15/02/2024
*😭ABWENZI APA DZIKO😭*
Panali pakati pa usiku pomwe mwana wanga anadwala mwa kayakaya.
Mutu wanga unaima kulingalira kuti ndiyenda naye bwanj kukafika kuchipatala popeza ndalama ndinalibe.
Ndinayesa kubwereka ndalama kwa neba wanga koma iye adati ndalama ndilibe.
Ndinayesa kuimbila phone azibale anga kuti andithandize koma onse anati tione mawa kukacha
Ndinayesa kuyimbila phone azinzanga aku ntchito ndi ena apa facebook kuti andithandize koma onsewo ankangoti ndilibe ndilibe. Komanso ena samandiyankha nkomwe, ankangondidyesa ma blue tick.
Ndinaimbira phone abwana anga ku ntchito kuti andithandize koma iwo anati mubwere mawa ku office kuti muzasayine form.
Kenako ndinaona kuti ndikuchedwa nditha kuluza moyo wa mwana. Ndinangom'beleka mwanayo nkuyamba kuthamanga naye wakuchipatala wapansi.
Koma zachisoni, ndili mu nsewu ndinadabwa kuona kuti mwana uja waumisa khosi wasiya kugwedera or kupuma.
Apa mpamene ndinadziwa kuti chinachake chachitika, komabe ndinazilimbitsa mtima mpaka ndinakafika kuchipatala kuja misozi ikusika m'masaya mwanga😭
Adotolo atangomugwira mwanayo adandiyang'ana nkupukusa mutu amvekere "pepani mwana watisiya kale uyu" oooooooh ndinalira😭😭😭
Azibale anga omwe amati alibe ndalama aja atamva uthenga wamaliro anabwera ndi galimoto kuzanyamula thupilo.
Abwana omwe amati ndipite ku office aja anabwera kuzandipasa ndalama zankhani nkhani ngati chipepeso opandaso ku sign form.
Azinzanga apa facebook omwe amandidyesa ma blue tick aja kunali kuika ma status a Rest in peace rest in peace.
Neba wanga amene amati ndalama alibe uja anandipepesa ndi ndalama zankhani nkhani.
Ndinazimvera chisoni kuona chithandizo chikubwera pa Nthawi yomwe mwana wanga saamafunikira
Abale anga okondeka dziwani izi : Abwenzi omwe tili nawowa amaonetsa chikondi pa Nthawi yomwe wasiya kupuma.Uli moyo utha kuvutika ndikuvutika opanda olo m'modzi wokuthandiza.
Koma pali m'mozi yemwe amakhala nafe Nthawi zonse ameneyo ndiye
YEHOVA bwezi losaona nyengo adzakhala nawe nt
Send a message to learn more