Sukamaere Youth Club - SUYOC

Sukamaere Youth Club - SUYOC Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Sukamaere Youth Club - SUYOC, Mulanje.

UNITY AND PEACE AWARENESS CAMPAIGN in photos
24/10/2023

UNITY AND PEACE AWARENESS CAMPAIGN in photos



MATERNITY WATER PIPE LINE INSTALLATIONLero SUYOC ndi ma Youth Club ena monga; Mambulu, Mbambazi ndi Duswa Girls Club ana...
03/10/2023

MATERNITY WATER PIPE LINE INSTALLATION

Lero SUYOC ndi ma Youth Club ena monga; Mambulu, Mbambazi ndi Duswa Girls Club anali pa chitapala cha Mimosa Health Center, kupitiliza kukumba ngalande yodusa ma pipe a madzi kupitisa Ku Maternity pa chipatala chi.
Ntchito yi inayambidwa ma sabata angapo apitawo, ndipo Lero kunali kumalizitsa chabe.
Wamkulu wa Mimosa youth network, Godfrey Chanza anayamikila ma Youth Club tonse mu network mmenemu chifukwa chobwera pamodzi kudzagwira ntchito yi.

MOMENTUM YOUTH COMPETITION
25/09/2023

MOMENTUM YOUTH COMPETITION

25/09/2023

MOMENTUM YOUTH COMPETITION - UPDATE

Dzulo, nthumwi ziwiri za SUYOC, zinapita Ku msonkhano omwe anachitisa ndi a Momentum Youth Challenge mothandizidwa ndi Boma la Malawi komanso USAID.

Kuitanidwaku, kunatsatira kalata yomwe tinalemba ngati club miyezi ingapo yapitayi polowa nawo mu mpikisano obweletsa njira zothesela mavuto omwe amai oyembekezera komanso ana amakumana nawo pofuna kupeza thandizo la za umoyo Ku chipatala.

A Innocent Vogah Misinde omwe ndi mmodzi mwa nthumwi zinapitazi, akhala akutitambasulila masana a Lero Mene anayendera kumeneko.

KULUMIKIZA CAMPAIGN LAUNCH - Chimwaza Primary School (21/09/2023)Dzulo, SUYOC inali nawo pa msonkhano omwe unachitikila ...
22/09/2023

KULUMIKIZA CAMPAIGN LAUNCH - Chimwaza Primary School (21/09/2023)

Dzulo, SUYOC inali nawo pa msonkhano omwe unachitikila pa sukulu pa Chimwaza komwe mwa zina analimbikitsa atsikana kubwelera Ku sukulu angakhale Ali ndi ana.
Ku mwamboku kunali zochitika zosiyanasiyana kuphatikizapo masewero ndi ndakatulo.
Amene anatsogolera SUYOC Ku mwambo wu, Man Chido Friday anatsindika za uthenga tinatenga kumeneku kuti amemeza achinyamata omwe Ali pansi pa SUYOC kulimbikitsa za kubweleranso Ku Sukulu.

Msonkhano wu anachitisa ndi akulu akulu a zamaphunziro mmadera a Mulanje ndi Thyolo, ndi thandizo lochokera Ku USAID. Panalinso nthumwi zochokera Ku Mulanje Police Station.

Zina mwa zinthuzi zomwe zinatoledwa Ku mwamboku, n**i::

19/09/2023

SUKAMAERE YOUTH CLUB CALENDAR

20 September 2023:: Kukumana pamalo athu (Chigayo) mwachizolowezi nthawi ya 3pm

21 September 2023:: TRIP kupita Kwa Chimwaza komwe taitanidwa Ku mwambo wa awareness campaign ndi Mafumu athu a Mulanje ndi Phalombe

24 September 2023:: TRIP kupita Kwa Maveya Ku YOUTH OPEN DAY

01 October 2023:: Kulandira alendo ochokera Ku MILONDE Youth Club

Yesterday in photos. Kukumba ngalande zodutsa ma pipe opita Ku Maternity Section pa Mimosa Health Center
15/09/2023

Yesterday in photos.

