Gaka FM Mafana Oyaka

Gaka FM Mafana Oyaka Lachitatu lilironse 4:30 madzulo komanso Loweruka lililonse 5:00 madzulo. 96.3Mhz

12/08/2024

Mothandizidwa ndi Bungwe la Developing Radio Partners tili ndi Msonkhano wodziwitsa anthu ntchito zomwe zimathandiza umoyo wa achinyamata maka pa nkhani ya zogonana monga kupewa ndikuthandiza matenda opatsirana pogonana monga HIV/AIDS, chindiko, chinzonono, manuka, mabomu ndi ena ambiri komanso kuwadziwitsa kuti zonsezi ndizaulere ku zipatala zaboma komanso zipatala zomwe kuli nthambi yaboma ndipo tikhala live pa tsamba lino.

Inu ntchito zaulere zothandizira achinyamata pankhani zogonana ndi monga ziti?

12/08/2024

Tili Ku Kaombe Primary school 🔥🔥🔥

Tinaitanidwa ndipo tinafikako😊Gulu la Tiyanjane listeners kwa Ngabu madera ozungulira Chambuluka labadwa🔥🔥🔥
14/05/2024

Tinaitanidwa ndipo tinafikako😊
Gulu la Tiyanjane listeners kwa Ngabu madera ozungulira Chambuluka labadwa🔥🔥🔥

Lero tinali kwa Group Anne Petro komwe tinacheza zobhebha💪Koma inuyo mumatenga nawo mbali popereka maganizo pa chitukuko...
24/10/2023

Lero tinali kwa Group Anne Petro komwe tinacheza zobhebha💪
Koma inuyo mumatenga nawo mbali popereka maganizo pa chitukuko chomwe chimapangidwa kudera kwanuko? Fufuzani zambiri kwa adindo akudera kwanu

25/08/2023

Tikudziwitsa makolo omwe Ali ndi ana aulumali wosaona, kuyankhula kapena kumva ndipo anasiya sukulu kamba ka vutoli Kwa Mbenje kuti Lolemba kubwera aphunzitsi kuchokera kwa Tengani ku Mpatsa Primary school kuzaona mmene ana anu aliri ndimomwe angathandizidwire kuti athe kupita ku sukulu yothandiza ana olumala yokhalira konko. Muzafike nthawi ya 9 koloko mmawa Lolemba

Tamvetsedwa kuti kwasowa mafuta omwe amayenera kuperekedwa kwa anthu okhudzidwa ndi Namondwe pa Nkhadzi Primary School, ...
20/08/2023

Tamvetsedwa kuti kwasowa mafuta omwe amayenera kuperekedwa kwa anthu okhudzidwa ndi Namondwe pa Nkhadzi Primary School, pofuna kukonza vutoli anthu okhudzidwa ndinkhaniyi agwirizana zoti anthu omwe akuyenera kulandira thandizoli asonkhe ndalama zobwezeretsera mafutawo, titayankhula ndi anthu angapo anakambapo kutiasonkhetsedwadi ndalamayo koma auzidwa kuti ndiyopatsa olondera mafutawo, alondawo akuyenera kulandila ndalama yokwana pafupifupi K60,000 koma yosonkhedwa itakwanilitsidwa itha kufika pafupifupi K167,000. Nyumba iyi ndi ya mmodzi mwa anthu omwe akupindula nawo ndi zolandira zi ndipo ndimunthu waulumali, ngati zomwe tamva zili zoona zikutanthauza kuti nayenso ayenera kupereka ndalama yomwe ndiyokwana K300. Anthu onse oyenera kupindula ndi ntchitoyi ndi opitilira 550 ndipo thandizoli likuchokera ku World Food Program. Tikhalakhaniyi ndipo tikuuzani zoona zake.

We're back!!Kodi ndizoona kuti munthu umafunika ubereke kaye kenako uziyamba kulera?
23/07/2023

We're back!!
Kodi ndizoona kuti munthu umafunika ubereke kaye kenako uziyamba kulera?

03/05/2022

Kumeneko mumadziwa za Cancer ya khomo la chiberekero? Nanga za katemera wake mukudziwa zotani?

Tiyake guys tiyeni nazo 🔥🔥🔥🔥

23/03/2022

Imakhalatu lero🔥🔥🔥
4:30 madzulo
Lero kuli issue yotani🤔 Tsegulani 96.3 kuti omwe muli komwe Gaka sikumveka pakalipano tangoperekani ma number a WhatsApp kuti tizigawana nanu

11/03/2022

Omwe muli Madera osamveka Gaka, tipatseni WhatsApp number kuti tizikugailani ma program ndi uthenga.

21/02/2022

Ikani manambala tizikutumizirani ma Program omwe timatulutsa pa week pa WhatsApp

09/02/2022

Achinyamata akuyenera kumapeza mauthenga oyenera okhudzana ndinkhani zogonana ndi uchembere wabwino. Inu kwanuko uthenga umakupezani motani?
🔥🔥🔥

Address

Nsanje

Telephone

+265881664437

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Gaka FM Mafana Oyaka posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share