G.D Natural Herbs

G.D Natural Herbs Purely Natural
(1)

06/03/2025

NTHENDA YA MALUNGO‼️

↪️ Malungo akulunsotu amachizinga ngati ukumwa cup imodzi ya madzi otentha utayikamo 2teaspoon za cinnamon powder ndi 2teaspoon za uchi kawiri patsiku for 14days then come back to me for checkup.

20/02/2025

MADZI A MMAPAPO‼️

↪️ Vutoli limayamba pazifukwa zingapo monga nthenda zina zokhudzana ndi mtima, kidney failure etc ndipo umavutika kapumidwe ndi kubanika so kupeza professional therapist ali ndi technic yomwe amathanirana ndizimenezi komanso kumamwa ginger or peppermint tea zimathandiza osayiwara masewera olimbitsa thupi.

20/02/2025

Big shout out to my newest top fans! 💎 Caroline Chisalanga, Khadija Msusa, Chikondano Ntunga, Mirriam Mandaliza, Desire Loyata Laureen
,

09/02/2025

NTHENDA YA MUDZI‼️

↪️ Tenthetsani olive oil wez akazizira mudzimwa 1teaspoon patsiku for 30days kapena mudzipangako massage ndi madzi a aloe vera oyera amakhara nkati aja 3x a day after 14days muona kusintha ngati ndi hemorrhoids/pules/mudzi (likango).

14/01/2025

MAVU AKULUMANI???‼️

↪️ Well, m***a kumapakapo uchi kapena kusenda aloe vera nkumapakapo madzi ake ankati aja ngati zonsezi zasowa kagureni baking soda nde muyike timadzi pang'ono nkupanga ka paste nkumamatapo.

29/12/2024

TEA, OILS AND SPICES
(TIZUKUTE)

⏩ History ina imatiuza kuti anthu ambiri adayamba kugwiritsa ntchito ma natural remedies some 60,000 years ago in Mesopotamia yomwe pano imatchedwa (Iraq).

⏩ Komabe zimaonetsa kuti ma herbs amagwiritsidwabe ntchito pa dziko lapansi even history isadalembedwe koma chifukwa choti ku Iraq nkomwe kudari kwa chonde ndi mitsinje yambiri that's why nkukapezeka zomera zambiri makhwara achilengedwewa ngakhare mu;

⏩ Old and new testament akupezeka such as John 19:39-40 (aloe vera), Number 11:5- (garlic, cucumber, onion and watermelon), song of Solomon 4:14 (cinnamon) and God himself said Behold, I have given you every herb bearing seed, which is upon the face of all the earth- Genesis 1:29) and read Psalms 104:14, God provides us with “herbs for the service of man.” so;

⏩ You can now see and have clear picture kuti za ma herbs zi sitidangoziyamba generation yathuyi koma nzakarekare kwambiri well, mu lesson ino tikufuna tiwone zokhudza tea, oils and spices kukhudzananso ndi ka history pang'ono kuti tithe kudzinvetsa bwino zinthuzi of course pali zambiri zomwe zikuyenera kuzizukuta koma for today let us start ndi zitatuzi then little by little tikhara tikupungura zinazo right????

1️⃣ TIDZUKUTE TEA

↪️ Pa remedy lesson iliyonse ndikadzati mumwe ginger tea kapena tumeric tea whatever considered tea muzadziwe kuti dikutanthawuza;

↪️ Kuti muwiritse zinthuzo nkusefa nkumamwa madziwo wether otentha or not komanso tea wina timangowiritsa madziwo nkuyikamo;

↪️ Powder emwe tikufunayo kaya cinnamon, garlic etc malinga ndi nthenda yomwe tikudwarayo komabe enseyi ndi tea ndipo;

↪️ Systems yomabwatitsa madzi nkuyikamo masamba a fresh or owuma kapena powder monga tea idachulukira maka ku East Asian countries;

↪️ Nkumafalikira kuma continent enawa nde pang'ono chabe tingowunguza zomera zomwe ndi zabwino kuzipanga tea komanso nthenda zomwe;

↪️ Mungachile pogwiritsa ntchito tea ameneyi monga kubwatitsa ginger nkumamwa madzi akewo cup 2x a day for just a week mudzakhara ndi ka thupi ka slim;

↪️ Amathandizanso digestion komanso ngati mukunva kuphwanya nthupi is regarded as natural antibiotic (Panadol) or m***a kumapanga powder wakeyo.