Kukumba ngalande zodutsa ma pipe opita Ku Maternity Section pa Mimosa Health Center

14/09/2023

KUIKA MA PIPE KU MATERNITY - Mimosa Health Center

Lero (14/09/2023) SUYOC motsogozedwa ndi azitsogoleri Ake inalawilila Ku section ya Maternity pa chipatala cha Mimosa mdera lawo kukakumba ngalande zomwe mudutse ma pipe opita Ku Maternity...

07/09/2023

MKUMANO NDI ADINDO AKU DISTRICT YOUTH OFFICE (D.Y.O)

Dzulo (06/09/2023) ma club a pansi pa MIMOSA YOUTH NETWORK, anakumana ndi nthumwi zitatu zochokela Ku office ya D.Y.O
Ena mwa ma club amene anali nawo pa mkumano wu ndi:

✓ Sukamaere Youth Club (SUYOC)
✓ Ng'omba
✓ New Vision
✓ Chisambe
✓ Bondo
✓ Nyimbiri
Ndi ena ambiri

Uthenga omwe unabwela ndi nthumwi zimenezi unali wofuna kukonzanso ma youth club athu kuti mu dongosolo labwino Ku boma.
Mwa zina tapemphadwa kuti:
> Tipangenso register ma club athu
> Tilembe constitution (Malamulo) oyendesela ma club athu
> Tipelekeso maina a ma membala a ma club athu.
Nthumwi zi, zatisiyila ma form omwe tikuyenela tilembemo mfundo zili pamwambazi kuti zizapite pa 16/09/23 kuma office a D.Y.O

Choncho tonse tikupemphedwa kuti Friday la pa 08/09/2023 lomwe ndi mawa, tonse tibwele mwa Unyinji pa chipatala nthawi ya 2:30pm kuti tizayambepo madongosolowa.

Kuchokela Ku SUYOC, tinaimiliridwa ndi a Godfrey Chanza omwenso ndi Secretary wa MIMOSA YOUTH NETWORK komanso a Innocent Vogah Misinde, membala wathu wa SUYOC.

DZIWE LA NKHALAMBA 😅😅Ulendo unafika potopesa anthu kufuna kubwelera 😂😂Enjoy the photos 🔥
04/09/2023

DZIWE LA NKHALAMBA 😅😅

Ulendo unafika potopesa anthu kufuna kubwelera 😂😂

Enjoy the photos 🔥

04/09/2023

Kukumana kwa Monday - 4 September 2023

Mu nkumano wathu wa Lero, lolemba lapa 4 September, SUYOC yakambilana izi mwa zina::

✓ Trip yaku Mission yomwe inalepheleka Friday Latha, tiipase Moto tizapite mwa unyinji!
✓ SUYOC ikumanenso Lachitatu pa 7 September 2023 kukapitiliza zokonzekera za ulendo watchulidwawo.

Mukulankhula kwawo, a vice secretary, Christina L Kaliza wapempha achinyamata tonse a SOYUC, kuti tiike Moto wambiri osafooka ndi kulephereka koyamba kwa event yomwe tikupitilayi.

Potsindira, a facilitator athu, Godfrey Chanza anatipempha kukonza ma activity ozakachita Ku meeting kumeneko.

Choncho tikupemphedwa tonse kuzabwela Lachitatu pa 7 September kuti tizamve zambiri. Malo ndi pa chigayo.


YOUTH DAY OUT!!SUYOC, Mbambazi ndi Njirambo Youth Clubs, Lero lachisanu, pa 1 September 2023, anapita Ku Dziwe la Nkhala...
01/09/2023

YOUTH DAY OUT!!

SUYOC, Mbambazi ndi Njirambo Youth Clubs, Lero lachisanu, pa 1 September 2023, anapita Ku Dziwe la Nkhalamba komwe mwa zina amakasangalala ndi kulimbikitsana ma ubale wao pakati pa achinyamata.

Mmodzi mwama organisers a trip imeneyi, Innocent Vogah Misinde anathokoza achinyamata omwe anali nawo pa trip imeneyi chifukwa chozipeleka kuti ulendo umenewu utheke.

Trip imeneyi inabwela mmalo mwa mwambo waku Mulanje Mission omwe wasunthiswa kupita Friday la week yamawa.

Address

Mulanje

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Sukamaere Youth Club - SUYOC posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Practice

Send a message to Sukamaere Youth Club - SUYOC:

Share