05/01/2026
KUFUNIKA KOYIKA ODWALA PA OXYGEN THERAPY
Akuluakulu m'thupi mwathu tili ndima selo(cells) amene amafuna oxygen kuti agwile ntchito yake moyenelera. Timapeza mpweyawu uzela mu mphepo yomwe timapuma tsiku ndi tsiku koma limafika nthawi Ina pamene timakanika kutenga mpweyawu moyenelera zomwe zimasokoneza kagwilidwe kantchito ka ma cells athu, apa ndipamene oxygen therapy imafunika.
KODI OXYGEN THERAPY NDICHANI?
✓Uku ndikupeleka mpweya wa oxygen Kwa odwala kapena kuti munthu amene akukanika kulowesa m'thupi mpweyawu kudzela pa tinthu monga
1. Nasal cannulas; iti nditizipangizo tomwe timayikidwa pamabowo amphuno zathu kuti zilowese mpweya mphuno wathu
2. Face mask; izi ndizija zimatchinga mphuno ndi kamwa, kuonesesa kuti mpweya ukulowa mokwanila kuchokela ku oxygen machine, dokotala/ anamwino ndamene amasankha kuti agwilise chiti kutengela katsikidwe ka oxygen m'thupi la munthu
KODI TIKATI MA CELLS NDICHANI?
✓ Ma cells ndi minyewa yomwe imagwilana ndikupanga chiwalo chilichonse mu m'thupi lathu monga; dzanja, mwendo,nkhungu, bongo, mafupa ndi zonse za m'thupi zimapangidwa ndi ma cells
✓ma cells amenewa kuti azigwila bwino ntchito amafuna oxygen kuti chiwalocho chizigwila ntchito yake moyenelera
KODI OXYGEN THERAPY NDIYOFUNIKA MOTANI?
✓ Oxygen therapy imathandiza kuonjezela mpweya wa oxygen m'thupi pamene oxygen'wo wachepamo m'thupi mwina kamba ka matenda omwe amagwila njira yopumila ngati; chibayo, asthma ndi ena komaso mavuto a mtima, kuchepa Kwa magazi, ngozi ndi zina
✓ kuonjezela mpweya kuma cells pamene wachepamo( chifukwa ngati paduse nthawi yaitali ziwalo opanda oxygen zimafa, tangoganizani ku bongo kukhale opanda oxygen Kwa mphindi zochulukilapo)
✓ oxygen therapy imachepesa ntchito yopuma, pamene tikupuma mobanika kamba kakuchepa Kwa oxygen m'thupi, ma papo komaso mtima amayenela kuti agwile ntchito kwambiri kubwezelesa oxygen. koma ndi oxygen therapy, mtima ndi ma papo zimagwila ntchito mwa mtendere munthu amapuma mosabanika
✓ kupewa zosatila zosakhala bwino monga; kuonongeka Kwa ubongo, kunika kugwila ntchito bwino Kwa mtima komaso ipso( kidneys) ngakhaleso kumwalira
KODI MA DOKOTALA AMADZIWA BWANJI KUTI MUNTHUYI MPWEYA WAKE WA OXYGEN NDIOCHEPA?
✓munthu amapuma mobanika
✓kupuma mwachanguchangu
✓khungu/ milomo/ zikadabo zimazaoneka mtundu wa blue
✓kuoneka obalalika
✓kuona chizungulire
✓ kukhala ofooka
✓ kusowa mtendere
✓ ndi Zina zambiri
ADokotala/ anamwino mayezaso kachulukidwe ka oxygen ndipo anaphunzisidwa mlingo oyenelera
NOTE;
✓ Izi zomakaniza ana anu, abale anu kapena Inu nomwe pamene mukufunikila oxygen sizabwino kwenikweni, eya ndichisankho chanu ndichifukwa wachipatala samakakamiza munthu amene akukana
✓ Pewani kunamizidwa pa nkhani ya oxygen therapy afuseni adotolo kapena anamwino pa zomwe munamva zakuyipa Kwa oxygen therapy akufotokozelani
NGATI PALI MAFUSO, MADANDO, NDEMANGA NDI ZINA TIYENI KU COMMENT BOX UKU 👇