↪️ Ngati mukunva kuwotcha pa mtima nkhani yake ndi ginger tea kaya nseru, chifukwa m***a kumangotafuna ngati amakuyanjani.

↪️ Nthawi yabwino kumwa ginger tea ndi mmawa 30 minutes after you awake coz amathandizanso kuti morning sickness ija ithe komabe during the day ndi zaboboh and;

↪️ Kwa azimayi oyembekezera m***anso kumwa ginger yi koma asapitilire makapu 4 patsiku fukwa atha kuyambitsanso mavuto ena pa thupipo.

↪️ Ginger yo m***a kumphatikizanso ndi tumeric ngati mukufuna kupanga boost immunity komanso it helps regulating hypertension.

↪️ Aloe Vera tea amathandiza kuchapa pachilonda kuti chipore nsanga komanso kuchiza matenda ena ammaso ngati muli zilonda.

↪️ Lemon tea amathandiza kupewa matenda a cancer, kuchiza diabetes komanso amathandiza kuti muchape nthupi through.

↪️ Kutsegura mmimba komanso ngati mumanva kuwotcha pa mtima kaya muli ndi stomach ulcers pewani lemon tea atha kukolezera ngati sanakuyanjeni.

↪️ Ngati mmavutika ndi high blood pressure m***a kumapanga tea wa garlic mixed with lemon even ginger ndi uchi zimathandiza.

↪️ Ngati mukusowa magazi mudzimwa tea wachidede or masamba a peyara shortly zopangira tea dzambiri zinazo ndizizitchura nkati mwa ma lessons.

2️⃣ TIZUKUTE ZA OIL

↪️ Mulungu akunena pa genesis paja kuti watipatsa ife zomera kuti zitibalire ife dzipatso ndinso nthangara zake kuti tichite nazo koma mwa nzeru for example.

↪️ Pali nthangara zambiri zimene timawengamo mafuta omwe ndiwothandiza kwambiri ku thanzi lathu monga mafuta;

↪️ Opangidwa kuchokera ku mtedza (kazinga) amathandiza ku matenda a mtima koma ngati tiwadya moyenera osati kungokhuthuliramo yayi tero.

↪️ Mafuta ena omwe ndi abwino kwambiri ndiwopangidwa kuchokera ku mpenda dzuwa (sunflower) it is good cholesterol level yabwino.

↪️ Ngati mukufuna kupewa stroke, kulimbitsa mafupa, kunyezimilitsa tsitsi komanso kudzora ngati mukukumana ndi matsoka nde nkhani yake ndi;

↪️ Extra virgin olive oil komanso ngati muli ndi breast cancer m***a kumapakapo or kumaphikira ndiwo zanu ndi wabwino kwambiri chabe;

↪️ Kwathu kuno siwotchuka komanso amadura chifukwa ali ndi mawubwino kholophethe m***anso or kungotenthetsa wez akazizira nkumamwa 1 teaspoon.

↪️ Mtengo wa olive udapezeka ku Asia- Syria nkomwenso adawuzindikira mawubwino ake then Turkey nkumafalikira ku Greece ndi mayiko ena mpaka kwathu kuno.

↪️ Ma teaspoon awiri ngokwana pa tsiku kumwa directly mutawatenthetsa wez nkuzizira ngati mmene ndafotokozera mwambamo lastly tiwone zokhudza ma spices zo.

3️⃣ TIZUKUTE MA SPICES

↪️ Ma spices omwe ndifotokoze apa ndi a locally found komanso not processed ngati achina Royco, Rajah etc ayi so let us zukuturise.

↪️ Cinnamon powder ali ndi antibacterial, antifungal and antimicrobial properties which is why it has been used as a health promoting spice for centuries and;

↪️ Amathandiza kuti mupewe nthenda ya diabetes komanso ndiwabwino kungoyila mu chakudyacho ngati spice m***anso kupanga tea zonse zaboboh.

↪️ Tsaboranso ndi spice ndipo ubwino wake ndi kholophethe monga kuwonjezera chitetezo nthupi komanso ndi pain killer koma ngati;

↪️ Samakuyanja sibwino kudya wambiri chifukwa amawotcha popanga chimbudzi komanso amatha kutsekulitsa mmimba so be careful.

