Ogama Vet Services

Ogama Vet Services Compassion in every care, Excellence in every Task

26/07/2024

Lowani nawo Maphunziro Athu Opanga Nkhuku Paintaneti!

Kodi mwakonzeka kusintha chidwi chanu cha nkhuku kukhala bizinesi yopindulitsa? Lowani nawo pulogalamu yathu yophunzitsa pa intaneti ndipo phunzirani zonse zomwe mungafune k*ti muyambe ndikuchita bwino pantchito yoweta nkhuku.

Zomwe Timapereka:
1.Chitsogozo cha Katswiri:
Phunzirani kuchokera kwa akatswiri omwe amaphunzitsitsa bwino za ulimiwu

2. Kuphunzira Mosinthasintha:
Pezani zida zathu zophunzitsira nthawi iliyonse, kulikonse.

3:Maphunziro Athunthu:
Kuphimba chilichonse kuyambira pakukhazikitsa mpaka k*tsatsa ndi kugulitsa.

4 Maphunziro anthu Mungodya zonse za ulimi wankhuku
A. Kamangidwe ka khola koyenera
B. Kasamalidwe ka Khola.
C. Kasamalidwe ka ziweto.(Mazira, Anapiye komaso nkhuku zofungatira)
D. Kapangidwe ka feed.
E. Matenda a nkhuku ,
F. Tizilombo ta nkhuku
G. mankhwala ndi katemera wake.

Kuwonjezera apo kuziwako njira zina zachilengedwe zothandiza Kupewa ndikuchiza matenda ena ndi ena

Chifukwa Chiyani Mutisankhe?
1.Ndalama zotsika mtengo
2.Nkhani Zotsimikizika Zopambana

Yambani Ulendo Wanu Lero!
Sinthani chidwi chanu kukhala bizinesi yopambana. Lembetsani tsopano ndik*tenga gawo loyamba lochita bizinesi yopambana yoweta nkhuku!

Lembetsani lero ndi k2000 yokha bas kudzera pa
WhatsApp/Call us on 0995157487
Calls only 0880262444
Email: gamablessings276@gmail.com

22/07/2024

Kod mukufuna kuyamba ulimi wa ziweto, kapena ndinu mulimi kale koma mukufuna upangiri wabwino k*ti mupindure nawo ulimiwu.

Musazengeleze tipezeni k*t muphunzire ndikukhala mulimi ozitsata

Mupeza maphunziro monga:

Kamangidwe ka khola koyenera.
Kasamalidwe ka Khola.
Kasamalidwe ka ziweto.
Kapangidwe ka feed.
Matenda aziweto, mankhwala ndi katemera wake komaso kapewedwe kake.

Kuwonjezera apo kuziwako njira zina zachilengedwe zothandiza Kupewa ndikuchiza matenda ena ndi ena

Ogama vet Services !
Nkhotakota
WhatsApp/Call us on 0995157487
Calls only 0880262444
Email: ogamavetservices@gmail.com

CHITOPA/CHIDERU (NEWCASTLE DZZ) Matenda omwe amagwira nkhuku za misinkhu yonse Amapha nkhuku zambiri pamasiku ochepa NJI...
18/05/2024

CHITOPA/CHIDERU (NEWCASTLE DZZ)

Matenda omwe amagwira nkhuku za misinkhu yonse
Amapha nkhuku zambiri pamasiku ochepa

NJIRA ZOMWE AMAFALIRA
o Amafala kudzera muzitosi, malobvu, mamina a nkhuku zodwala, kudzera
mmafupa ndi zotaya zochokera ku nkhuku yakufa ndi Chitopa.
o Amafalanso ndi anthu ngati sasamalira ziwiya
o Atha kufala pamene nkhuku yodwala Chitopa ikhalira limodzi ndi nkhuku
zina zosadwala

ZIZINDIKIRO ZAKE

o Nkhuku zimakhosomola ndipo zimakhala ndi thobvu kukamwa
o Kupuma mobvutika
o Nkhuku zimaphepheluka poyenda komanso zimazunguza makosi

o Kutsegula mmimba mwachikasu komanso kusakanikirana ndi kubiriwira
o Nkhuku zimabwerera pa kadyedwe mwina kusiya kumene
o Mapiko ake amalendewera ngati zabvala jekete komanso nthenga
zimanyankhalala
o Nkhuku zimafa zambiri pafupi theka mwinanso kufa zonse
o Ziweto zamtundu wa mbalame monga abakha, nkhanga, nkhunda
sikwenikweni kugwidwa ndi matendawa koma zimangofalitsa

