Mbali Ya Mdima

Mbali Ya Mdima Nkhani za M'madera | Entertainment | Politics | Breaking News around the world

A Silvester Ayuba James, Membala wa Chipani cha MCP  alemba kuti :Ku Tanzania inde sizinakhale bwino, koma at least mkaz...
30/10/2025

A Silvester Ayuba James, Membala wa Chipani cha MCP alemba kuti :

Ku Tanzania inde sizinakhale bwino, koma at least mkazi uja anali ndi plan B. Kupanga eliminate competition. Amadziwa kuti chisankho sichipanganika. Koma adha athu aja kumagwira makhoma ndi mapemphero anzawo akuwaponda ku ma polling center. No plan B, no emergency response plan, no political foresight. Greed basi.

Kenako kumadzalira pa TV eleventh hour, akuti anthu akundilepheretsa kuyendetsa Boma, koma mukandivoteranso ndidzawachotsa chifukwa ndikuwadziwa.

Malabishi!!!

Adha aja ndi panja penipeni. Mwati munakawakumba kutiko kodi?

30/10/2025

Earlier today, the Minister of State, Honourable Alfred Gangata , represented His Excellency President Prof. Arthur Peter Mutharika at Parliament to carry out Presidential duties in preparation for the official opening of Parliament tomorrow, which will be presided over by His Excellency President Prof. Arthur Peter Mutharika.

30/10/2025

"Leroli apopo anandipatsako kamkute amati azitayira agalu. Nkuti pepani musataye mkute nchakudya" - Gogo Maziko

30/10/2025

Border ya Kasumulu mdziko la Tanzania yasasulidwa ndi anthu amene akupanga ziwonetsero mdzikolo. Apa ndi pachipata potulukira ku Tanzania kubwera ku Songwe m’boma la Karonga.

Anthuwo ndi wokwiya chifukwa chakuti mtsogoleri wa dziko la Tanzania adamanga anthu onse omwe amayenera kupikisana nawo pa chisankho cha pulezidenti dzulo.

Malingana ndi ziwawazi galimoto zomwe zanyamula mafuta kuchoka ku Tanzania kubwera kuno ku Malawi zizifika mochedwerapo.

BREAKING NEWSBwalo la chief resident magistrate kulilongwe latulutsa pa belo anthu 9 omwe akuwaganila kuti anamenya ndiz...
30/10/2025

BREAKING NEWS

Bwalo la chief resident magistrate kulilongwe latulutsa pa belo anthu 9 omwe akuwaganila kuti anamenya ndizikwanje a Silvester Namiwa.

Oweluza milandu kubwaloli Benjamin Chulu wati mbali yaboma yalephela kuonetsa kuti oganizilidwawa akatuluka pa belo asokoneza mboni ndiumboni komanso akhoza kuthawa.

Mwazina bwaloli lati oganizilidwawa apeleke chikole chandalama zokwana K500 thousand, komanso kuti azikaonekela kulikulu lapolisi lachinayi lililonse pasabata ziwili komanso kuti apeleke ziphaso zawo zoyendela kubwalo la milandu.

Pakadali pano, mbali yaboma ndibwaloli akuunguza zikole.

Bungwe la Chisankho la National Electoral Commission ku Tanzania lalengeza kuti a Samia Suluhu Hassan apambana chisankho...
30/10/2025

Bungwe la Chisankho la National Electoral Commission ku Tanzania lalengeza kuti a Samia Suluhu Hassan apambana chisankho chomwe chachitika mdziko la Tanzania

Izi zili chonchi ngakhale Pali kusamvana pa nkhani za ndale mdzikomo





Nthambi yowona zolowa ndi zotuluka yalengeza kuti vuto lopeza ziphaso likhala likutha sabata yamawa pamene yaika makina ...
30/10/2025

Nthambi yowona zolowa ndi zotuluka yalengeza kuti vuto lopeza ziphaso likhala likutha sabata yamawa pamene yaika makina amakono omwe azitsindikiza ziphaso zopitilira 3000 patsiku.

Izi zadza pamene anthu ambili akupitilizabe kuvutika kuti apeze ziphaso pamene ena akugona panja pa Immigration munzinda wa Lilongwe.

Kampani yomwe imagwirizila kudinda ziphaso posachedwapa patsiku amatha kungopanga ziphaso zokwana 200.

Poyankhula ndi MIJ Online Pasqually Zulu mneneri wa Immigration watsimikiza kuti makina atsopano aikidwa ndipo ayamba kugwira ntchito sabata yamawa munzinda wa Lilongwe.

Zulu wanenanso kuti kuyambila sabata yamawa asiya kugwiritsa ntchito token yomwe anthu amayenela kutenga akafuna chiphaso.


-Malumbo Ngwira-

Pamene Mr Zembani (mwana wa Malemu Lucius Banda) akuyendela zimagalimoto zopuma mpamene Bambo ake akulu Paul Banda akuma...
30/10/2025

Pamene Mr Zembani (mwana wa Malemu Lucius Banda) akuyendela zimagalimoto zopuma mpamene Bambo ake akulu Paul Banda akumakwera Tax kapena minibusi uku akudwala ulendo kuchipatala.

Dziko ndi athu ake. 💔

30/10/2025

Kwavutiratu ku Tanzania mpaka Airport 🥺 kwafika zipolowe

30/10/2025

Kondwani Nankhumwa anaseweredwa ndale zowopsya ndi DPP system Mpana anakanika kuyimila pa mpando wa Speaker

Chikhala kuti mulungu amationetsera mawa sipano tikuyima pachulu nkumati "WE GOT THIS". 🙄
30/10/2025

Chikhala kuti mulungu amationetsera mawa sipano tikuyima pachulu nkumati "WE GOT THIS". 🙄

30/10/2025

Richard Chimwendo kumupanga congratulate Sameer Suleman as a Speaker.

Address

69 Cumberland Road , Bryanston
Sandton
2196

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mbali Ya Mdima posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Share on Facebook Share on Twitter Share on LinkedIn
Share on Pinterest Share on Reddit Share via Email
Share on WhatsApp Share on Instagram Share on Telegram