↪️ Ngati mukufuna mafupa anu akhare olimba, kuteteza liver kumatenda komanso respiratory infection mwina m***a;

↪️ Kumdabwa kuti clove yi nde uti nkhani njoti zambirizi zidapangidwa discover ku Asia and clove yi ku Indonesia nde it's origin.

↪️ Ngati mmayiwalaiwara, ma mood ammawa aja, mpweya wa nkamwa oyipa, kaya cancer mudzigwiritsa ntchito rosemary as a spice.

↪️ Komanso rosemary yi amapangira perfume chifukwa cha fungo lake labwino so tiyeni tichite nazo and zinvekekenso kuti;

↪️ Padziko lonse la pansi dziko la India ndilomwe lili pa number one ku nkhani ya ma spices yomwe imatenga 75% most of them are healthier....🤷‍♂️🤷‍♂️🤷‍♂️

23/12/2024

FUNGO LA NTHUPI
(PUTRID)

⏩ Kupatula unve thupi limatha kumanunkha olo utasamba ndipo ena amanunkhabe or atadzifayira very expensive perfumes.

⏩ Ambiri amaona ngati munthu akamanunkha ndekuti ndi wawunve koma ena amakhara kuti it's just naturally, guess what; thukuta palokha silinunkha pokhapokha ngati mu thukutamo muli ma bacteria omwe amafuna kukasungura ma proteins.

⏩ Well, thupi likamatulutsa thukuta limatulutsira limodzi ndi mafuta anthupi through those tiny holes called poles so what happens is ma bacteria yo ndiwo amayambitsa kunukha kwa khungu makamaka ngatinso ukhondo ukuchepa nde zimaonjeza komabe pali solution.

↘️ ZINA ZOYAMBITSA

↪️ Sometimes kununkha kwa thuphupiku zimakahara zizindikiro za matenda ena eg yellow fever and typhoid fever.

↪️ Zimaonetsanso kuti ma victim ambiri a vutori amakhara okonda kudya nyama take note.

↪️ Do you even know that kusuta kumaononga ma poles aja result yake sweat imadziolera pa skin layer yoyera?

↪️ Ukamwetsa mankhara akuchipatara umayamba kununkha ka fungo ka mankhwarawo but for yourself it's hard to notify.

↪️ Ena omwe ali ndi hormone problems amatulutsanso thukuta lokhara ndi fungo chifukwa cha ma bacteria aja.

↪️ Kugwiritsa ntchito mankhwara ozunguza ubongo eg ni****ne ndi ma substance ena omwe ali harmful to our skin.

↪️ Monga ndinanena kare kuti kununkha kwa thupi sometimes si unve okha pena zimakhara kuti ndi;

↪️ Chizindikiro cha nthenda inayake for example myself i once suffered from appendix koma fungo ndinkatulutsalo zamanyanzitu.

↪️ Nthenda zina zomwe zimapangitsa thupi kununkha ndi monga kuwonongeka kwa liver ndi ma kidneys.

↪️ Palinso ma bacteria ena omwe amakonda malo otentha ngati ku nkhwapa, mphechepeche komanso kunsi kwa mabere so;

↪️ What happens is pamene kukutulutsa thukuta ma bacteria aja amabwera pofunapo ma oils wo komanso kutentherana in the process of breaking down the sweat mpamene amatulutsa fungo.

↪️ Nthawinso zina kununkhaku kumabwera chifukwa cha process yotulutsa ma toxic substances from the body ( excretion ).

↪️ Koma pomaliza tisayiware kuti ambiri omwe amatulutsa fungoli kumakhara osowa chisamaliro pa thupi lawo.

↘️ KUTHANA NAZO

↪️ Ngati simukunva bwino nthupi at the same time mukununkhanso kwambiri suspect something immediately rush to the doctor then;

↪️ Come back to me with your results then am gonna provide needful remedies.

↪️ Muzisamba madzi otenthesela limozi ndi masamba amagwafa zathandiza kuchotsa fungo.

↪️ Mudzimwa grass imozi yamadzi mammawa ulionse mutathilamo 2 teaspoon ya wheatgrass oil ngakhare kudzora.

↪️ Musakanize tea tree oil ndi madzi wez nkuika mu spray bottle nkumafaila mmalo monga mphechepechemo.

↪️ Masamba owuma a rosemary mubwatitse nkuyika beseni nkukharamo kwa kamphindi uku mukuzithira madziwo thupi lonse.