KUPEWA KWAKE

o Kutsatira njira zonse zaukhondo mkhola., ziwiya, ndi zina zonse
o Iphani nkhuku zonse mkhola pamene matenda afika mwa mphamvu
o Poperani mkhola ndi mankhwala wopha tizilombo musanalowe nkhuku zina
o Osayendera makola a anthu ena pamene kuli Chitopa kapena ayi
o Pewani kugwiritsa ntchito ziwiya zomwe zakhudzana ndi nkhuku zakufa
o Osagula nkhuku pamene kwagwa matendawa
o Muzipereka katemera wa Chitopa pakatha miyezi itatu kapena inayi ili yonse
Chitopa chilibe mankhwala ochizira

MITUNDU YAKATEMERA

o Katemera odonthetsa mu diso (I-2)
o Katemera omwetsa (Lasota)
Nthawi zonse funsani kumene mukugula katemera njira yomwe mungatsate
poperekera katemerayu ku nkhuku

KUPELEKA KATEMERA WACHITOPA

Katemera amayenera kumusunga mu malo ozizira a 2-8
0C (fridge, koma asaume)
Ndipo anyamulidwe mu cooler box kapenanso
Mu frask ndipo muikemo ice block. Katemera amayenera kuperekedwa nthawi ya kummmawa kuli
kozizira kapena madzulo

KASUNGUNULIDWE KA LASOTA

o Tsukani magome omwera ndi madzi apa mjigo/pachitsime
o Musazipatse nkhuku zanu madzi kwa maola 1-2, k*ti zikhale ndi ludzu
o Chotsani chibvundikiro cha pa botolo la katemera
o Thirani madzi okwana theka la botolo la katemerayo ndi k*tseka kenako
takasani
o Tengani choikamo madzi chocheperapo ndi k*thiramo madzi
o Kenako thirani katemera uja mu madzi ndi k*takasa
o Kenako ikani k*temera wanu mu magome omwera madzi otsukidwa bwino
k*ti nkhuku zimwe
o Onetsetsani k*ti nkhuku zonse zamwa madzi akatemera pomatha mpindi 30

KATEMERA WA I2

Tikuyenera k*ti tisamusunge mmanja kwa nthawi yoposera mphindi 20.
Tikuyenera kumubwezeretseranso mu Fulasiki momwe muli ice msanga k*ti kuzizira
kusatheretu.
Tikuyenera kudonthetsa diso limodzi basi
Tikuyenera kudzazipatsanso nkhukuzi katemera ngati amenei pakatha miyezi inayi
Katemerayu sitikuyenera kumusunga koposera sabata tikatsegula amayamba
kununkha ndipo amatha mphanvu

Compassion in every care, Excellence in every Task
09/05/2024

Compassion in every care, Excellence in every Task

09/05/2024
08/05/2024

π˜Όπ™‘π™„π˜Όπ™‰_π™„π™‰π™π™‡π™π™€π™‰π™•π˜Ό
( )

βœ“ Also called: H5N1, H5N6, H5N8, H7N9, fowl plague.
βœ“ It is a respiratory disease of birds.
βœ“ It infects chickens, turkeys, pheasants, quail, ducks, geese, and guinea fowl etc.

#π™€π™‹π™„π˜Ώπ™€π™ˆπ™„π™Šπ™‡π™Šπ™‚π™”
βœ“ Migratory waterfowl, a natural reservoir of it.
βœ“ Type A are classified according to the severity of illness they cause.
βœ“ It can be classified into low pathogenic and highly pathogenic

#π™€π™π™„π™Šπ™‡π™Šπ™‚π™”
βœ“ Virus family: Orthomyxoviridae
βœ“Genus: influenzavirus

#π™π™π˜Όπ™‰π™Žπ™„π™ˆπ™„π™Žπ™Žπ™„π™Šπ™‰
βœ“ Direct contact with respiratory secretions and f***s.
βœ“Illegal international movement of birds
βœ“Movement of people &farm equipment
βœ“Smuggling of poultry and its products.
βœ“ Contaminated poultry equipment (such as cages and crates, manure, vehicles, and egg flats)
βœ“ Contaminated people's clothes, shoes.
βœ“Direct bird-to-bird contact


βœ“ Sudden death without clinical signs
βœ“ Lack of energy and appetite
βœ“ Decreased egg production
βœ“ Soft-shelled/misshapen eggs
βœ“ Swelling of the head, eyelids, comb, wattles, and legs
βœ“ Purple discoloration of the wattles, combs& legs
βœ“ Nasal discharge, coughing/sneezing
βœ“ Ataxia
βœ“ Diarrhea

#π˜Ώπ™„π˜Όπ™‚π™‰π™Šπ™Žπ™„π™Ž
βœ“ Symptoms
βœ“ Lesions.
βœ“ Confirmed by serologic testing for influenza virus A (AGID or ELISA)
β˜… Identify the flu virus by swabbing the nose or throat.

