mu COMMENT mmusimu tiphunzira nawo... thank you

---------------------------------
Osaiwala kupanga LIKE, SHARE, COMMENT...kuti muthandizenso anthu ena. Zikomo

Address

Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Machiritso Natural Remedies posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share