↪️ Mudzikonda kumwa tea wa lemon grass or kumasamba madzi obwatitsa ndi lemon grass yo.

↪️ Mudzisamba madzi othira masamba a sadyara ( neem ) at least kawiri patsiku for 14 days mudzapeza bwino.

↪️ Mmalo mmakonda kununkhamo mudzipakamo apple cider vinegar zimathandiza kupha ma bacteria aja.

↪️ Osayiwara kumapanga masewera olimbitsa thupi kuti ma bowo apakhunguwo atseguke mudzituluka zonyansa zosakamira pa skin yanuyo.

↪️ Mind your lifestyle otherwise healthy status yathu ikhara ndi nthenya zochuluka lekani zomwe zimakolezera vutori.

↪️ Ukhondo nde ndofunika pa nthenda iliyonse komanso kumachapa ndi kusita ngati kuli kotheka...🤷‍♂️🤷‍♂️🤷‍♂️

12/12/2024

TIONEKO ZA NTHENDA YA ASTHMA

↪️ Pezani masamba a blue gum nkuwilitsa kwa 15-20 minutes then muzike mmbeseni lotambalala bwino.

↪️ Zidakari zotentha chomcho weramilanimo mutafundira bwino kudzitchinga ndi bulangete nkumapumira mphuno kutulutsira nkamwa kapena kupumira nkamwa kutulutsira mphuno.

↪️ pangani izi kwa 5-10 minutes daily pokagona kwa 26 days uku mukumwa madzi ake half kapu owiritsira masambawo mudzachira ndipo nthendayi idzakhara mbiri komanso mudzachila kumatenda ena ambiri oti ngakhare inu simmawadziwa kuti ali nthupi mwanumo....🤷‍♂️🤷‍♂️🤷‍♂️

12/12/2024

Big shout out to my newest top fans! 💎 Caroline Chisalanga, Khadija Msusa, Chikondano Ntunga, Mirriam Mandaliza, Desire Loyata Laureen

,

11/12/2024

KODI MMADZIWA ZA BAY LEAVES ????

↪️ Ndiwachilendo ku mtundu wathu wachi Africa monga alili black seed chifukwa;

↪️ Amalimidwa mbari za ku America, Russia, Turkey, Italy, Spain, Mexico, France ndi India etc;

↪️ Koma ndiwabwino chifukwa muli vitamin A, vitamin B6 ndi vitamin C and ntchito yake yayikuru;

↪️ Nkulimbikitsa chitetezo cha nthupi kuti chisafooke komanso ngati mmimba mukupotokora;

↪️ Kamfuno ndi zina zambiri komanso muli ma minerals ngati iron, magnesium, calcium and potassium.

↪️ Which means atha kuchiza matenda ambiri kuposa mmene tikuganizira (go and re-read vitamins and minerals lesson).

↪️ Chofunika nkumawiritsa masambawo nkumamwa ngati tea kawiri patsiku mmawa;

↪️ Before breakfast ndi madzulo pokagona kwa 7days and m***a kumpeza mma shop akuluakuru monga spa, shoprite etc komanso ine ndili naye kwa inu around Pretoria town....🤷‍♂️🤷‍♂️🤷🏻‍♂️

10/12/2024

MORNING THERAPY ON DIZZINESS

↪️ Kodi mmapanga chizungulire???, Kutupa mapazi, Dzanzi, Kusowa tulo, maso osaona bwino, thupi kumangoofooka, kutupikana???.

↪️ Nthawi zambiri zizindikiro izi zimasonyeza kuti mulibe magazi.

↪️ Kuti m***ane nazo musavutike koma mudzibwatitsa chidede nkumamwa katatu patsiku daily for 30 days.

↪️ Muthanso kumawiritsa masamba a peyara nkumamwa kawiri patsiku kwa 14 days.

↪️ Mudziwiritsa beetroot nkumamwa kawiri patsiku kwa 16 days osayiwara kumamwa madzi okwanira paja mu blood composition muli madzi ambiri.

Address

Centurion

Opening Hours

Monday 09:00 - 17:00
Tuesday 09:00 - 17:00
Wednesday 09:00 - 17:00
Thursday 09:00 - 17:00
Friday 09:00 - 17:00

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when G.D Natural Herbs posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Practice

Send a message to G.D Natural Herbs:

Share