#π™π™π™€π˜Όπ™π™ˆπ™€π™‰π™
βœ“ Neuraminidase inhibitors (e.g, oseltamivir, zanamivir) medication shown to be effective in reducing its related deaths.

#π™‹π™π™€π™‘π™€π™‰π™π™„π™Šπ™‰
βœ“ House poultry indoors
βœ“ Avoid the use of farm ponds and bird feeders
βœ“ Avoid all contact with wild and domestic waterfowl
βœ“ Avoid live bird markets
βœ“ Control cats, rodents, insects, & other pests
βœ“ Seek diagnostic help on unusual deaths
βœ“ Avoid contact with your flock if working in poultry or swine processing.

*ogamavetservices*
*ogamavetservices@gmail.com*
πŸ₯ *+265995157487 *
πŸͺ€ *+265880262444 *

29/04/2024

Kusamalira mazira

Malo oikilira mazira akhale oti palibe chinyezi, posaomba dzuwa kwambiri komanso
tiikepo udzu ofewa bwino k*ti ipange chisa chabwino. Tisaike nkhata.
Tikuyenera kumachosapo mazira nthawi imene ikuikira, tizisiyapo dzila limodzi
poopetsa nkhuku zina zomwe zimamwa mazira
Tisunge mu thileyi yosamalidwa bwino ndipo kunsonga kwazira kukhale pansi poika
mu thireyi
Nkhuku ikuyenera kufungatira mazira osadutsa 10 k*ti igogomole bwino
Ndizofunika kulipuputa dzira ndi mankhwala opha tizilombo (sanitizer) pofuna
k*teteza ku matenda
Ngati nkhuku ikuikira pa kona la nyumba tikuyenera kusunthako chisa 30cm
kuchokera pa konapo ndi cholinga choti nkhukuyo izitha kumatakasuntha ndi
kusuntha sunthako. Izi zimathandiza k*ti k*tentha kufikire bwino ku mazira
Nkhuku ikakhalira mazira kwa masiku 7 mpaka 10, tikuyenera kuona ngati dziralo
lidzaswe mwana kapena ayi. Dzila labwino likaunikidwa ndi tochi mumaoneka
timagazi..

28/04/2024

Kusankha nkhuku zoweta

Tisankhe nkhuku:
o zolera anapiye
o zogogomola mazira bwino
o zokula mwachangu
o zoikira mazira
o zathanzi
o zanganga yaikulu bwino
Tikuyenera kusunga chiwerengero choyenera cha a tambala ndi misoti k*ti
asamalimbilane ndi kumenyana nthawi yofuna kukwera. Tambala mmodzi (1) atha
kukwera misoti khumi (10).
Tikuyeneranso kusintha sintha tambala pa khola k*ti nkhuku zathu zikhale
zosakanirana magazi.
Nkhuku imatenga masiku 21 k*ti imalize seko yoikira mazira
Nkhuku imafungatira mazira ake kwa masiku 21
Msoti ukataila ana umatenga masiku 7 mpaka 14 k*ti uyambenso kuikira mazira

28/04/2024

Ubwino wa nkhuku za lokolo

o Zimapilira ku matenda
o Mazira komanso nkhuku sizimasowa malonda
o Zosavuta kusamalira ndipo zimadya zakudya zosiyana siyana
o Zopilira ku matenda ndi nyengo zovuta
o Zimatha kuzifunira zakudya zokha
o Zimathethetsa ndi kusamala bwino anapiye
o Zimatha kubisala pa malo abwino wosaoneka ku zimphampha ndi k*thawa
zilombo zolusa komanso zimauluka

Address

Post Office Box 41 Nkhotakota
Nkhotakota

Opening Hours

Monday 09:00 - 17:00
Tuesday 09:00 - 17:00
Wednesday 09:00 - 17:00
Thursday 09:00 - 17:00
Friday 09:00 - 17:00

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ogama Vet Services posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Share on Facebook Share on Twitter Share on LinkedIn
Share on Pinterest Share on Reddit Share via Email
Share on WhatsApp Share on Instagram Share on Telegram